LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
Tulukani
Loŵani
LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
Cilengezo
Taikaponso citundu cina: Dendi
  • Lelo

Cisanu, July 18

Nʼkutipanga kukhala mafumu ndi ansembe kuti titumikile Mulungu wake ndi Atate wake.​—Chiv. 1:6.

Ophunzila a Khristu oŵelengeka anadzozedwa na mzimu woyela, ndipo amasangalala kukhala paubale wapadela na Yehova. A 144,000 amenewa azikatumikila pamodzi na Yesu kumwamba monga ansembe. (Chiv. 14:1) Malo Oyela m’cihema amaimila kudzozedwa kwawo monga ana a Mulungu pa dziko lapansi. (Aroma 8:15-17) Malo Oyela Koposa amaimila kumwamba kumene Yehova amakhala. “Nsalu yochinga” imene inalekanitsa Malo Oyela na Malo Oyela Koposa inali kuimila thupi la Yesu laumunthu limene linali kumulepheletsa kuloŵa kumwamba monga Mkulu Wansembe woposa onse wakacisi wauzimu. Pomwe Yesu anapeleka nsembe thupi lake laumunthu, anatsegulila Akhristu odzozedwa njila yopita kumwamba. Iwo ayenela kusiya matupi awo aumunthu kuti akalandile mphoto yawo kumwamba.​—Aheb. 10:19, 20; 1 Akor. 15:50. w23.10 28 ¶13

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Ciŵelu, July 19

Nthawi indicepela kuti ndipitilize kufotokoza za Gidiyoni.​—Aheb. 11:32.

Gidiyoni anayankha mofatsa pamene a Efuraimu anamuimba mlandu. (Ower. 8:1-3) Iye sanayankhe mwaukali. Anaonetsa kudzicepetsa mwa kumvetsela zokamba zawo, ndipo mwaluso anabweza mkwiyo wawo. Akulu anzelu amatengela citsanzo ca Gidiyoni mwa kumvetsela mwachelu, komanso kuyankha mofatsa ena akamawaimba mlandu. (Yak. 3:13) Mwakutelo, iwo amalimbikitsa mtendele mu mpingo. Gidiyoni atatamandidwa cifukwa cogonjetsa Amidiyani, anapeleka citamandoco kwa Yehova. (Ower. 8:22, 23) Kodi amuna apaudindo angatengele motani citsanzo ca Gidiyoni? Iwo ayenela kupeleka citamando kwa Yehova pa zimene iwowo akwanitsa kucita. (1 Akor. 4:6, 7) Mwacitsanzo, mkulu akayamikilidwa cifukwa ca luso lake la kuphunzitsa, anganene kuti malangizowo acokela m’Mawu a Mulungu, komanso kuti gulu la Yehova n’limene limatiphunzitsa tonsefe. Akulu ayenela kudziunika kuti aone ngati amaphunzitsa m’njila imene imalemekeza Yehova, kapena ngati akudzifunila ulemelelo. w23.06 4 ¶7-8

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025

Sondo, July 20

Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu.​—Yes. 55:8.

Ngati sitinalandile cinthu cimene takhala tikupemphelela, tingafunike kudzifunsa kuti, ‘Kodi nikupemphelela cinthu coyenela?’ Nthawi zambili timaona kuti tidziŵa zoyenela kwa ife. Koma nthawi zina zimene timapemphela sizingatiphindulile kwenikweni. Tikamapemphelela za vuto linalake, pangakhale njila ina yabwino yothetsela vutolo kuposa imene tikupempha. Ndipo nthawi zina zimene timapemphelela sizingakhale zogwilizana na cifunilo ca Yehova. (1 Yoh. 5:14) Mwacitsanzo, ganizilani za makolo amene anapempha Yehova kuti athandize mwana wawo kukhalabe m’coonadi. Pempho limenelo lingakhale lomveka. Koma Yehova sakakamiza aliyense kumutumikila. Iye amafuna kuti tonsefe, kuphatikizapo ana athu, tidzisankhile tokha kum’tumikila. (Deut. 10:12, 13; 30:19, 20) Conco m’malomwake, makolo angapemphe kuti Yehova awathandize kum’fika pamtima mwana wawo pom’phunzitsa kuti adzisankhile yekha kukonda Yehova na kukhala bwenzi lake.​—Miy. 22:6; Aef. 6:4. w23.11 21 ¶5; 23 ¶12

Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2025
Takulandilani
Ici ni cida cofufuzila m'mabuku olembewa na Mboni za Yehova mu vitundu volekana-lekana.
Ngati mufuna kucita daunilodi, yendani pa jw.org.
  • Cinyanja
  • Gawilani
  • Makonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenela Kutsatila
  • Mfundo Yosunga Cisinsi
  • Kusunga Cinsinsi
  • JW.ORG
  • Loŵani
Gawilani