Mawu Amunsi
a Yehova ni Bwenzi lathu la pamtima. Ubwenzi wathu na iye ni wamtengo wapatali, ndipo timafuna kumudziŵa bwino. Pamatenga nthawi kuti udziŵe munthu wina. Ni mmenenso zilili ngati tifuna kupitiliza kulimbitsa ubale wathu na Yehova. Popeza timatangwanika kwambili pa umoyo, kodi tingapeze bwanji nthawi yoyandikila Atate wathu wa kumwamba? Nanga tingapindule bwanji tikatelo?