Mawu Amunsi
a Lemba la caka ca 2022 lacokela pa Salimo 34:10. Limati: “Ofuna-funa Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.” Atumiki ambili a Yehova okhulupilika alibe zinthu zambili zakuthupi. Nanga n’cifukwa ciani tikamba kuti iwo ‘sasoŵa ciliconse cabwino’? Kodi kumvetsetsa tanthauzo la vesiyi, kungatithandize bwanji kukonzekela nthawi zovuta m’tsogolomu?