Mawu Amunsi
a Aliyense wa ife amakumana na mavuto osiyanasiyana. Pali pano, palibe njila yothetsela ambili mwa mavuto amenewa. Timangofunika kuwapilila. Koma sitili tekha. Yehova nayenso akupilila zambili. M’nkhani ino, tikambilane zinthu 9 zimene Yehova wakhala akupilila. Tikambilanenso zimene zatheka cifukwa ca kupilila kwa Yehova, komanso zimene tingaphunzilepo pa citsanzo cake ca kupilila.