Mawu Amunsi
a Aisiraeli ambili amene anaona cozizwitsa cimene Yehova anacita pa Nyanja Yofiila sanaloŵemo m’Dziko Lolonjezedwa. (Num. 14:22, 23) Yehova anakamba kuti anthu onse a zaka 20 kupita m’tsogolo adzafela m’cipululu. (Num. 14:29) Komabe, Yoswa, Kalebe, komanso ena ambili amene anali asanakwanitse zaka 20, kuphatikizapo anthu ambili a fuko la Levi, anapulumuka. Iwo anaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yehova pamene anawoloka Mtsinje wa Yorodano n’kuloŵa m’dziko la Kanani.—Deut. 1:24-40.