Mawu Amunsi
a Nthawi zina, si copepuka kupatsa wina uphungu. Koma ngati pangafunike kutelo, kodi tingapeleke bwanji uphungu m’njila yabwino komanso yolimbikitsa? Nkhani ino, idzathandiza maka-maka akulu kuona mmene angapelekele uphungu m’njila imene ingathandize munthu kuulandila mosavuta.