Mawu Amunsi
a Tikukhala m’nthawi yapadela! Maulosi a m’buku la Chivumbulutso akukwanilitsika masiku ano. Kodi maulosi amenewo amatikhudza motani? Nkhani ino komanso ziŵili zotsatilapo, zidzafotokoza mfundo za m’buku la Chivumbulutso. Cina, zidzationetsa kuti kutsatila zonse zolembedwa m’buku la Chivumbulutso kungatithandize kuti kulambila kwathu kukhalebe kovomelezeka kwa Yehova Mulungu.