NKHANI 12
Mmene Mungakhalile Bwenzi La Mulungu
1, 2. Kodi ena a mabwenzi a Mulungu anali ndani?
KODI mungasankhe munthu wabwanji kuti akhale bwenzi lanu? Mosakaikila, mungasankhe munthu amene mumakonda, amene mumamvelana naye, wokoma mtima, ndiponso wa makhalidwe amene mumakonda.
2 Yehova Mulungu nayenso amasankha anthu ena kukhala mabwenzi ake. Mwacitsanzo, Abulahamu anali bwenzi la Mulungu. (Yesaya 41:8; Yakobo 2:23) Yehova anali kukondanso Davide. Ndipo anati Davide anali ‘munthu wa pamtima pake.’ (Machitidwe 13:22) Mneneli Danieli nayenso anali “munthu wokondedwa kwambili” ndi Yehova.—Danieli 9:23.
3. Kodi Abulahamu, Davide, ndi Danieli anakhala bwanji mabwenzi a Yehova?
3 Kodi Abulahamu, Davide, ndi Danieli anakhala bwanji mabwenzi a Yehova? Yehova anauza Abulahamu kuti: “Wamvela mau anga.” (Genesis 22:18) Yehova amakhala bwenzi kwa anthu amene amadzicepetsa ndi kumumvela. Ngakhale mtundu wonse wa anthu ungakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Mwacitsanzo, Yehova anauza mtundu wa Aisiraeli kuti: “Muzimvela mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.” (Yeremiya 7:23) Conco, ngati inunso mufuna kukhala bwenzi la Yehova, mufunika kukhala womvela kwa iye.
YEHOVA AMACINJILIZA MABWENZI AKE
4, 5. Kodi Yehova amawacinjiliza bwanji mabwenzi ake?
4 Baibulo imakamba kuti Yehova nthawi zonse amafuna njila zoonetsela “mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Pa Salimo 32:8, Yehova amalonjeza mabwenzi ake kuti: “Ndidzakupatsa nzelu ndi kukulangiza njila yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anila.”
5 Koma pali mdani wina wamphamvu amene nthawi zonse amafuna kuwononga ubwenzi wathu ndi Mulungu. Komabe, Yehova amafuna kuticinjiliza kwa mdani ameneyu. (Ŵelengani Salimo 55:22.) Cifukwa ndife mabwenzi a Yehova, timam’tumikila ndi mtima wathu wonse. Timakhalabe okhulupilika kwa iye ngakhale tikumane ndi mavuto abwanji. Tili ndi cikhulupililo monga ca wamasalimo, amene anati za Yehova: “Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Salimo 16:8; 63:8) Kodi Satana amacita ciani kuti asokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova?
CINENEZO CA SATANA
6. Kodi Satana amati ciani pa nkhani ya anthu kutumikila Mulungu?
6 M’Nkhani 11 tinaphunzila kuti Satana anatsutsa Yehova, ndi kum’neneza kuti Iye ni wabodza ndipo si wacilungamo. Anati alibe cilungamo cifukwa cosalola Adamu ndi Hava kumadzigamulila okha cabwino ndi coipa. Tikaŵelenga mu Baibulo m’buku ya Yobu, timaona kuti Satana amakaikila anthu onse amene afuna kukhala mabwenzi a Mulungu. Satana amakamba kuti cimene anthu amatumikilila Mulungu si cifukwa comukonda iyai, koma cifukwa ca zabwino zimene angapeze kwa Iye. Ndipo Satana amacita kudzithemba kuti akhoza kupandutsa aliyense kwa Mulungu. Koma tiyeni tione mmene Yehova anacinjilizila Yobu, ndi phunzilo limene tingatengepo.
7, 8. (a) Kodi kwa Yehova, Yobu anali munthu wabwanji? (b) Koma Satana anakamba ciani za Yobu?
7 Kodi Yobu anali ndani? Anali munthu wabwino amene anakhalako zaka ngati 3,600 kumbuyoku. Ndipo Yehova anakamba kuti panthawiyo, pa dziko lapansi panalibe munthu wina wofanana ndi Yobu. Anali munthu woopa Mulungu, ndipo anali kupewa zoipa. (Yobu 1:8) Zoona, Yobu anali bwenzi la Yehova la pamtima.
8 Koma nthota za Satana zinam’cititsa kukamba kuti Yobu anali kutumikila Mulungu pa zifukwa zadyela. Satana anauza Yehova kuti: “Kodi inuyo simwam’hinga iyeyo? Mwachingilanso nyumba yake ndi ciliconse cimene ali naco. Mwadalitsa nchito ya manja ake ndipo ziŵeto zake zaculuka kwambili padziko lapansi. Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa.”—Yobu 1:10, 11.
