Mawu Amunsi
a Solomo komanso Yesu anali anthu anzelu kwambili. Gwelo la nzelu zimenezo anali Yehova Mulungu. M’nkhani ino, tiona zimene tingaphunzile ku uphungu wouzilidwa wa Solomo komanso Yesu, pa nkhani ya mmene tiyenela kuonela ndalama, nchito ya kuthupi, komanso mmene timadzionela. Cina, tione mmene abale na alongo apindulila poseŵenzetsa mwanzelu uphungu wozikika pa Baibo pa mbali zimenezi.