Mawu Amunsi
b Kusonkhanitsa “zinthu zakumwamba” kumene Paulo anachula pa Aefeso 1:10, n’kosiyana ndi kusonkhanitsa “osankhidwa” kumene Yesu anachula pa Mateyo 24:31 ndi pa Maliko 13:27. Paulo anali kukamba za nthawi pamene Yehova amasankha amene adzalamulila ndi Yesu mwa kuwadzoza ndi mzimu woyela. Koma Yesu anali kukamba za nthawi pamene otsalila odzozedwa adzatengedwele kumwamba cisautso cacikulu cili mkati.