9. Kodi Yehova analola Satana kucitanji?
9 Satana ananeneza Yobu kuti anali kutumikila Yehova cabe cifukwa ca zabwino zimene anali kufuna kwa Iye. Anafika mpaka podzithemba kuti akhoza kupangitsa Yobu kuleka kutumikila Yehova. Koma Yehova anadziŵa kuti Satana angokamba za m’mutu mwake. Ndiye pofuna kum’tsiliza nthota, Yehova analola Satana kuti amuyese Yobu, aone ngati sanali kukondadi Mulungu.
SATANA AYESA YOBU
10. Kodi Satana anamuyesa bwanji Yobu? Kodi Yobu anagonja?
10 Coyambilila, Satana anawononga ziweto zonse za Yobu. Kucoka apo, Satana anapha anchito ambili a Yobu, kumusiya alibiletu kalikonse! Koma Satana anabwelanso mwa nkhalwe, ndi kupha ana onse 10 a Yobu ndi cimphepo. Koma Yobu anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova. “M’zonsezi Yobu sanacimwe, kapena kunena kuti Mulungu wacita zosayenela.”—Yobu 1:12-19, 22.
Yehova anadalitsa Yobu cifukwa cokhala bwenzi lake lokhulupilika
11. (a) Kodi Satana anacitanso ciani cina kwa Yobu? (b) Kodi apa lomba Yobu anagonja?
11 Satana sanalekele pamenepo. Anauza Mulungu kuti: ‘Khudzani mnofu wake mpaka fupa lake, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa.’ Conco Satana anadwalitsa Yobu matenda ozunza kwambili. (Yobu 2:5, 7) Koma Yobu anapitiliza kukhulupilika kwa Yehova. Iye anati: “Mpaka ine kumwalila, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—Yobu 27:5.
12. Kodi Yobu anaonetsa bwanji kuti Satana ni wabodza?
12 Cocititsa cidwi n’cakuti, Yobu sanadziŵepo kanthu za cinenezo ca Satana. Sanadziŵenso kuti n’cifukwa ciani anali kuvutika conco. Anali kungoganiza kuti mavuto ake onse anali kucokela kwa Yehova. (Yobu 6:4; 16:11-14) Ngakhale n’telo, Yobu anakhalabe nga nga nga! kwa Yehova. Apa lomba panalibe kukaika ngakhale pang’ono. Yobu analibe dyela. Sanali kutumikila Mulungu cifukwa ca dyela. Anali bwenzi la Mulungu cifukwa cokonda Mulungu. Bodza la Satana linaonekela poyela ndi nthota zake.
13. Kodi kukhulupilika kwa Yobu kunakhala ndi cotulukapo canji cabwino?
13 Yobu sanadziŵe zimene zinali kucitika kumwamba. Ngakhale ni conco, anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu. Mwa ici, anaonetsa kuti Satana ni woipa. Ndipo Yehova anadalitsa Yobu cifukwa cokhala bwenzi lake lokhulupilika.—Yobu 42:12-17.
CINENEZO CA SATANA LOMBA CILI PA IFE
14, 15. Kodi Satana amati ciani za ife tonse anthu?
14 Tingatengepo maphunzilo ofunika pa zimene zinacitika kwa Yobu. Lelo lino, Satana amaneneza ife kuti timatumikila Yehova cabe cifukwa ca zabwino zimene tingapeze kwa Iye. Pa Yobu 2:4, Satana anakamba kuti: “Munthu angalolele kupeleka ciliconse cimene ali naco kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4) Mwa kukamba conco, Satana anatanthauza kuti Yobu, kuphatikizapo anthu onse ni adyela. Ngakhale kuti papita zaka mahandiledi kucokela pamene Yobu anafa, Satana sanaleke kutonza Yehova ndi kuneneza atumiki ake. Mwacitsanzo, pa Miyambo 27:11, timaŵelenga kuti: “Mwana wanga, khala wanzelu ndi kukondweletsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”
15 Ngakhale inu mungasankhe kukhala womvela kwa Yehova, ndi kukhala bwenzi lake lokhulupilika. Pamenepo, mudzaonetsa kuti Satana ni wabodza. Mwina mungafunikile kusintha zinthu zina zikulu-zikulu mu umoyo wanu kuti mukhale bwenzi la Mulungu. Koma dziŵani kuti kucita zimenezo ndiye cinthu cofunika kupambana zonse. Imeneyi ni nkhani ikulu kwambili. Satana akuti inu simungakhulupilike kwa Mulungu mukakumana ndi mavuto. Amafuna kutipusitsa kuti tileke kukhulupilila Mulungu. Kodi amacita bwanji zimenezi?
16. (a) Ni macenjela anji amene Satana amaseŵenzetsa kuti alepheletse anthu kutumikila Yehova? (b) Nanga kwa inu, n’ciani cimene Mdyelekezi angacite kuti musatumikile Yehova?
