Mawu Amunsi
b Malemba a Ezekieli 37:1-14, ndi Chivumbulutso 11:7-12, amanena za zinthu zimene zinacitika mu 1919. Ulosi wa pa Ezekieli 37:1-14, umanena za anthu onse a Mulungu amene anayambanso kulambila koona mu 1919, pambuyo pa zaka zambili za ukapolo. Koma lemba la Chivumbulutso 11:7-12, limanena za kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene akhala akutsogolela anthu a Mulungu. Kwa kanthawi, abale amenewa analibe ufulu wocita zinthu zauzimu. Koma mu 1919, anayambilanso kucita zinthu zauzimu.