Mawu Amunsi
a Timakondwela anthu akalandila uthenga wathu, koma timakwinyilila akakana uthengawo. Bwanji ngati munthu amene mumaphunzila naye Baibo sapita patsogolo? Kapena bwanji ngati mukalibe kuthandizapo munthu mpaka kufika pobatizika? Kodi muyenela kuganiza kuti mwalephela nchito yopanga ophunzila? M’nkhani ino, tiona mmene tingakhalile opambana komanso acimwemwe mu ulaliki, kaya anthu amvetsele kapena ayi.