Mawu Amunsi
a Tikukhala m’nthawi yocititsa cidwi kwenikweni m’mbili yonse ya anthu. Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa, malinga na zimene maulosi ambili a m’Baibo anakambilatu. M’nkhani ino, tikambilane ena mwa maulosi amenewo n’colinga cakuti tizamitse cikhulupililo cathu mwa Yehova, komanso kuti atithandize kukhala osatekeseka ndi acidalilo pali pano ndiponso m’tsogolo.