MUTU 15
Kupindula na Cigonjelo ca Umulungu
POKHALA gulu lokhazikitsidwa kucita cifunilo ca Yehova, tiyenela kukhala ogonjela kwa Mulungu, amene ndiye Mfumu ya cilengedwe conse. Timalemekeza Mwana wake monga mutu wa mpingo wacikhristu, ndipo timagonjelanso umutu m’mbali zina za umoyo. Kugonjela umutu kumeneku kumapindulitsa onse okhudzidwa.
2 Anthu anaphunzitsidwa mfundo ya kugonjela ulamulilo kuyambila m’munda wa Edeni. Mfundo imeneyi inaphatikizidwa m’malamulo a Mulungu opezeka pa Genesis 1:28 komanso 2:16, 17. Zamoyo zonse zotsikilapo kwa munthu zinafunikila kukhala zogonjela kwa anthu, pamene Adamu na Hava anafunikila kugonjela ku ulamulilo wa Mulungu mwa kucita cifunilo cake. Kugonjela ulamulilo wa Mulungu kukanabweletsa mtendele na dongosolo labwino la zinthu. Ndipo mfundo yogonjela umutu imeneyi inadzaunikidwanso pa 1 Akorinto 11:3. Pa lembali mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndikufuna mudziŵe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.” Izi zionetsa kuti pa ndondomeko ya umutu yonseyi, aliyense ali na mutu wofunika kuugonjela, kupatulapo Yehova yekha cabe.
3 Anthu ambili masiku ano sailemekeza mfundo yogonjela kwa amene ali mutu. Cifukwa ciani? Vuto linayambila m’munda wa Edeni pamene makolo athu oyambilila anasankha kudzimasula ku ulamulilo wa Mulungu monga mutu. (Gen. 3:4, 5) Ngakhale n’telo, iwo sanapeze ufulu weni-weni. M’malomwake, anadzipeza pansi pa ulamulilo wa munthu wamzimu woipa, Satana Mdyelekezi. Cipanduko coyamba cimeneco cinapatutsa anthu kwa Mulungu. (Akol. 1:21) Pa cifukwa cimeneci, mpaka pano unyinji wa anthu uli m’manja mwa woipayo.—1 Yoh. 5:19.
4 Koma ife pamene tinaphunzila coonadi ca m’Mawu a Mulungu na kuyamba kucigwilitsila nchito, tinacokamo m’manja mwa Satana. Pokhala Mboni za Yehova zodzipatulila, tinadzipeleka kwa Yehova kuti akhale Wolamulila miyoyo yathu. Timavomekezana na Mfumu Davide amene anakamba kuti Yehova ndiye “mutu pa onse.” (1 Mbiri 29:11) Indedi, modzicepetsa timavomeleza mfundo yakuti: “Dziŵani kuti Yehova ndi Mulungu. Iye ndi amene anatipanga, sitinadzipange tokha. Ndife anthu ake ndi nkhosa zimene akuweta.” (Sal. 100:3) Yehova alidi Wamkulukulu ndipo tiyenela kum’gonjela kothelatu, popeza analenga zinthu zonse. (Chiv. 4:11) Inde, monga atumiki a Mulungu woona, timatsatila Yesu Khristu, amene anapeleka citsanzo cabwino koposa pa nkhani yogonjela Mulungu.
5 Kodi Yesu anaphunzilapo ciani pa mavuto amene anakumana nawo padziko lapansi? Aheberi 5:8 imayankha kuti: “Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzila kumvela cifukwa ca mavuto amene anakumana nawo.” Zoonadi, Yesu anakhalabe wogonjela kwa Atate wake wakumwamba ngakhale panthawi ya zovuta. Komanso, Yesu sanacitepo cinthu ciliconse mwa maganizo ake ayi, sanakambepo za m’mutu mwake, ndiponso sanadzifunilepo ulemelelo. (Yoh. 5:19, 30; 6:38; 7:16-18) Pocita utumiki wake, Yesu anakondwela kucita cifunilo ca Atate wake, ngakhale kuti kunam’bweletsela adani ambili na mazunzo. (Yoh. 15:20) Ngakhale n’conco, Yesu anakhalabe wogonjela kwa Mulungu. Iye “anadzicepetsa” mpaka “pamtengo wozunzikilapo.” Kugonjela Yehova na mtima wonse kumeneku kunabweletsa madalitso ambili. Mwa ena, anthu adzapeza moyo wosatha, Yesu anakwezedwa, komanso anapeleka ulemelelo kwa Atate wake.—Afil. 2:5-11; Aheb. 5:9.
