NYIMBO 103
Abusa ni Mphatso za Amuna
Yopulinta
(Aefeso 4:8)
1. Yehova ‘tipatsa Abusa,
Kuti atiwete.
Mwa citsanzo cawo cabwino,
Amatsogolela.
(KOLASI)
M’lungu watipatsa amuna,
Amatisamalila.
Iwo ni okhulupilika;
Ise tiziŵakonda.
2. Abusawa amatikonda;
Amatisamala.
Tikavulala mwauzimu,
Amaticilitsa.
(KOLASI)
M’lungu watipatsa amuna,
Amatisamalila.
Iwo ni okhulupilika;
Ise tiziŵakonda.
3. Kuti ise tisatayike,
Amatilangiza.
Amatithandiza kuyenda,
M’njila ya Yehova.
(KOLASI)
M’lungu watipatsa amuna,
Amatisamalila.
Iwo ni okhulupilika;
Ise tiziŵakonda.
(Onaninso Yes. 32:1, 2; Yer. 3:15; Yoh. 21:15-17; Mac. 20:28.)