MUTU 2
Kuvomeleza Udindo wa Khristu m’Makonzedwe a Mulungu
“PA CIYAMBI, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Ndipo zonse zimene analenga zinali “zabwino kwambili.” (Gen. 1:1, 31) Yehova analenga anthu na kuwapatsa tsogolo labwino kwambili. Koma cipanduko ca mu Edeni cinasokoneza cimwemwe ca anthu, koma osati kwacikhalile. Ngakhale n’telo, colinga ca Yehova pa dziko lapansi na munthu sicinasinthe. Mulungu anaonetsa kuti ana omvela a Adamu adzapulumutsidwa, kulambila koona kudzabwezeletsedwa, ndipo oipa adzawonongedwa pamodzi na nchito zawo. (Gen. 3:15) Panthawi imeneyo, zinthu zidzakhalanso “zabwino kwambili.” Yehova adzacita zimenezi kupitilila mwa Mwana wake, Yesu Khristu. (1 Yoh. 3:8) Ndiye cifukwa cake tiyenela kumvetsa na kuvomeleza udindo wa Khristu m’makonzedwe a Mulungu.—Mac. 4:12; Afil. 2:9, 11.
KODI KHRISTU ALI NA UDINDO WOTANI?
2 Udindo wa Khristu m’makonzedwe a Mulungu uli na mbali zambili. Yesu ni Mpulumutsi wa anthu, ni Mkulu wa Ansembe, ni Mutu wa mpingo wacikhristu, ndipo lomba ni Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Kuganizila pa maudindo amenewa, kumatithandiza kumvetsa bwino makonzedwe a Mulungu, na kuzamitsa cikondi cathu pa Khristu Yesu. Baibo imafotokoza bwino mbali zolekana-lekana za udindo wa Yesu.
Yesu ndiye mzati wokwanilitsila colinga ca Yehova pa anthu
3 Pamene Khristu anali padziko lapansi, zinaonekela bwino kuti anthu omvela adzayanjanitsidwa kwa Mulungu kupitila mwa Yesu. (Yoh. 14:6) Monga Muwomboli wa anthu, Yesu anadzipeleka kukhala dipo lowombolela anthu ambili. (Mat. 20:28) Conco, Yesu sali cabe citsanzo ca makhalidwe a umulungu. Iye ndiye mzati wokwanilitsila colinga ca Yehova pa anthu. Ndipo iye yekha ndiye angatiyanjanitsenso kwa Mulungu. (Mac. 5:31; 2 Akor. 5:18, 19) Imfa ya Yesu yodzipeleka nsembe komanso kuukitsidwa kwake, kunatsegula njila yakuti anthu omvela akalandile madalitso osatha pansi pa Ufumu wakumwamba wa Mulungu.
4 Pokhala Mkulu wa Ansembe, Yesu ‘amatimvela cisoni pa zofooka zathu,’ ndipo anapeleka nsembe yophimba macimo a otsatila ake padziko lapansi. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti: “Mkulu wa ansembe amene tili naye si mkulu wa ansembe amene sangatimvele cisoni pa zofooka zathu. Koma tili ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa m’zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda ucimo.” Ndiyeno, Paulo analimbikitsa aja okhulupilila mwa Yesu Khristu kuti atengele mwayi makonzedwe amenewa oyanjanitsidwanso kwa Mulungu. Iye anati: “Conco, tiyeni tiyandikile mpando wacifumu wa kukoma mtima kwakukulu [kapena kuti cisomo], ndipo tipemphele kwa Mulungu ndi ufulu wa kulankhula, kuti aticitile cifundo ndi kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu [cisomo] pa nthawi imene tikufunika thandizo.”—Aheb. 4:14-16; 1 Yoh. 2:2.
5 Yesu alinso Mutu wa mpingo wacikhristu. Monga zinalili kwa otsatila ake m’zaka za zana loyamba, ifenso masiku ano sitifunikila mtsogoleli waumunthu. Yesu amatsogolela mpingo poseŵenzetsa mzimu woyela komanso abusa aang’ono oyenelezedwa. Abusawo adzayankha mlandu kwa iye komanso kwa Atate wake wakumwamba, za mmene anali kusamalila nkhosa za Mulungu. (Aheb. 13:17; 1 Pet. 5:2, 3) Ponena za Yesu, Yehova mwa ulosi anati: “Taonani! Ine ndamupeleka iye monga mboni kwa mitundu ya anthu, ndiponso monga mtsogoleli ndi wolamulila wa mitundu ya anthu.” (Yes. 55:4) Yesu anaonetsa kuti ulosi umenewu unakwanilitsidwa pamene anauza ophunzila ake kuti: “Musamachedwe ‘atsogoleli,’ pakuti Mtsogoleli wanu ndi mmodzi, Khristu.”—Mat. 23:10.
