Mawu Amunsi
a Makolo acikhristu amakonda kwambili ana awo. Iwo amagwila nchito mwakhama kuti asamalila ana awo kuthupi. Koma koposa zonse, makolo amenewa amayesetsa kuthandiza ana awo kukonda kwambili Yehova. M’nkhani ino, tikambilane mfundo zinayi za m’Baibo zimene zingathandize makolo pophunzitsa ana awo.