MBALI ZOFUNIKILA CIGONJELO CA UMULUNGU
6 Tikakhala ogonjela kwa Mulungu pocita cifunilo cake, tidzapewa nkhawa zambili na zogwilitsa mwala zimene zimapeza anthu okana kugonjela ulamulilo wa Yehova. Mdani wathu Mdyelekezi sagona pankhani yofuna kutibwandila. Kuti tipulumuke kwa woipayo, tiyenela kucilimika potsutsana naye, komanso kudzicepetsa kwa Yehova pocita cifunilo cake.—Mat. 6:10, 13; 1 Pet. 5:6-9.
7 Mumpingo wacikhristu, timalemekeza umutu wa Khristu na ulamulilo umene iye anapatsa “kapolo wokhulupilila ndi wanzelu.” Zimenezi zimaonekela mwa maganizo na mmene timacitilana zinthu wina na mnzake. Tikakhala ogonjela mumpingo, tidzakhalanso omvela Mawu a Mulungu m’mbali zonse za kulambila kwathu. Cimvelo cimeneci cimakhudza utumiki wathu, kupezeka kumisonkhano na kutengako mbali, mgwilizano wathu na akulu, komanso mmene timalemekezela makonzedwe a gulu.—Mat. 24:45-47; 28:19, 20; Aheb. 10:24, 25; 13:7, 17.
8 Cigonjelo cathu kwa Mulungu cimalimbikitsa mtendele, citetezo, na dongosolo mumpingo wacikhristu. Mwa ici, makhalidwe abwino a Yehova amaonekela mwa anthu ake. (1 Akor. 14:33, 40) Zimene taona m’gulu la Yehova zitipangitsa nafenso kubweleza mawu amene Mfumu Davide ananena. Iye ataona kusiyana pakati pa atumiki a Yehova na anthu oipa, anafuula mosangalala kuti: “Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Sal. 144:15.
9 M’kakonzedwe ka banja, ‘mutu wa mkazi ni mwamuna.’ Koma amuna nawonso ayenela kugonjela kwa Khristu, pamene mutu wa Khristu ni Mulungu. (1 Akor. 11:3) Akazi ayenela kugonjela kwa amuna awo, ndipo ana kwa makolo awo. (Aef. 5:22-24; 6:1) Ngati aliyense m’banja alemekeza ndondomeko ya umutu, pamakhala mtendele.
10 Potengela citsanzo ca Khristu, mwamuna ayenela kuyendetsa umutu wake mwacikondi. (Aef. 5:25-29) Ngati apewa kugwilitsila nchito umutu wake molakwika, ndiponso saunyanyala, mkazi wake komanso ana ake azimugonjela mokondwa. Gawo la mkazi n’kukhala wothandiza mwamuna wake, kapena kukhala wom’kwanilitsa. (Gen. 2:18) Pocilikiza mwamuna wake modzicepetsa na kum’lemekeza, mwamuna wake amam’konda kwambili, ndipo Mulungu amatamandika. (1 Pet. 3:1-4) Amuna na akazi awo akamamvela uphungu wa m’Baibo wolemekeza umutu, amapeleka citsanzo cabwino kwa ana awo cogonjela Mulungu.
11 Kugonjela kwathu Mulungu kumakhudzanso mmene timaonela “olamulila akuluakulu,” amene “ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.” (Aroma 13:1-7) Monga nzika zomvela malamulo a boma, Akhristu amakhoma misonkho, amapeleka “zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma zinthu za Mulungu kwa Mlungu.” (Mat. 22:21) Ngakhale pa kafoledwe ka magawo a ulaliki, timatsatilabe malamulo oteteza cinsinsi ca anthu ena. Conco, kukhala ogonjela ndiponso omvela maulamulilo okhazikitsidwa, m’ciliconse cosasemphana na malamulo a Yehova, kumatithandiza kuigwila bwino nchito yolalikila.—Maliko 13:10; Mac. 5:29.
12 Cigonjelo ca umulungu cimafunika m’mbali zonse za umoyo wathu. Na maso acikhulupililo, timatha kuona nthawi pamene anthu onse adzakhala ogonjela kwa Yehova Mulungu. (1 Akor. 15:27, 28) Inde, awo amene amalemekeza ulamulilo wa Yehova mosangalala, na kugonjelabe kwa iye nthawi zonse, adzalandila madalitso osaneneka!
Cigonjelo ca umulungu cimafunika m’mbali zonse za umoyo wathu