6 Poonetsa maganizo ake na mtima wofunitsitsa kutithandiza, Yesu akupeleka ciitano kuti: “Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzilani kwa ine, cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.” (Mat. 11:28-30) Potsogolela mpingo wacikhristu mwacikondi ndiponso m’njila imene imatitsitsimula, Yesu Khristu waonetsa kuti ni “m’busa wabwino,” potengela Atate wake wakumwamba Yehova Mulungu.—Yoh. 10:11; Yes. 40:11.
7 M’kalata yake kwa Akorinto, Paulo anafotokoza mbali ina ya udindo wa Yesu Khristu. Anati: “[Iye] ayenela kulamulila monga mfumu kufikila Mulungu ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwanayonso adzadziika pansi pa amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulungu akakhale zinthu zonse kwa aliyense.” (1 Akor. 15:25, 28) Asanabwele pa dziko lapansi, Yesu anali “mmisili waluso,” woyambilila kulengedwa na Mulungu. (Miy. 8:22-31) Pamene Mulungu anatuma Yesu pa dziko lapansi, iye anacita cifunilo ca Atate wake nthawi zonse. Anapilila mayeso osautsa kosaneneka, ndipo anafa ali wokhulupilikabe kwa Atate wake. (Yoh. 4:34; 15:10) Cifukwa cokhalabe wokhulupilika mpaka imfa, Mulungu anamuukitsa kupita kumwamba, na kukamulonga kukhala Mfumu mu Ufumu wakumwamba. (Mac. 2:32-36) Pokhala Mfumu, Khristu Yesu anapatsidwa nchito na Mulungu, yakuti pamodzi na makamu a angelo amphamvu, akacotsepo maulamulilo onse a anthu, pamodzi na zoipa zonse. (Miy. 2:21, 22; 2 Ates. 1:6-9; Chiv. 19:11-21; 20:1-3) Pamenepo, dziko lonse lapansi lidzakhala pansi pa ulamulilo umodzi wokha, wa Ufumu wa Mulungu, wolamulilidwa na Khristu kucokela kumwamba.—Chiv. 11:15.
TINGAONETSE BWANJI KUTI TIVOMELEZA UDINDO WAKE?
8 Yesu Khristu, amene ni Citsanzo cathu, ni wangwilo. Iye anapatsidwa udindo wotisamalila. Conco, kuti tipindule na cisamalilo cake cacikondi, tiyenela kukhalabe okhulupilika kwa Yehova, komanso kumayendela pamodzi na gulu la Yehova lopita patsogolo.
9 Otsatila a Yesu m’nthawi ya atumwi, anavomeleza kwathunthu udindo wa Khristu m’makonzedwe a Mulungu. Anaonetsa zimenezo pogwila nchito mogwilizana pansi pa umutu wa Khristu, akumalabadila malangizo ake opelekedwa mwa mzimu woyela. (Mac. 15:12-21) Pofotokoza mgwilizano umene unalipo pa mpingo wa Akhristu odzozedwa, mtumwi Paulo anati: “Polankhula zoona, tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzela m’cikondi, pansi pa iye amene ndi mutu, Khristu. Kucokela kwa iye, thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwacikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwilizana mwa mfundo iliyonse yogwila nchito yake yofunikila, malinga ndi nchito yoyenelela ya ciwalo ciliconse.”—Aef. 4:15, 16.
10 Ngati onse mumpingo agwila nchito mogwilizana pansi pa utsogoleli wa Khristu, mpingo umakula ndipo cikondi cimawonjezeleka, cimene “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu kwambili.”—Yoh. 10:16; Akol. 3:14; 1 Akor. 12:14-26.
11 Zocitika zapadziko zokwanilitsa maulosi a m’Baibo, zionetsa kuti kuyambila mu 1914, Yesu Khristu wakhala akulamulila monga Mfumu. Inde, akulamulila pakati pa adani ake. (Sal. 2:1-12; 110:1, 2) Kodi izi zitanthauza ciani kwa anthu okhala padziko? Zitanthauza kuti posacedwa, Yesu adzaseŵenzetsa mphamvu zake monga Mfumu ya mafumu, komanso Mbuye wa ambuye, kupeleka ciweluzo ca Mulungu pa adani ake. (Chiv. 11:15; 12:10; 19:16) Pamenepo, Yehova adzakwanilitsa lonjezo lake lopulumutsa anthu okhala ku mbali ya Khristu, limene anapeleka pamene munthu anapanduka. (Mat. 25:34) Ndife okondwa cotani nanga, kuvomeleza udindo wa Khristu m’makonzedwe a Mulungu! Conco, tiyeni tipitilize kugwilana manja pa nchito yolalikila padziko lonse, pansi pa utsogoleli wa Khristu, m’masiku ano otsiliza.