NYIMBO 114
“Khalani Oleza Mtima”
Yopulinta
	(Yakobo 5:8)
- 1. Yehova Mbuye wathu - Amakonda dzina lake. - Iye afunitsitsa - Kuti lisamanyozedwe. - Kucokela kalelo - Iye apililabe. - Yehova sanatope, - Amaleza mtima. - Afuna kuti anthu - Onse akapulumuke. - Kuleza mtima kwake - Sikudzapita pacabe. 
- 2. Tifunika kukhala - Oleza mtima kwa onse. - Tidzapeza mtendele - Ndipo tidzapewa mkwiyo. - Tidzapewa kuona - Zoipa mwa anzathu. - Tikhale odziletsa - Olo pa mavuto. - Titengele Yehova - Tikhale oleza mtima. - Ise tikayesetsa - Tidzapeza madalitso. 
(Onaninso Eks. 34:14; Yes. 40:28; 1 Akor. 13:4, 7; 1 Tim. 2:4.)