Mawu Amunsi
a Ngakhale munthu wokhulupilika Yobu anayamba kuganizila dzina lake, kapena kuti mbili yake, mopitilila malile anzake atatu atamuneneza kuti anacita colakwa. Poyamba, pamene iye anataikilidwa ana ake ndi katundu wake wonse, “Yobu sanacimwe kapena kuimba Mulungu mlandu woti wacita zinthu zoipa.” (Yobu 1:22; 2:10) Komabe, pamene anamuimba mlandu wakuti anacita zinazake zoipa, anayamba kulankhula “mosaganiza bwino.” Iye anaika kwambili maganizo ake pa kuteteza dzina lake m’malo moyeletsa dzina la Mulungu, kapena kuti mbili yake.—Yobu 6:3; 13:4, 5; 32:2; 34:5.