LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od mutu 3 masa. 17-23
  • “Kumbukilani Amene Akutsogolela Pakati Panu”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Kumbukilani Amene Akutsogolela Pakati Panu”
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMUDZIŴA “KAPOLO WOKHULUPILIKA NDI WANZELU”
  • N’CIFUKWA CIANI TIYENELA ‘KUKUMBUKILA AMENE AMATITSOGOLELA’?
  • MMENE TIMAONETSELA KUTI TIMAWADALILA OTITSOGOLELA
  • “Ndani Kweni-kweni Amene Ali Kapolo Wokhulupilika Ndi wanzelu?”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Kodi Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu Ndani?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Udindo wa “Kapolo Wokhulupilika ndi Wanzelu”
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • N’ndani Akutsogolela Anthu a Mulungu Masiku Ano?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od mutu 3 masa. 17-23

MUTU 3

“Kumbukilani Amene Akutsogolela Pakati Panu”

MAWU a mtumwi Paulo amenewa, opezeka pa Aheberi 13:7, angamasulidwenso kuti: “Kumbukilani akutsogolo kwanu.” Kucokela pa Pentekosite wa mu 33 C.E., atumwi okhulupilika a Ambuye Yesu Khristu ndiwo anatumikila monga bungwe lolamulila. Iwo anali kupeleka malangizo ku mpingo wacikhristu umene unangokhazikitsidwa cakumene. (Mac. 6:2-4) Pofika m’caka ca 49 C.E., bungwe lolamulila linakulilako powonjezelapo abale ena amene sanali atumwi a Yesu. Pokambilana nkhani ya mdulidwe, m’bungwe lolamulila munali “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu.” (Mac. 15:1, 2) Unali udindo wawo kusamalila nkhani zokhudza Akhristu kulikonse. Iwo anali kutumiza makalata na malamulo kuti alimbitse mipingo, komanso kuti ophunzila onse a Yesu apitilize kukhala pa umodzi wa maganizo na zocita. Mipingo inali kulabadila na kugonjela citsogozo ca bungwe lolamulila. Zotsatilapo zake n’zakuti Yehova anadalitsa mipingoyo, cakuti inapitiliza kukula na kuwonjezeleka.—Mac. 8:1, 14, 15; 15:22-31; 16:4, 5; Aheb. 13:17.

2 Atumwi onse atamwalila, mpatuko waukulu unayambika. (2 Ates. 2:3-12) Monga mmene Yesu anakambilatu mu fanizo la tiligu komanso namsongole, tiligu (Akhristu odzozedwa) anafesedwa pakati pa namsongole (Akhristu onyenga). Kwa zaka zambili, magulu aŵiliwa analoledwa kukulila pamodzi kufikila nthawi yokolola, imene ni “mapeto a nthawi ino.” (Mat. 13:24-30, 36-43) M’nthawi imeneyi, Yesu anali kusamalila Mkhristu wodzozedwa aliyense payekha-payekha. Palibe bungwe lolamulila, kapena munthu wodziŵika bwino padziko lapansi, mwa amene Yesu anali kutsogolela otsatila ake. (Mat. 28:20) Ngakhale n’telo, iye anakambilatu kuti zinthu zidzasintha panthawi yokolola.

3 “Ndani kweni-kweni amene ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu?” Poyankha funso limeneli, Yesu Khristu anafotokoza fanizo, kapena kuti citsanzo, cimene ni mbali ya “cizindikilo” ca “mapeto a nthawi ino.” (Mat. 24:3, 42-47) Yesu anaonetsa kuti kapolo wokhulupilika ameneyu, adzakhala wotangwanika na kupeleka cakudya cauzimu kwa anthu a Mulungu “pa nthawi yoyenela.” M’nthawi ya Akhristu oyambilila, Yesu anaseŵenzetsa gulu la amuna [osati munthu mmodzi] kuti atsogolele. N’cimodzimodzinso m’nthawi ino yamapeto. Kapolo wokhulupilika amene Yesu akuseŵenzetsa ni kagulu, osati munthu mmodzi.

KUMUDZIŴA “KAPOLO WOKHULUPILIKA NDI WANZELU”

4 Kodi Yesu anaika ndani kuti azidyetsa otsatila ake? M’pomveka kuti anapatsa udindo umenewu Akhristu odzozedwa padziko lapansi. Baibo imawacha “ansembe acifumu” amene anapatsidwa nchito ‘yolengeza makhalidwe abwino kwambili a uyo amene anawaitana kucoka mu mdima kukaloŵa m’kuwala kwake kodabwitsa.’ (1 Pet. 2:9; Mal. 2:7; Chiv. 12:17) Kodi kapolo wokhulupilika ameneyu amaphatikizapo Akhristu odzozedwa onse padziko lapansi? Iyai. Pamene Yesu mozizwitsa anadyetsa amuna 5,000, kusaŵelengelapo akazi na ŵana, anapeleka cakudyaco kwa ophunzila ake, ndipo iwo anacigaŵila kwa anthuwo. (Mat. 14:19) Anadyetsa ambili poseŵenzetsa anthu ocepa. Masiku anonso, iye amapeleka cakudya cauzimu mwa njila yofananayo.

