Mawu Amunsi
a Buku la Chivumbulutso limagwilitsa nchito zizindikilo povumbula adani a Mulungu. Buku la Danieli limatithandiza kudziŵa tanthauzo la zizindikilo zimenezo. M’nkhani ino, tiona mmene maulosi ena ochulidwa m’buku la Danieli, amagwilizanilana na maulosi a m’Chivumbulutso. Izi zidzatithandiza kudziŵa adani a Mulungu. Kenaka, tikambilane cimene cidzacitikila adaniwo.