Mawu Amunsi
c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Onani mmene kuphunzila Baibo na munthu kungam’thandizile kupanga masinthidwe mu umoyo wake: Poyamba munthu uyu aoneka kuti moyo wake ulibe colinga, ndipo sadziŵa Yehova. Ndiyeno Mboni za Yehova zakumana naye pamene zikulalikila, ndipo wavomela kuphunzila Baibo. Zimene waphunzilazo zam’thandiza kuti adzipatulile na kubatizika. M’kupita kwanthawi, iyenso wayamba kuthandiza ena kukhala ophunzila a Yesu. Pamapeto pake, onse akukondwela na moyo m’paradaiso.