Kulamanzele: Mlongo ku Alabama, m’dziko la U.S.A., akumvetsela nkhani ya M’bale Rutherford imene inajambulidwa pa tepi ca kumapeto kwa zaka za m’ma 1930; kulamanja: ku Switzerland
CIGAWO 1
Coonadi ca Ufumu—Kugaŵila Cakudya ca Kuuzimu
YELEKEZELANI kuti mukuphunzila Baibulo ndi wophunzila Baibulo wanu. Nkhope yake ikuoneka yacimwemwe cifukwa cakuti wamvetsetsa mfundo ya palemba limene mwaŵelenga naye. Motsitsa mau, wophunzilayo akufunsa kuti, “Kodi mukutanthauza kuti Baibulo limaphunzitsa kuti tingakhale m’Paladaiso kwamuyaya pano padziko lapansi?” Mnzanu amene muli naye muutumiki akumwetulila ndi kuyankha kuti, “Izi n’zimene Baibulo limaphunzitsa.” Kenako wophunzilayo akugwedeza mutu, ndipo modabwa akunena kuti, “Izi n’zocititsa cidwi kwambili, ndipo sindinaphunzilepo zimenezi.” Ndiyeno inu mukukumbukila kuti milungu ingapo yapita, iye anakamba mau ofanana ndi amenewa pamene anadziŵa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.
Kodi zotelezi zinakucitikilamponi? Atumiki ambili a Mulungu zinawacitikilapo. Zocitika zotele zimatikumbutsa za mphatso ya mtengo wapatali imene tinapatsidwa. Mphatso imeneyi ndi coonadi cimene tinaphunzila. Komabe, kodi zinatheka bwanji kuti inuyo muphunzile coonadi cimeneci? M’cigawo cino tiphunzila yankho la funso limeneli. Njila imene anthu a Mulungu aphunzilila coonadi ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni. Kwa zaka zambili, Mfumu ya Ufumuwu, Yesu Kristu, yakhala ikuthandiza anthu a Mulungu kuphunzila coonadi.