Mawu Amunsi
a Nthawi zina, mafuko aciisiraeli inali kumenyana okha-okha. Koma nkhondo zimenezo Yehova sanali kukondwela nazo. (1 Maf. 12:24) Ngakhale n’conco, iye anali kulola nkhondo zimenezo akaona kuti mafuko ena amupandukila, kapena akacita macimo aakulu.—Ower. 20:3-35; 2 Mbiri. 13:3-18; 25:14-22; 28:1-8.