Mawu Amunsi
a Yehova anatipatsa ciyembekezo cabwino ngako ca zam’tsogolo. Ciyembekezo cimeneci cimatilimbikitsa, na kutithandiza kupewa kumangoganizila za mavuto athu. Cimatithandizanso kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu, kaya tikumane na mavuto otani. Cina, ciyembekezo cimeneci cimatiteteza ku zinthu zimene zingasokoneze maganizo athu. Monga tionele m’nkhani ino, zonsezi ni zifukwa zabwino zotithandiza kulimbitsabe ciyembekezo cathu cimeneci.