Mawu Amunsi
a Pamene Yesu anakamba kuti nkhosa zake zidzamva mawu ake, anatanthauza kuti ophunzila ake adzamvela ziphunzitso zake, na kuziseŵenzetsa pa umoyo wawo. M’nkhani ino, tikambilane ziphunzitso ziŵili za Yesu zofunika kwambili, zimene ni kuleka kudela nkhawa zinthu zakuthupi, komanso kuleka kuweluza ena. Tikambilanenso mmene tingaseŵenzetsele malangizo a Yesu amenewa.