5 Conco, “mtumiki woyang’anila nyumba wokhulupilika ndi wanzelu,” ni kagulu kocepa ka abale odzozedwa amene amakonza na kugaŵila cakudya cauzimu m’nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. (Luka 12:42) M’masiku ano otsiliza, abale odzozedwa omwe ndiwo “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” akhala akutumikila pamodzi ku likulu lathu. Lelo lino, abale odzozedwa amenewa ndiwo akupanga Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova.

6 Khristu amagwilitsila nchito bungwe limeneli kufalitsa nkhani zounikila kukwanilitsidwa kwa maulosi a m’Baibo, komanso kupeleka malangizo a pa nthawi yake a mmene tingatsatilile mfundo za m’Baibo pa umoyo wathu. Cakudya cauzimu cimeneco cimapelekedwa kudzela m’mipingo ya Mboni za Yehova. (Yes. 43:10; Agal. 6:16) M’nthawi za m’Baibo, kapolo wokhulupilika, kapena kuti mtumiki, anali kuyang’anila zonse zapanyumba. Mofananamo, kapolo wokhulupilika ndi wanzelu wapatsidwa udindo woyang’anila banja la cikhulupililo. Amayang’anilanso cuma, nchito yolalikila, mapulogilamu a misonkhano yadela komanso yacigawo, kulemba mabuku ophunzilila Baibo, na kuika abale pa maudindo olekana-lekana m’gulu lathu. Zonsezi zimapindulitsa “anchito a pakhomo” onse.—Mat. 24:45.

7 Nanga “anchito a pakhomo” ndani? Mwacidule, ni onse amene amadyetsedwa mwauzimu. Poyamba, odzozedwa okha ndiwo anali anchito apakhomo. M’kupita kwa nthawi, anchitowo anadzaphatikizapo khamu lalikulu la “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Magulu onse aŵiliwa amadya cakudya cauzimu cogaŵilidwa na kapolo wokhulupilika.

8 Pamene Yesu adzabwela pa cisautso cacikulu kudzaweluza dziko loipali, adzaika kapolo wokhulupilika kuti “aziyang’anila zinthu zake zonse.” (Mat. 24:46, 47) Pamenepo a kagulu ka kapolo wokhulupilika adzalandila mphoto yawo yakumwamba. Onse pamodzi okwana 144,000, adzalamulila pamodzi na Khristu kumwamba. Olo kuti padziko lapansi padzakhala palibe kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, Yehova na Yesu adzapeleka malangizo ku nzika za Ufumu wa Mesiya, kupitila mwa abale amene adzaikidwe kukhala “akalonga.”—Sal. 45:16.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA ‘KUKUMBUKILA AMENE AMATITSOGOLELA’?

9 Pali zifukwa zambili zokumbukilila ‘amene amatitsogolela’ na kuwakhulupilila. N’cifukwa ciani kucita izi kuli kwaphindu kwa ife? Mtumwi Paulo anakamba kuti: “Iwo amayang’anila miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvela ndi kuwagonjela kuti agwile nchito yawo mwacimwemwe, osati modandaula, pakuti akatelo zingakhale zokuvulazani.” (Aheb. 13:17) Conco, tiyenela kumvela na kugonjela citsogozo ca awo amene amatitsogolela, cifukwa amatiyang’anila na kutiteteza mwauzimu.

10 Pa 1 Akorinto 16:14, Paulo anati: “Zonse zimene mukucita, muzicite mwacikondi.” Zigamulo zimene iwo amapanga zokhudza anthu a Mulungu, zimazikidwa pa cikondi ceni-ceni. Ponena za cikondi cimeneco, 1 Akorinto 13:4-8 imati: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. Cikondi sicicita nsanje, sicidzitama, sicidzikuza, sicicita zosayenela, sicisamala zofuna zake zokha, sicikwiya. Sicisunga zifukwa. Sicikondwela ndi zosalungama, koma cimakondwela ndi coonadi. Cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse. Cikondi sicitha.” Inde, popeza zigamulo zawo zonse zimazikidwa pa cikondi copindulitsa atumiki a Yehova, ndife otetezeka kwambili pansi pa uyang’anilo wawo. Ndipo Yehova ndiye gwelo la cikondi cimeneci.

