Mawu Amunsi
a Yehova timam’konda kwambili, ndipo timafuna kum’kondweletsa. Iye ni woyela, ndipo amafuna kuti alambili ake akhale oyela. Kodi n’zotheka anthu opanda ungwilo kukhala oyela? Inde n’zotheka. Kuganizila mofatsa malangizo amene mtumwi Petulo anapatsa Akhristu anzake, komanso malamulo amene Yehova anapatsa Aisiraeli, kudzatithandiza kuona mmene tingakhalile oyela m’makhalidwe athu onse.