Mawu Amunsi
a Anthu ambili amavutika kucipeza cimwemwe ceniceni cifukwa amacifuna-funa kolakwika. Iwo amaona kuti angacipeze m’zosangulutsa, cuma, kuchuka, kapena mwa kukhala na mphamvu. Koma pamene Yesu anali padziko lapansi, anauza anthu mmene angacipezele cimwemwe ceniceni. Ndiye cifukwa cake m’nkhani ino, tikambilane zinthu zitatu zimene zingatithandize kupeza cimwemwe ceniceni.