Mawu Amunsi
a M’buku la 1 Petulo caputala 2 na 3, mtumwi Petulo anafotokoza zopanda cilungamo zimene zinali kucitikila Akhristu a m’zaka za zana loyamba. Akapolo anali kucitidwa zopanda cilungamo na ambuye wawo, ndipo akazi a Cikhristu anali kuvutitsidwa na amuna awo osakhulupilila.—1 Pet. 2:18-20; 3:1-6, 8, 9.