Mawu Amunsi
b MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Monga mmene cisoti colimba cimatetezela mutu wa msilikali, komanso mmene nangula amathandizila kuti boti isatengeke na mafunde kapena cimphepo, ciyembekezo cathu naconso cimateteza maganizo athu, na kutithandiza kukhala osasunthika tikakumana na mayeso. Mlongo akupemphela kwa Yehova mwacidalilo. M’bale akusinkhasinkha mmene Mulungu anakwanilitsila malonjezo ake kwa Abulahamu. M’bale winanso akuganizila mmene Mulungu wamudalitsila.