Lambilani Yehova, Mfumu Yamuyaya
“Kwa Mfumu yamuyaya, . . . kwa iyeyo kupite ulemu ndi ulemelelo mpaka muyaya.”—1 TIM. 1:17.
1, 2. (a) Kodi “Mfumu yamuyaya” ndani? Nanga n’cifukwa ciani dzina limeneli n’lomuyenelela? (Onani cithunzi-thunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Kodi ulamulilo wa Yehova umatipangitsa bwanji kumuyandikila?
MFUMU SOBHUZA II ya ku Swaziland inalamulila kwa zaka pafupi-fupi 61. Zinali zocititsa cidwi kuona kuti mfumu inalamulila zaka zambili conco m’zaka zathu zino. Ngakhale kuti Mfumu Sobhuza inalamulila zaka zambili conco, pali mfumu ina imene ulamulilo wake sudzatha cifukwa cakuti iyo sidzafa. Baibo imacha mfumu imeneyo kuti “Mfumu yamuyaya.” (1 Tim. 1:17) Wamasalimo anachula dzina la Wolamulila ameneyu pamene analengeza kuti: “Yehova ndi Mfumu mpaka kale-kale, ndithu mpaka muyaya.”—Sal. 10:16.
2 Mulungu wakhala akulamulila monga mfumu kwa zaka zambili kuposa munthu wina aliyense. Komabe, njila imene Yehova amalamulila anthu ndi imene imatipangitsa kumuyandikila. Mfumu ina imene inalamulila Aisiraeli kwa zaka 40 inatamanda Mulungu ndi mau akuti: “Yehova ndi wacifundo ndi wacisomo, Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha. Yehova wakhazikitsa mpando wake wacifumu kumwamba. Ndipo ufumu wake ukulamulila ciliconse.” (Sal. 103:8, 19) Yehova ndi Mfumu yathu komanso Atate wathu wacikondi wakumwamba. Mfundo imeneyi ikudzutsa mafunso aŵili awa: Kodi Yehova ndi Atate wathu motani? Kodi Yehova wakhala akulamulila motani anthu kucokela pa kupanduka kwa m’munda wa Edeni? Mayankho a mafunso awa angatithandize kuyandikila kwambili Yehova ndi kumulambila ndi mtima wathu wonse.
MFUMU YAMUYAYA INALENGA ANGELO NDI ANTHU
3. Kodi ndani amene anali mwana woyamba kulengedwa ndi Yehova? Nanga ndani ena amene analengedwa monga “ana” a Mulungu?
3 Yehova anasangalala kwambili pamene analenga Mwana wake wobadwa yekha. Mulungu sanali kuona mwana wake woyamba kubadwa monga wopanda pake. M’malomwake, Mulungu anali kukonda kwambili Mwana wake ndipo anagwila naye nchito yosangalatsa yolenga angelo angwilo mamiliyoni ambili. (Akol. 1:15-17) Baibo imakamba kuti angelo amenewa amatumikila Mulungu mwacimwemwe monga “atumiki ake . . . ocita cifunilo cake.” Iye amawalemekeza mwa kuwacha kuti “ana” ake. Iwo ali mbali ya banja la Yehova.—Sal. 103:20-22; Yobu 38:7.
4. Kodi anthu anakhala bwanji mbali ya banja la Mulungu?
4 Pambuyo polenga kumwamba ndi dziko lapansi, Yehova anapanga zolengedwa zina zimene zinadzakhala mbali ya banja lake. Atalenga dziko lapansi lokongola, iye analenganso munthu woyamba, Adamu, m’cifanizilo cake. (Gen. 1:26-28) Adamu anafunika kugonjela Yehova monga Mlengi wake. Pokhala Tate, Yehova mwacikondi ndiponso mokoma mtima, anawapatsa malangizo omveka bwino. Malangizo amenewo sanawalande ufulu mwanjila ina iliyonse.—Ŵelengani Genesis 2:15-17.
