ZAKUMAPETO
Mgonelo wa Ambuye—Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu
AKRISTU amalamulidwa kucita mwambo wokumbukila imfa ya Yesu. Mwambo umenewu umachedwanso mgonelo wa Ambuye kapena “cakudya camadzulo ca Ambuye.” (1 Akorinto 11:20) Kodi n’cifukwa ciani mwambo umenewu uli wofunika kwambili? Kodi uyenela kucitika bwanji, ndipo liti?
Yesu Kristu ndiye anayambitsa mwambo umenewu usiku wa Pasika ya Ayuda m’caka ca 33 C.E. Mwambo wa Pasika unali cikondwelelo cimene cinali kungocitika kamodzi pacaka, patsiku la 14, mwezi wa Nisani malinga ndi kalendala yaciyuda. Cioneka kuti Ayuda pofuna kupeza tsiku limeneli, anali kuyembekezela tsiku limene limakhala ndi maola pafupi-fupi 12 masana ndi 12 usiku, mu March kapena mu April. Tsiku limene mwezi unali kutuluka, loyandikana kwambili ndi tsiku limene linali kukhala ndi maola 12 masana ndi 12 usiku, ndilo linali ciyambi ca mwezi wa Nisani. Mwambo wa Pasika unali kucitika pambuyo pa masiku 14, dzuŵa litaloŵa.
Pamene Yesu anatsiliza kucita mwambo wa Pasika pamodzi ndi atumwi ake, anacotsa Yudasi Isikariyoti, ndiyeno anayambitsa Mgonelo wa Ambuye. Mwambo umenewu unaloŵa m’malo mwa Pasika ya Ayuda imene inali kucitika kamodzi pacaka. Ndiye cifukwa cake mwambo wa Mgonelo wa Ambuye nawonso uyenela kucitika kamodzi caka ciliconse.
Uthenga Wabwino wa Mateyu umakamba kuti: “Yesu anatenga mkate, ndipo atapempha dalitso, anaunyema-nyema n’kuupeleka kwa ophunzila ake. Iye anati: ‘Eni, idyani. Mkate uwu ukuimila thupi langa.’ Kenako anatenga kapu ndipo atayamika, anaipeleka kwa io n’kunena kuti: ‘Imwani nonsenu. Vinyoyu akuimila “magazi anga a pangano,” amene adzakhetsedwa cifukwa ca anthu ambili kuti macimo akhululukidwe.’”—Mateyu 26:26-28.
Anthu ena amakhulupilila kuti Yesu anasandutsa mkate kukhala thupi lake leni-leni, ndi vinyo kukhala magazi ake eni-eni. Komabe, thupi la Yesu linali lathunthu pamene anali kupeleka mkate umenewu. Kodi m’ceni-ceni atumwi a Yesu anali kudya thupi ndi kumwa magazi ake eni-eni? Iyai, cifukwa kucita zimenezi kukanakhala kudya thupi la munthu kumene kunali kuphwanya lamulo la Mulungu. (Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:10) Malinga ndi lemba la Luka 22:20, Yesu anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa cifukwa ca inu.” Kodi kapu yeni-yeniyo ndi imene inakhala “pangano latsopano”? Zimenezi n’zosatheka, popeza pangano ni mgwilizano, osati cinthu cogwilika kapena cooneka ndi maso.
Conco, zonse ziŵili mkate ndi vinyo ndi zizindikilo cabe. Mkate umaimila thupi laungwilo la Kristu. Yesu anagwilitsila nchito mkate umene unatsala pa cakudya ca Pasika. Mkatewo unali wopanda cofufumitsa ciliconse. (Ekisodo 12:8) Baibo imagwilitsila nchito cofufumitsa monga cizindikilo ca ucimo kapena coipitsa. Conco, mkate umaimila thupi laungwilo la Yesu limene anapeleka. Linalibe ucimo uliwonse.—Mateyu 16:11, 12; 1 Akorinto 5:6, 7; 1 Petulo 2:22; 1 Yohane 2:1, 2.
Vinyo wofiila umaimila magazi a Yesu. Magazi amenewo amacititsa pangano latsopano kugwila nchito. Yesu anakamba kuti magazi ake anakhetsedwa kuti “macimo akhululukidwe.” Tsopano kunakhala kotheka kuti anthu angakhale oyela pamaso pa Mulungu, ndipo angaloŵe m’pangano latsopano ndi Yehova. (Aheberi 9:14; 10:16, 17) Pangano limeneli limatheketsa kuti Akristu okhulupilika okwana 144,000, apite kumwamba. Kumeneko adzatumikila monga mafumu ndi ansembe kuti mtundu wonse wa anthu ukadalitsidwe.—Genesis 22:18; Yeremiya 31:31-33; 1 Petulo 2:9; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-3.
Kodi ndani ayenela kudyako zizindikilo zimenezi? Ndi anthu cabe amene ali m’pangano latsopano, kutanthauza ao amene ali ndi ciyembekezo copita kumwamba. Anthu amenewa mzimu woyela wa Mulungu umawakhutilitsa maganizo ndi kuwatsimikizila mu mtima, kuti asankhidwa kukakhala mafumu kumwamba. (Aroma 8:16) Iwo alinso m’pangano la Ufumu ndi Yesu.—Luka 22:29.
Nanga bwanji za aja amene ciyembekezo cao n’codzakhala m’Paladaiso padziko lapansi kosatha? Iwo amatsatila lamulo la Yesu la kupezeka pa mwambo wa Mgonelo wa Ambuye. Koma amangokhala openyelela mwaulemu, osati kudyako. Mboni za Yehova zimacita mwambo wa Mgonelo wa Ambuye kamodzi pacaka pa Nisani 14, dzuŵa litaloŵa. Ngakhale kuti ni Akristu ocepa cabe amene ali ndi ciyembekezo copita kumwamba, mwambo umenewu ndi wofunika kwa Akristu onse. Imakhala nthawi imene onse amaganizila za cikondi cacikulu cimene Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu anacionetsa.—Yohane 3:16.