Mawu Amunsi
a Tikaganizila za munthu amene anapilila mayeso aakulu, nthawi zambili amene amabwela m’maganizo mwathu ni Yobu. Kodi tingaphunzilepo ciyani pa zimene zinacitikila munthu wokhulupilika ameneyu? Tiphunzilapo kuti Satana sangatikakamize kum’siya Yehova. Tiphunzilaponso kuti Yehova amadziŵa zonse zimene zimaticikila pa umoyo. Tsiku lina, iye adzacotsapo mavuto athu onse monga anacitila kwa Yobu. Tiyenela kuonetsa mwa zocita zathu kuti timakhulupililadi mfundo zimenezi. Mwa kutelo, timaonetsa kuti ‘tikuyembekezela Yehova.’