Tikhale ogonjela kwa aja oyang’anila umoyo wathu wauzimu

11 Monga zinalili m’nthawi ya Akhristu oyambilila, Yehova amagwilitsila nchito anthu opanda ungwilo kutsogolela gulu lake. Kuyambila kale, Yehova wakhala akugwilitsila nchito anthu opanda ungwilo kuti akwanilitse cifunilo cake. Nowa anakhoma cingalawa na kulalikila za ciwonongeko. (Gen. 6:13, 14, 22; 2 Pet. 2:5) Mose anasankhidwa kuti atsogolele anthu a Yehova kutuluka mu Iguputo. (Eks. 3:10) Amuna opanda ungwilo anauzilidwa kulemba Baibo. (2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21) Sititaya cidalilo cathu pa gulu la Mulungu, ngakhale kuti Yehova amagwilitsila nchito anthu opanda ungwilo kutsogolela nchito yolalikila na kupanga ophunzila. M’malomwake, zimatilimbikitsa podziŵa kuti popanda thandizo la Yehova, gulu lathu silikanakwanitsa kucita zimene limacita. Ngakhale kuti kapolo wokhulupilikayo wapita m’mavuto ambili, iye waonetsa kuti amatsogoleledwa na mzimu wa Mulungu. Yehova wakhala akukhuthulila madalitso ake pa gawo la padziko lapansi la gulu lake. Conco, tiyeni tilicilikize gulu limeneli, komanso tilikhulupilile na mtima wonse.

MMENE TIMAONETSELA KUTI TIMAWADALILA OTITSOGOLELA

12 Awo amene aikidwa pa maudindo mumpingo amaonetsa kuti amakhulupilila kapoloyo ngati alandila maudindowo na manja aŵili, komanso kukwanilitsa nchito zake. (Mac. 20:28) Monga alengezi a Ufumu, timalalikila mokangalika ku nyumba na nyumba, kucita maulendo obwelelako, na kutsogoza maphunzilo a Baibo. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kuti tizipindula mofikapo na cakudya cauzimu cimene kapolo wokhulupilika amapeleka, tiyenela kumakonzekela misonkhano ya mpingo na kupezekapo, kuphatikizapo misonkhano yadela komanso yacigawo. Pamisonkhano imeneyi, timapindula ngako na mayanjano olimbikitsana na abale athu.—Aheb. 10:24, 25.

13 Tikamacilikiza gulu la Mulungu na zopeleka zathu, timaonetsa kuti timalidalila. (Miy. 3:9, 10) Tikaona kuti abale athu ni osoŵa kuthupi, timagwapo mwamsanga kuti tiwathandize. (Agal. 6:10; 1 Tim. 6:18) Timacita izi na mzimu wacikondi. Timakhala chelu nthawi zonse kufuna mipata yothandizilana, pofuna kuonetsa Yehova na gulu lake kuti timayamikila zabwino zimene amaticitila.—Yoh. 13:35.

14 Timaonetsanso kuti timadalila gulu la Mulungu mwa kulabadila zigamulo zake. Timakhalanso odzicepetsa potsatila citsogozo ca abale oikidwa pa maudindo, monga oyang’anila madela komanso akulu mumpingo. Abalewa akuphatikizidwa pa “amene akutsogolela,” oyenela kuwamvela na kuwagonjela. (Aheb. 13:7, 17) Ngakhale tisamvetse zifukwa zonse zopangila zigamulo zina zake, timadziŵa kuti kulabadilabe kuli na ubwino wake kwa ife. Zotulukapo n’zakuti Yehova amatidalitsa pomvela Mawu ake na gulu lake. Tikatelo, timaonetsanso kuti timagonjela Mbuye wathu, Yesu Khristu.

15 Inde, tili na zifukwa zambili zodalila kapolo wokhulupilika ndi wanzelu. Satana, mulungu wa dongosolo loipali, akucita zonse zotheka kuti abweletse citonzo pa dzina la Yehova na gulu lake. (2 Akor. 4:4) Koma inuyo musakopeke na macenjela oipa a Satana. (2 Akor. 2:11) Iye amadziŵa kuti “wangotsala ndi kanthawi kocepa” cabe kuti aponyedwe ku phompho, ndipo akucita zonse zotheka kuti apatutse anthu a Yehova ambili pa coonadi. (Chiv. 12:12) Conco, pamene Satana akuwonjezela macenjela ake, tiyeni tiyandikane naye kwambili Yehova. Tiike cidalilo cathu conse mwa Yehova, komanso m’makonzedwe amene akugwilitsila nchito potsogolela anthu ake lelo. Tikatelo, ubale wathu wa padziko lonse udzalimbila-limbila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani