Mawu Amunsi
a Mabuku a Uthenga Wabwino komanso mabuku ena a m’Baibo amaonetsa maulendo angapo pamene Yesu anaonekela kwa ophunzila ake pambuyo poukitsidwa. Iye anaonekela kwa: Mariya Magadala (Yoh. 20:11-18); kwa azimayi ena (Mat. 28:8-10; Luka 24:8-11); kwa ophunzila aŵili (Luka 24:13-15); kwa Petulo (Luka 24:34); komanso kwa atumwi koma Thomasi sanalipo. (Yoh. 20:19-24) Anaonekelanso kwa atumwi ndipo Thomasi analipo (Yoh. 20:26); kwa ophunzila 7 (Yoh. 21:1, 2); kwa ophunzila oposa 500 (Mat. 28:16; 1 Akor. 15:6); kwa m’bale wake Yakobo (1 Akor. 15:7); kwa atumwi onse (Mac. 1:4); komanso kwa atumwi pomwe anali pafupi na mzinda wa Betaniya. (Luka 24:50-52) N’kutheka kuti olemba Baibo sanachule maulendo onse amene Yesu anaonekela kwa ophunzila ake pambuyo poukitsidwa.—Yoh. 21:25.