Mawu Amunsi
a Kulapa kwenikweni sikungovomeleza cabe mwa kunena kuti n’nacimwa, koma kumafuna kucitapo kanthu. Nkhani ino, idzatithandiza kumvetsa kuti kulapa kwenikweni n’ciani. Tikambilane citsanzo ca Mfumu Ahabu, Mfumu Manase, komanso ca mwana woloŵelela wa m’fanizo la Yesu. Tikambilanenso zimene akulu ayenela kuona kuti adziŵe ngati m’bale kapena mlongo amene anacita chimo lalikulu ni wolapadi.