5. Kodi Mulungu anapanga makonzedwe otani kuti dziko lapansi lidzaze ndi ana ake aumunthu?
5 Mosiyana ndi mafumu ambili aumunthu, Yehova amaona atumiki ake kukhala banja lake. Amawakhulupilila kwambili ndipo amasangalala kuwapatsa ulamulilo ndi maudindo osiyana-siyana. Mwacitsanzo, Mulungu anapatsa Adamu ulamulilo pa zamoyo zonse ndiponso nchito yaikulu koma yosangalatsa yakuti ache maina zinyama zonse. (Gen. 1:26; 2:19, 20) Mulungu sanalenge anthu angwilo mamiliyoni ambili kuti adzaze dziko lapansi. M’malomwake, iye analenga mkazi wangwilo, Hava, kuti akhale mthandizi wa Adamu. (Gen. 2:21, 22) Ndiyeno Mulungu anapatsa banja limeneli mwai wodzaza dziko lapansi ndi ana ao. Pansi pa mikhalidwe yabwino, anthu anafunikila kufutukula Paladaiso mpaka dziko lonse lapansi. Monga banja la Mulungu, io anafunikila kulambila Yehova kosatha pamodzi ndi angelo. Iwo anali ndi ciyembekezo cabwino kwambili. Mwa njila imeneyi, Yehova anasonyeza kuti anali kukonda kwambili Adamu ndi Hava.
ANA OPANDUKA ANAKANA ULAMULILO WA MULUNGU
6. (a) Kodi zinacitika bwanji kuti ena apanduke m’banja la Mulungu? (b) Kodi kupanduka kunaonetsa kuti Yehova walephela kulamulila anthu? Fotokozani.
6 N’zomvetsa cisoni kuti Adamu ndi Hava sanafune kuti Yehova aziwalamulila. Iwo anasankha kutsatila Satana, mwana wopanduka wauzimu wa Mulungu. (Gen. 3:1-6) Cifukwa cakuti anakana ulamulilo wa Mulungu, io anavutika ndipo anafa. Ana ao akhalanso akuvutika ndipo amafa. (Gen. 3:16-19; Aroma 5:12) Pamene anthu oyamba anacimwa, padziko lapansi panalibe amene anali kugonjela Mulungu. Koma kodi zimenezi zinasonyeza kuti Mulungu walephela kulamulila anthu padziko lapansi? Kutalitali. Iye anasonyeza ulamulilo wake pamene anathamangitsila mwamuna ndi mkazi woyamba kunja kwa munda wa Edeni, ndipo anaonetsetsa kuti io asabwelelenso m’mundamo mwa kuika akelubi pacipata ca mundawo. (Gen. 3:23, 24) Panthawi imodzi-modziyo, Mulungu anaonetsa cikondi cake monga tate mwa kutsimikizila kuti cifunilo cake cidzakwanilitsika. Cifunilo cimeneco n’cakuti akhale ndi banja la ana akuuzimu ndi aumunthu odzipeleka kwa iye. Iye analonjeza kuti padzakhala “mbeu” imene idzaononga Satana ndi kucotsa mavuto amene amabwela cifukwa ca ucimo wa Adamu.—Ŵelengani Genesis 3:15.
7, 8. (a) Kodi makhalidwe a anthu anaipa motani m’nthawi ya Nowa? (b) Kodi Yehova anapanga makonzedwe otani kuti ayeletse dziko lapansi ndi kuteteza anthu?
7 Pambuyo pa zaka zambili, anthu ena anasankha kukhala okhulupilika kwa Yehova. Abele ndi Enoki ndi ena mwa anthu amenewo. Koma anthu ambili anakana Yehova kuti akhale Atate wao ndi Mfumu yao. Pofika nthawi ya Nowa, dziko lapansi “linadzaza ndi ciwawa.” (Gen. 6:11) Kodi zimenezi zinasonyeza kuti Yehova walephela kulamulila zocitika za padziko lapansi? Kodi Baibo imati ciani pankhani imeneyi?
8 Taganizilani nkhani ya Nowa. Yehova anapatsa Nowa mapulani ndi malangizo a kamangidwe ka cingalawa cacikulu kuti iye ndi anthu a m’banja lake adzapulumukilemo. Mulungu anaonetsanso cikondi cake cacikulu kwa mtundu wonse wa anthu pamene analamula Nowa kukhala “mlaliki wa cilungamo.” (2 Pet. 2:5) Mosakaikila, uthenga wa Nowa unaphatikizapo kuuza anthu kuti alape ndi kuwacenjeza za cionongeko cimene cinali kubwela. Koma anthuwo sanamvele. Kwa zaka zambili, Nowa ndi banja lake anali kukhala pakati pa anthu aciwawa ndi okonda kwambili ciwelewele. Monga Atate wacikondi, Yehova anateteza ndi kudalitsa anthu 8 okhulupilikawo. Pamene Yehova anabweletsa Cigumula padziko lapansi, iye anaonetsa mphamvu zake pa anthu opandukawo ndi angelo oipa. Ndithudi, Yehova analidi kulamulila.—Gen. 7:17-24.
ULAMULILO WA YEHOVA PAMBUYO PA CIGUMULA
9. Kodi Yehova anapatsa anthu mwai wotani pambuyo pa Cigumula?
9 N’zoonekelatu kuti pamene Nowa ndi banja lake anatuluka m’cingalawa anayamikila Yehova kwambili cifukwa cowasamalila ndi kuwateteza. Mwamsanga, Nowa anamanga guwa lansembe ndi kupeleka nsembe kwa Yehova. Mulungu anadalitsa Nowa ndi banja lake ndipo anawalamula kuti: “Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi.” (Gen. 8:20–9:1) Anthu analinso ndi mwai wolambila Mulungu mogwilizana ndi kudzaza dziko lapansi.
10. (a) Pambuyo pa Cigumula, kodi n’kuti kumene anthu anayambila kupandukila Yehova? Nanga anacita bwanji zimenezo? (b) Kodi Yehova anacita ciani kuti akwanilitse cifunilo cake?
10 Komabe, Cigumula sicinacotse kupanda ungwilo, ndipo anthu anali kuvutikabe cifukwa ca cisonkhezelo ca Satana ndi angelo opanduka. Pasanapite nthawi yaitali, anthu anayambanso kupandukila ulamulilo wabwino wa Yehova. Mwacitsanzo, mdzukulu wa Nowa, Nimurodi, anatsutsa kwambili ulamulilo wa Yehova. Nimurodi anali “mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.” Iye anamanga mizinda ikulu-ikulu monga wa Babele ndi kudziika kukhala mfumu “m’dziko la Sinara.” (Gen. 10:8-12) Kodi Mfumu yamuyaya inacita ciani ndi mfumu yopandukayo imene inali kufuna kulepheletsa colinga ca Mulungu cakuti anthu ‘adzaze dziko lapansi’? Mulungu anasokoneza cilankhulo ca anthu ndipo anthu amene anali kucilikiza Nimurodi anabalalika “padziko lonse lapansi.” Kulikonse kumene anthuwo anapita, anali kulambila milungu yao yonama ndi kudzilamulila okha.—Gen. 11:1-9.
11. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupilika kwa bwenzi lake Abulahamu?
11 Ngakhale kuti anthu ambili anali kulambila milungu yonama pambuyo pa Cigumula, anthu ena okhulupilika anapitilizabe kulambila Yehova. Abulahamu anali mmodzi wa anthu okhulupilika amenewo. Iye anamvela Mulungu ndi kusiya cuma cake ndi umoyo wabwino mumzinda wa Uri ndi kukhala m’mahema kwa zaka zambili. (Gen. 11:31; Aheb. 11:8, 9) Abulahamu sanali kukhulupilila kuti angatetezedwe ndi mafumu aumunthu kapena mizinda yamipanda. M’malomwake, iye anali kukhulupilila kuti Yehova ndi amene adzamuteteza pamodzi ndi banja lake. Posonyeza kuti Yehova amateteza mwacikondi, wamasalimo anati: “Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awacitile zacinyengo, koma anadzudzula mafumu cifukwa ca io.” (Sal. 105:13, 14) Yehova anali wokhulupilika kwa bwenzi lake Abulahamu, ndipo anam’lonjeza kuti: “Mwa iwe mudzatuluka . . . mafumu.”—Gen. 17:6; Yak. 2:23.
12. Kodi Yehova anaonetsa bwanji ulamulilo wake ku Iguputo? Nanga zimenezo zinakhudza bwanji anthu ake osankhika?
12 Mulungu analonjeza mwana wa Abulahamu, Isaki ndi mdzukulu wake, Yakobo kuti adzawadalitsa ndi kuti m’banja lao mudzatuluka mafumu. (Gen. 26:3-5; 35:11) Koma izi zisanacitike, mbadwa za Yakobo zinakhala akapolo ku Iguputo. Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Yehova sadzakwanilitsa lonjezo lake ndi kuti walephela kulamulila anthu padziko lapansi? Ai ndithu. Patapita nthawi, Yehova anaonetsa mphamvu zake ndi ulamulilo wake pa Farao wouma khosi. Aisiraeli amene anali akapolo anakhulupilila Yehova ndipo iye anawapulumutsa modabwitsa pa Nyanja Yofiila. Yehova anaonetsa kuti ndi Mfumu ya Cilengedwe Conse, ndipo monga Tate wacikondi, anagwilitsila nchito mphamvu zake kuteteza anthu ake.—Ŵelengani Ekisodo 14:13, 14.
YEHOVA ANAKHALA MFUMU YA AISIRAELI
13, 14. (a) M’nyimbo imene Aisiraeli anaimba, kodi analengeza ciani ponena za ulamulilo wa Yehova? (b) Kodi ndi lonjezo lotani lokhudza ufumu limene Mulungu analonjeza Davide?
13 Aisiraeli anaimba nyimbo yacilakiko yotamanda Yehova pambuyo pakuti alanditsidwa mozizwitsa muukapolo ku Iguputo. Nyimbo imeneyi, imapezeka pa lemba la Ekisodo caputala 15, ndipo pa vesi 18 pamati: “Yehova adzalamulila monga mfumu mpaka kale-kale. Adzalamulila mpaka muyaya.” Zoonadi, Yehova anakhala Mfumu pa mtundu watsopanowo. (Deut. 33:5) Koma anthu sanakhutile ndi ulamulilo wa Yehova amene anali Mfumu yao yosaoneka. Pambuyo pa zaka pafupi-fupi 400 Aisiraeli atatuluka mu Iguputo, io anapempha Mulungu kuti awapatse mfumu yaumunthu potengela mitundu ina. (1 Sam. 8:5) Ngakhale zinali conco, Yehova ndi amene anali Mfumu yao ndipo mfundo imeneyi inaonekela bwino pamene Davide, mfumu yaciŵili ya Isiraeli anali kulamulila.
14 Davide anabweletsa likasa lopatulika la pangano ku Yerusalemu. Pa cocitika capadela cimeneci, Alevi anaimba nyimbo yacitamando imene mbali yake ina timaiŵelenga pa 1 Mbiri 16:31, pamene pamati: “Anene pakati pa anthu a mitundu ina kuti: ‘Yehova wakhala mfumu!’” Koma mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi Yehova anakhala bwanji mfumu panthawiyo popeza kuti iye ndi Mfumu yamuyaya?’ Yehova amakhala Mfumu mwa kucita zinthu zoonetsa kuti ali ndi ulamulilo kapena kugwilitsila nchito munthu wina kuti amuimile pocita zofuna zake. Kudziŵa mmene Yehova amakhalila mfumu n’kofunika kwambili. Davide asanafe, Yehova anam’lonjeza kuti ufumu wake udzakhala kosatha. Mulungu anati: “Ndidzautsa mbeu yako yobwela pambuyo pako, imene idzatuluka m’ciuno mwako. Ndipo ndidzakhazikitsadi ufumu wake.” (2 Sam. 7:12, 13) Pambuyo pa zaka zoposa 1,000, lonjezo limeneli linakwanilitsidwa pamene “mbeu” kapena kuti mwana wa Davide anaonekela. Kodi mwana ameneyu anali ndani ndipo ndi liti pamene anakhala Mfumu?
YEHOVA ANASANKHA MFUMU YATSOPANO
15, 16. Kodi Yesu anadzozedwa liti monga Mfumu yamtsogolo? Pamene Yesu anali padziko lapansi, kodi anapanga makonzedwe otani okhudza ulamulilo wake?
15 M’caka ca 29 C.E., Yohane Mbatizi anayamba kulalikila kuti “Ufumu wakumwamba wayandikila.” (Mat. 3:2) Pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane, Yehova anadzoza Yesu kukhala Mesiya wolonjezedwa ndiponso Mfumu ya Ufumu wa Mulungu yamtsogolo. Monga tate, Yehova anaonetsa kuti amakonda Yesu pamene anati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.”—Mat. 3:17.
16 Pa utumiki wake wonse, Yesu anali kulemekeza Atate wake. (Yoh. 17:4) Anacita zimenezi mwa kulalikila za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43) Iye anaphunzitsanso otsatila ake kuti azipemphela kuti Ufumuwo ubwele. (Mat. 6:10) Monga Mfumu yosankhidwilatu, Yesu anauza anthu amene anali kumutsutsa kuti: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” (Luka 17:21) Usiku wakuti maŵa Yesu aphedwa, iye anapanga “pangano la ufumu” ndi otsatila ake. Mwakutelo, iye anapatsa ophunzila ake ena okhulupilika mwai wodzalamulila naye monga mafumu mu Ufumu wa Mulungu.—Ŵelengani Luka 22:28-30.
17. Kodi Yesu anayamba kulamulila mu 33 C.E m’njila yotani? Koma kodi anafunikila kuyembekezela ciani?
17 Kodi Yesu anafunikila kuyamba liti kulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu? Iye sanayambe kulamulila nthawi imeneyo atapanga pangano la Ufumu ndi ophunzila ake. Zili conco cifukwa cakuti m’masana a tsiku lotsatila, Yesu anaphedwa ndipo otsatila ake anabalalika. (Yoh. 16:32) Komabe Yehova anali kulamulilabe monga mmene anali kucitila m’nthawi yakale. Pa tsiku lacitatu, iye anaukitsa Mwana wake, ndipo pa tsiku la Pentecosite wa mu 33 C.E.,Yesu anakhazikitsa ufumu wauzimu pa mpingo wacikristu wa abale ake odzozedwa. (Akol. 1:13) Ngakhale zinali conco, Yesu monga “mbeu” yolonjezedwa, anafunika kuyembekezela kuti apatsidwe mphamvu zolamulila dziko lapansi. Yehova anauza Mwana wake kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikila nditaika adani ako monga copondapo mapazi ako.”—Sal. 110:1.
LAMBILANI MFUMU YAMUYAYA
18, 19. Kodi kudziŵa kuti Yehova ndi mfumu yamuyaya kuyenela kutipangitsa kucita ciani? Nanga tidzaphunzila ciani m’nkhani yotsatila?
18 Kwa zaka zambili, ulamulilo wa Yehova unatsutsidwa kumwamba ndi padziko lapansi. Koma Yehova sanaleke kulamulila. Monga Atate wacikondi, iye anateteza ndi kusamalila anthu ake okhulupilika monga Nowa, Abulahamu ndi Davide. Kodi kudziŵa zimenezi sikuyenela kutipangitsa kugonjela ndi kuyandikila Mfumu yathu?
19 Koma tingafunse kuti: Kodi Yehova wakhala bwanji Mfumu masiku ano? Kodi tingaonetse bwanji kuti ndife nzika zokhulupilika za Ufumu wa Yehova ndi kukhala m’banja lake la ana angwilo? Nanga timatanthauza ciani tikamapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele? Mafunso amenewa adzayankhidwa m’nkhani yotsatila.