LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • bh nkhani 200-nkhani 201 pala. 4
  • Yesu Kristu—Mesiya Wolonjezedwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Kristu—Mesiya Wolonjezedwa
  • Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
bh nkhani 200-nkhani 201 pala. 4

ZAKUMAPETO

Yesu Kristu—Mesiya Wolonjezedwa

KUTI atithandize kuzindikila Mesiya, Yehova Mulungu anauzila aneneli ambili kuti alosele za kubadwa kwa mpulumutsi wolonjezedwa ameneyu, utumiki wake, ndi imfa yake. Maulosi onse a m’Baibo amenewo anakwanilitsika mwa Yesu Kristu. Kulondola kwake ndi tsatane-tsatane wa maulosi amenewa n’kocititsa cidwi. Mwacitsanzo, tiyeni tione maulosi ocepa cabe amene anakambilatu za zinthu zokhudza kubadwa kwa Mesiya ndi mmene umoyo wake unalili pamene anali mwana.

Mneneli Yesaya anakambilatu kuti Mesiya adzakhala mbadwa ya Mfumu Davide. (Yesaya 9:7) Ndipo Yesu anabadwiladi mu mzela wa Davide.—Mateyu 1:1, 6-17.

Mneneli wina wa Mulungu, Mika, nayenso anakambilatu kuti mwana ameneyu adzabadwila mu “Betelehemu Efurata,” ndi kuti m’kupita kwa nthawi adzakhala wolamulila. (Mika 5:2) Panthawi ya kubadwa kwa Yesu, mu Isiraeli munali matauni aŵili ochedwa Betelehemu. Tauni imodzi inali kumpoto kwa dzikolo, ndipo ina inali pafupi ndi Yerusalemu m’dziko la Yuda. Tauni ya Betelehemu imene inali pafupi ndi Yerusalemu poyamba inali kuchedwa Efurata. Yesu anabadwila m’tauni imeneyi, ndendende monga mmene maulosi anakambila.—Mateyu 2:1.

Ulosi wina wa m’Baibo unakambilatu kuti mwana wa Mulungu adzaitanidwa “kuti atuluke mu Iguputo.” Pamene anali mwana, Yesu anapita naye ku Iguputo. Pambuyo pa imfa ya Herode, anabwelela naye kudziko lakwao, ndipo zimenezi zinakwanilitsa ulosi.—Hoseya 11:1; Mateyu 2:15.

Pa chati imene ili papeji 200, pali malemba amene aikidwa pansi pa mutu wakuti “Ulosi” amene ali ndi mfundo zokamba za Mesiya. Yelekezelani zimenezi ndi malemba amene ali pa mutu wakuti “Kukwanilitsika.” Kucita zimenezi kudzalimbikitsa kwambili cikhulupililo canu cakuti Mau a Mulungu ndi oona.

Pamene muona malemba aulosi amenewa, kumbukilani kuti analembedwa zaka mazana ambili Yesu akalibe kubadwa. Yesu anati: “Zonse zokhudza ine zolembedwa m’cilamulo ca Mose, mu zolemba za Aneneli ndi m’Masalimo ziyenela kukwanilitsidwa.” (Luka 24:44) Pamene muona m’Baibo yanu mudzapeza kuti, mbali iliyonse ya maulosi onsewa inakwanilitsika!

MAULOSI OKAMBA ZA MESIYA

COCITIKA

ULOSI

KUKWANILITSIKA

Adzabadwila m’fuko la Yuda

Genesis 49:10

Luka 3:23-33

Adzabadwa kwa namwali

Yesaya 7:14

Mateyu 1:18-25

Adzabadwila mu mzela wa Mfumu Davide

Yesaya 9:7

Mateyu 1:1, 6-17

Yehova adzam’lengeza kuti ndi Mwana wake

Salimo 2:7

Mateyu 3:17

Sadzam’khulupilila

Yesaya 53:1

Yohane 12:37, 38

Adzaloŵa mu Yerusalemu atakwela pa bulu

Zekariya 9:9

Mateyu 21:1-9

Adzapelekedwa ndi mnzake

Salimo 41:9

Yohane 13:18, 21-30

Adzam’peleka ndi ndalama 30 za siliva

Zekariya 11:12

Mateyu 26:14-16

Adzakhala cete pamaso pa omuimba mlandu

Yesaya 53:7

Mateyu 27:11-14

Adzacita maele pa zovala zake

Salimo 22:18

Mateyu 27:35

Adzanyozedwa ali pa mtengo wozunzikilapo

Salimo 22:7, 8

Mateyu 27:39-43

Sadzathyola ngakhale fupa lake limodzi

Salimo 34:20

Yohane 19:33, 36

Adzaikidwa m’manda a munthu wolemela

Yesaya 53:9

Mateyu 27:57-60

Adzaukitsidwa akalibe kuvunda

Salimo 16:10

Machitidwe 2:24, 27

Adzakwezedwa kukhala ku dzanja lamanja la Mulungu

Salimo 110:1

Machitidwe 7:56

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani