-
Nkhani Yofunika KwambiliNsanja ya Mlonda (Yogawila)—2016 | No. 4
-
-
NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA
Nkhani Yofunika Kwambili
Palibe buku ina yacipembedzo imene ingalingane ndi Baibulo. Anthu ambili akhala akuikhulupilila kwa nthawi yaitali kupambana mabuku ena. Komabe, palibe buku ina imene yafufuzidwa kwambili ndi kutsutsidwa kuposa Baibulo.
Mwacitsanzo, akatswili ena amakaikila ngati zimene zili m’Mabaibulo a masiku ano n’zimenenso zinali m’mipukutu yoyambilila ya Baibulo. Pulofesa wina wa maphunzilo a zacipembedzo anati: “Sitidziŵa ngati tamasulila Baibulo molondola mogwilizana ndi mipukutu yoyambilila. Makope amene tili nawo ali ndi zolakwika zambili, ndipo analembedwa zaka mahandiledi ambili mipukutu yoyambilila ya Baibulo italembedwa kale. Makope amenewa ni osiyana ndi mipukutu yoyambilila m’njila zambili.”
Anthu ena amakaikila ngati Baibulo ni yoona cifukwa ca cipembedzo cao. Mwacitsanzo, Faizal anaphunzitsidwa ndi makolo ake, amene sanali Akhiristu, kuti Baibulo ni buku yopatulika koma inasinthidwa. Iye anakamba kuti: “Anthu akafuna kuniphunzitsa Baibulo, n’nali kukana. N’nali kuona kuti io analibe Baibulo yoyambilila ndipo Baibulo imene anali nayo inasinthidwa.”
Kodi kudziŵa kuti Baibulo inasinthidwa kapena ayi kuli ndi phindu? Inde. Ganizilani mafunso awa: Kodi mungakhulupilile malonjezo otonthoza a m’Baibulo ngati simudziŵa kuti malonjezowo analimo m’mipukutu yoyambilila ya Baibulo? (Aroma 15:4) Kodi mukanatsatila mfundo za m’Baibulo popanga zosankha zofunika kwambili monga zokhudza nchito, banja, kapena kulambila, ngati Mabaibulo a masiku ano anali ndi zolakwika zokhazokha?
Ngakhale kuti mipukutu yoyambilila ya Baibulo palibe, tingatsimikizile kuti Mabaibulo amene tili nao ni olondola mwa kuwayelekezela ndi makope ndiponso mipukutu yakale ya Baibulo. Kodi mipukutu imeneyo inapulumuka bwanji kuti isawonongeke? Nanga inapulumuka bwanji kwa anthu otsutsa ndi ofuna kusintha uthenga wake? Kodi kudziŵa mmene inapulumukila kungakuthandizeni bwanji kukhulupilila kuti Baibulo imene tili nayo masiku ano ni yoona? Pezani mayankho a mafunso amenewa m’nkhani yotsatila yokamba za mmene Baibulo inapulumukila.
-
-
Baibulo SiinawoleNsanja ya Mlonda (Yogawila)—2016 | No. 4
-
-
NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA
Baibulo Siinawole
VUTO LIMENE LINALIPO: Olemba Baibulo ndi okopela malemba, nthawi zambili anali kuseŵenzetsa gumbwa ndi zikopa (zikumba) za nyama.a (2 Timoteyo 4:13) Kodi zinthu zimenezi zikanapangitsa bwanji kuti Baibulo iwonongeke?
Gumbwa imang’ambika mosavuta, imasintha maonekedwe, ndipo imawonongeka. Akatswili odziŵa mbili ya ku Iguputo, Richard Parkinson ndi Stephen Quirke, anakamba kuti: “Gumbwa amawola mwamsanga ndi kusanduka dothi. Akasungidwa, akhoza kuwola ndi cinyontho kapena kudyewa ndi makoswe kapenanso tuzilombo twina, makamaka ciswe ngati amubisa m’nthaka.” Ofufuza anapeza kuti akaika gumbwa padzuŵa kapena pamalo a cinyontho, amawonongeka mofulumila.
Cikumba ca nyama n’colimba kupambana gumbwa, koma cimawonongeka ngati sicinasamalidwe bwino, kapena ngati caikidwa pamalo otentha kwambili, a cinyontho, kapena padzuŵa.b Cikumba naconso cimadyewa na tuzilombo. Ndiye cifukwa cake zolemba zambili zakale kulibe masiku ano. Baibulo ikanawonongeka, sembe uthenga wake kulibe.
MMENE BAIBULO INATETEZEKELA: M’cilamulo cimene Ayuda anapatsidwa, munali lamulo lakuti mfumu iliyonse iyenela “kukopela buku lakelake la Cilamulo,” kutanthauza mabuku asanu oyambilila a m’Baibulo. (Deuteronomo 17:18) Kuonjezela apo, okopela malemba aluso analemba mipukutu yambili cakuti pofika m’nthawi ya atumwi, Malemba anali kupezeka m’masunagoge a m’dziko lonse la Isiraeli, ngakhale kutali kwambili ku Makedoniya. (Luka 4:16, 17; Machitidwe 17:11) Kodi mipukutu yakale imeneyo inapulumuka bwanji?
Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inapezeka m’mitsuko imene anaisungila m’mapanga a m’zipululu. Mipukutuyi yakhalapo kwa zaka zambili
Katswili wa Cipangano Catsopano dzina lake Philip W. Comfort anati: “Ayuda anali kukonda kuika mipukutu ya Malemba m’mitsuko kuti isungike bwino.” Mwacionekele, Akhiristu anapitiliza kucita zimenezo. Ndipo mipukutu ina yoyambilila ya Baibulo inapezeka m’mitsuko, m’zipinda zosungilamo zinthu, ndi m’mapanga. Ina anaipeza m’zipululu.
ZOTSATILAPO ZAKE: Mipukutu ya Baibulo masauzande ambili ikalipo. Ina mwa mipukutu imeneyo inalembedwa zaka zoposa 2,000 zapitazo. Palibe buku lina lakale limene lili ndi mipukutu yambili imene inalembedwa kale kwambili monga ya Baibulo.
a Gumbwa ndi zomela zinazake za m’madzi zimene kale anali kupangila mapepala.
b Mwacitsanzo, cikalata ca boma la United States coonetsa kuti dzikolo lalandila ufulu wodzilamulila cinalembedwa pa cikumba ca nyama. Koma tsopano n’cowonongeka kwambili cakuti mawu ambili anafutika ngakhale kuti papita zaka zosakwana 250.
-
-
Baibulo Inapulumuka kwa Anthu OtsutsaNsanja ya Mlonda (Yogawila)—2016 | No. 4
-
-
NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA
Baibulo Inapulumuka kwa Anthu Otsutsa
VUTO LIMENE LINALIPO: Abusa ndi atsogoleli a ndale ambili anali ndi zolinga zosagwilizana ndi uthenga wa m’Baibulo. Nthawi zambili, anali kuletsa anthu kukhala ndi Baibulo, kuisindikiza, kapena kuimasulila. Tiyeni tione zitsanzo ziŵili izi:
Ca m’ma 167 B.C.E.: Mfumu yaciselukasi dzina lake Antiyokasi Epifanasi, amene anali kukakamiza Ayuda kuyamba cipembedzo ca Cigiriki, analamula kuti mipukutu yonse ya Malemba a Ciheberi iwonongedwe. Wolemba mbili yakale Heinrich Graetz, analemba kuti nduna za mfumuyi “zikapeza mipukutu ya Cilamulo zinali kuing’amba ndi kuitentha.” Analembanso kuti nduna zimenezi “zinali kupha anthu onse amene anali kuŵelenga malemba kuti apeze citonthozo ndi cilimbikitso.”
Zaka za m’ma 500 C.E. mpaka 1500 C.E.: Abusa ena Acikatolika anali kukwiya kwambili akaona mamembala awo ena akulalikila zimene Baibulo imaphunzitsa, m’malo mwa ziphunzitso za Cikatolika. Abusawo akaona anthu akuseŵenzetsa mabuku ena a m’Baibulo, kusiyapo buku la Masalimo la Cilatini, anali kuwaona ngati ampatuko. Atsogoleli a chalichi cina analamula amuna ena kuti ‘akafufuze mwakhama anthu ampatuko m’nyumba zonse zimene anali kuganizila kuti muli Mabaibulo. . . . Nyumba iliyonse imene apezamo anthu ampatuko inafunika kuwonongedwa.’
Adani amenewa akanakwanitsa kuononga Mabaibulo onse, sembe kulibe Baibulo masiku ano.
Baibulo ya Cingelezi ya William Tyndale inatetezeka ngakhale kuti atsogoleli ena anali kuletsa anthu kukhala ndi Baibulo, anali kuitentha, ndipo anapha Tyndale mu 1536
MMENE BAIBULO INATETEZEKELA: Ngakhale kuti Mfumu Antiyokasi inayesetsa kuononga Mabaibulo m’dziko la Isiraeli, panthawiyo Ayuda anali atafalikila kale m’maiko ena ambili. Ndipo akatswili amakamba kuti pofika m’nthawi ya atumwi, Ayuda oposa 60 pelesenti sanali kukhala m’dziko la Isiraeli. Ayuda anali kusunga mipukutu ya Malemba m’masunagoge awo. Patapita zaka zambili, anthu ena, kuphatikizapo Akhiristu, anayamba kugwilitsila nchito mipukutu imeneyo.—Machitidwe 15:21.
M’zaka za pakati pa 500 C.E. ndi 1500 C.E., anthu okonda Baibulo anapitiliza kuimasulila ndi kukopela Malemba ake ngakhale kuti anali kuzunzidwa kwambili. Pofika zaka za m’ma 1400 C.E., zigawo za Baibulo ziyenela kuti zinali zitamasulidwa kale m’zinenelo 33. Zimenezi zinacitika akalibe kutulukila makina opulintila. Pambuyo potulukila makina opulintila, nchito yomasulila ndi kusindikiza Mabaibulo inayamba kucitika mofulumila kwambili.
ZOTSATILAPO ZAKE: Baibulo ni buku imene yamasulidwa ndi kufalitsidwa kwambili m’mbili yonse ya anthu, ngakhale kuti mafumu amphamvu ndi abusa a cipembedzo anayesetsa kuti aiwononge. Baibulo yasintha kwambili malamulo a m’maiko ena, makhalidwe a anthu, ndi zinenelo zambili.
-
-
Baibulo Inapulumuka kwa Anthu Ofuna Kusintha Uthenga WakeNsanja ya Mlonda (Yogawila)—2016 | No. 4
-
-
Amasorete anakopela Malemba mosamala kwambili
NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA
Baibulo Inapulumuka kwa Anthu Ofuna Kusintha Uthenga Wake
VUTO LIMENE LINALIPO: Anthu otsutsa ndiponso zinthu zimene analembapo uthenga wa m’Baibulo, sizinapangitse kuti Baibulo iwonongedwe. Koma sizinathele pamenepo. Anthu okopela ndi omasulila malemba anayesa kusintha uthenga wa m’Baibulo. Nthawi zina, anali kusintha mau a m’Baibulo kuti agwilizane ndi zikhulupililo zawo, m’malo mokhulupilila zimene Baibulo imaphunzitsa. Onani zitsanzo zotsatilazi:
Malo olambilila: Zaka zapakati pa 100 B.C.E. ndi 300 B.C.E., olemba Pentatuke ya Asamariya anawonjezelapo mawu ena pa Ekisodo 20:17 akuti “ku Gerizimu. Kumeneko mudzamanga guwa la nsembe.” Pamenepa, Asamariya anali kufuna kuti Malemba agwilizane ndi nchito yawo yomanga kacisi ku “Gerizimu” kapena kuti pa Phili la Gerizimu.
Ciphunzitso ca Utatu: Patapita zaka pafupifupi 300 pambuyo pakuti Baibulo yatha kulembedwa, munthu wina wokhulupilila Utatu anawonjezela mawu ena pa 1 Yohane 5:7 akuti “kumwamba, Atate, Mawu, ndi Mzimu Woyela: ndipo atatu amenewa ndi mmodzi.” Mawu amenewa mulibe mumpukutu woyambilila wa Baibulo. Katswili wina wa Baibulo dzina lake Bruce Metzger, anati: “Kuyambila zaka za m’ma 500 C.E.,” mawu amenewa anali “kupezeka kwambili m’mipukutu ya Cilatini Cakale ndi Baibulo la Cilatini lochedwa Vulgate.”
Dzina la Mulungu: Potengela mwambo wa Ayuda, omasulila Baibulo ambili anaganiza zocotsa dzina la Mulungu m’Malemba. M’malomwake, anaikamo maina audindo monga akuti “Mulungu” kapena “Ambuye.” Komabe m’Baibulo, maina audindo amenewa sagwilitsidwa nchito ponena za Mlengi cabe, koma amagwilitsidwanso nchito ponena za anthu, mafano, ngakhale Mdyelekezi amene.—Yohane 10:34, 35; 1 Akorinto 8:5, 6; 2 Akorinto 4:4.a
MMENE BAIBULO INATETEZEKELA: Coyamba, ngakhale kuti okopela Baibulo ena anali osasamala ndi acinyengo, ambili anali aluso ndi osamala kwambili. Zaka zapakati pa 500 C.E. ndi 900 C.E., Amasorete anakopela Malemba Aciheberi. Zimene anakopelazo zimachedwa kuti malemba Acimasorete. Iwo anali kupenda mau ndi zilembo mosamala kuti pasapezeke zolakwika zilizonse. Akapeza kuti zimene anali kukopela zinali zolakwika penapake, anali kulemba mau ofotokoza zimenezo m’mphepete mwa pepala. Amasorete anapewelatu kusintha uthenga wa m’Baibulo. Pulofesa wina dzina lake Moshe Goshen-Gottstein analemba kuti: “Iwo anali kuona kuti kusintha mwadala mau a m’Baibulo ndi mlandu waukulu.”
Caciŵili, popeza kuti pali mipukutu yambili masiku ano, akatswili a Baibulo amakwanitsa kudziŵa mawu olakwika. Mwacitsanzo, kwa zaka zambili, abusa a cipembedzo anali kuuza anthu kuti Mabaibulo awo a Cilatini ni amene anali ndi mawu olongosoka a m’Baibulo. Komabe, pa 1 Yohane 5:7, anawonjezelapo mawu olakwika amene tawachula kale m’nkhani ino. Mawu olakwikawo anayamba kupezeka ngakhale m’Baibulo yochuka yacingelezi ya King James Version. Koma atapeza mipukutu ina, zenizeni zinadziŵika. Bruce Metzger analemba kuti: “Mawu olakwikawo [a pa 1 Yohane 5:7] mulibe m’mipukutu yonse yakale (ya Cisiriya, Cikoputiki, Ciameniya, Ciitiyopiya, Ciarabu, Cisilavo), kupatulapo ya Cilatini.” Zotsatilapo zake n’zakuti Mabaibulo okonzedwanso a King James Version ndi Mabaibulo ena anacotsamo mawu olakwikawo.
Chester Beatty P46, mpukutu wa Baibulo wolembedwa pa gumbwa m’zaka za m’ma 200 C.E.
Kodi mipukutu ya Baibulo yakale imatsimikizila bwanji kuti uthenga wa m’Baibulo unatetezedwa? Pamene Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inapezeka mu 1947, akatswili a Baibulo anayelekezela malemba Aciheberi Acimasorete ndi zimene zinali m’mipukutuyo. Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inalembedwa zaka zoposa 1000, malemba Aciheberi Acimasorete akalibe kulembedwa. Mmodzi wa olemba nkhani zokhudza Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa anakamba kuti mpukutu umodzi “ndi wokwanila kupeleka umboni woonekelatu wakuti anthu Aciyuda amene anakopela mawu a m’Baibulo pa zaka zopitilila 1000 anali okhulupilika ndi osamala kwambili.”
M’laibulale ina ya mumzinda wa Dublin m’dziko la Ireland, muli mabuku pafupifupi onse a Malemba Acigiriki Acikhiristu olembedwa pa gumbwa. Mulinso mipukutu ya m’zaka za m’ma 100 C.E., imene inalembedwa patapita zaka pafupifupi 100 pambuyo pakuti Baibulo yatha kulembedwa. Dikishonale ina inati: “Ngakhale kuti zimene zinalembedwa pa gumbwa zikuonetsa njila ya kalembedwe katsopano, zolembazi zinalembedwa molondola kwambili ndipo zionetsa kuti Baibulo ni buku lodalilika.” (The Anchor Bible Dictionary)
“Tingakambe motsimikiza kuti palibe zolemba zina zakale zimene uthenga wake unakopedwa mosamala kwambili kupambana Malemba Aciheberi.”
ZOTSATILAPO ZAKE: Ngakhale kuti pali mipukutu yambili ya Baibulo ndipo ina ni yakale kwambili, uthenga wa m’Baibulo sunasinthe. M’malomwake, mipukutu imeneyi yathandiza kuti Mabaibulo a masiku ano akhale olondola kwambili. Pokamba za Malemba Acigiriki Acikhiristu, Sir Frederic Kenyon analemba kuti: “Palibe buku lina lakale limene lili ndi umboni woculuka ndi wodalilika wotsimikizila kuti zolembedwa zake n’zolongosoka. Ndipo palibe katswili wa Baibulo woona mtima amene angakane kuti Baibulo imene tili nayo masiku ano mawu ake ni olongosoka.” Kuwonjezela apo, ponena za Malemba Aciheberi, katswili wina dzina lake William Henry Green anati: “Tingakambe motsimikiza kuti palibe zolemba zina zakale zimene uthenga wake unakopedwa mosamala kwambili kupambana Malemba Aciheberi.”
a Kuti mudziŵe zambili, onani Zakumapeto 1 ndi 2 mu Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika. Baibulo imeneyi ipezekanso pa Webusaiti ya www.jw.org.
-
-
Cifukwa Cake Baibulo YapulumukaNsanja ya Mlonda (Yogawila)—2016 | No. 4
-
-
NKHANI YA PACIKUTO | BAIBULO—MMENE YAPULUMUKILA
Cifukwa Cake Baibulo Yapulumuka
Baibulo yapulumuka zambili. Pa cifukwa cimeneci, masiku ano tili na mwai wokhala nayo ndi kuiŵelenga. Ngati mwasankha kuŵelenga Baibulo lomasulidwa bwino, mungatsimikizile kuti muŵelenga Malemba ogwilizana kwambili ndi zolemba zoyambilila.a Baibulo siinawole ngakhale kuti inalembedwa pa zinthu zosalimba, ndipo inatetezeka kwa anthu otsutsa ndi kwa omasulila amene anafuna kusintha uthenga wake. Kodi zimenezi zinatheka bwanji? Kodi buku limeneli lili ndi uthenga wabwanji kwenikweni?
“Tsopano nikhulupilila kuti Baibulo imene nili nayo ni mphatso yocokela kwa Mulungu”
Anthu ambili amene amaphunzila Baibulo afika pokamba mau amene mtumwi Paulo analemba akuti: “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Timoteyo 3:16) Iwo akhulupilila kuti Baibulo lapulumuka cifukwa ni Mau a Mulungu, ndi kuti Iye ndiye waiteteza kufikila masiku ano. Faizal amene takamba m’nkhani yoyambilila, anaganiza zophunzila Baibulo n’colinga cakuti adzionele yekha ngati n’locokeladi kwa Mulungu. Zimene anapeza ataiphunzila, zinam’cititsa cidwi. Posapita nthawi, iye anazindikila kuti ziphunzitso zambili zimene zili m’machechi osiyanasiyana si zipezeka m’Baibulo. Kuwonjezela apo, iye anakhudzidwa kwambili atadziŵa colinga ca Mulungu ca dziko lapansi cimene Mau Ake amakamba.
Iye anakambanso kuti: “Tsopano nikhulupilila kuti Baibulo imene nili nayo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Ngati Mulungu anapanga cilengedwe conse, iye sangalephele kutipatsa Baibulo ndi kuiteteza. Ndipo ngati ningaganize kuti Mulungu sangateteze Baibulo, zingakhale monga nikamba kuti Mulungu alibe mphamvu. Kumeneku kungakhale kukaikila Mulungu Wamphamvuyonse. Koma ndine ndani kuti nicite zimenezo?”—Yesaya 40:8.
a Onani nkhani imene ili mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2008, ya mutu wakuti: “Kodi Mungadziŵe Bwanji Baibulo Lomasulilidwa Bwino?
-