16 Satana amayesa-yesa njila zambili kuti tilephele kukhala mabwenzi a Mulungu. Amatiukila “ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) Osadabwa ngati mabwenzi anu, acibanja, ndi anthu ena ayesa kukuletsani kuphunzila Baibulo ndi kucita zinthu zina zabwino. Ndipo zingamveke monga akuukilani.a (Yohane 15:19, 20) Nthawi zinanso, Satana amadzipanga kukhala monga “mngelo wa kuwala.” Cakuti angaoneke monga atithandiza, pamene atipusitsa kuti tilakwile Yehova. (2 Akorinto 11:14) Macenjela ena amene Satana amabwela nawo, ni kupangitsa munthu kumvela kuti mulimonse mmene angacitile zinthu, Mulungu sangamukonde. Ici cingapangitse munthu kungoleka zotumikila Mulungu.—Miyambo 24:10.
MVELANI MALAMULO A YEHOVA
17. N’cifukwa ciani tiyenela kumvela Yehova?
17 Ngati timvela malamulo a Yehova, timaonetsa kuti Satana ni wabodza. Kodi cofunika n’ciani kuti tikhale omvela? Baibulo imakamba kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.” (Deuteronomo 6:5) Timamvela Yehova cifukwa timam’konda. Ndipo pamene cikondi cathu pa Yehova cikulila-kulila, timakhala ofunitsitsa kucita ciliconse cimene iye atiuza. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yohane 5:3.
18, 19. (a) Chulani zina mwa zinthu zimene Yehova amatiuza kuti ni zoipa. (b) Timadziŵa bwanji kuti Yehova sangatipemphe kucita zimene sitingakwanitse?
18 Kodi ni zinthu ziti zimene Yehova amatiuza kuti ni zoipa? Onani zina pa danga lakuti “Muzizonda Zimene Yehova Amazonda.” Mudzapezapo zina mwa zinthu zimenezo. Pa zinthu zimenezi, mwina pali zina zimene simunaziganizilepo kuti n’zoipa. Koma mukaŵelenga m’Baibulo ndi kuganizilapo bwino, mudzaona kuti kumvela malamulo a Yehova ni cinthu canzelu. Ndipo mungaonenso kuti mufunikila kusintha zinthu zina mu umoyo wanu. N’zoona kuti cingakhale covuta kucita zimenezo, koma mukasintha, mudzapeza mtendele wa mu mtima ndi maganizo cifukwa cokhala bwenzi lokhulupilika la Mulungu. (Yesaya 48:17, 18) Koma kodi n’zoona kuti mungakwanitse kusintha?
19 Dziŵani kuti Yehova sangatiuze kucita zimene sitingakwanitse. (Deuteronomo 30:11-14) Popeza kuti Iye ni bwenzi lathu la pamtima, amatidziŵa bwino kupambana mmene timadzidziŵila ife eni ŵake. Amadziŵa bwino zimene tingakwanitse ndi zimene sitingakwanitse. (Salimo 103:14) Mtumwi Paulo anakamba kuti: “Mulungu ndi wokhulupilika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile, koma pamene mukukumana ndi mayeselowo iye adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.” (1 Akorinto 10:13) Tiyenela kukhala ndi cidalilo conse cakuti Yehova adzapitiliza kutipatsa mphamvu kuti tizikwanitsa kucita zabwino. Ngakhale inu, adzakupatsani “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti mupilile kapena kugonjetsa zovuta. (2 Akorinto 4:7) Pamene anathandizidwa ndi Yehova pa nthawi yovuta, Paulo anakamba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kucokela kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.
MUZIKONDA ZIMENE YEHOVA AMAKONDA
20. Ni makhalidwe ati amene muyenela kutengelako? Nanga n’cifukwa ninji?
20 Ngati tifuna kukhala bwenzi la Yehova, tiyenela kuleka zimene iye amatiuza kuti ni zoipa. Koma palinso zinthu zina zofunikila. (Aroma 12:9) Mabwenzi a Mulungu ayenela kukonda zimene Mulungu amakonda. Lemba la Salimo 15:1-5 (Ŵelengani) limafotokoza bwino mabwenzi a Mulungu. Iwo amatengelako makhalidwe ake, ndipo amaonetsa “cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, kufatsa ndi kudziletsa.”—Agalatiya 5:22, 23.
21. Mungacite ciani kuti mukhale ndi makhalidwe amene Mulungu amakonda?
21 Mungacite ciani kuti mukhale ndi makhalidwe abwino amenewa? Mufunika kudziŵa zimene Yehova amakonda mwa kuŵelenga ndi kuphunzila Baibulo nthawi zonse. (Yesaya 30:20, 21) Mwa kucita zimenezi, cikondi canu pa Yehova cidzakula, ndipo mudzakhala wofunitsitsa kumumvela.
22. Kodi padzakhala cotulukapo canji cabwino mukasankha kumvela Yehova?
22 Mungafunikile kusintha umoyo wanu monga mmene munthu amavulila zovala zakuda ndi kuvala zoyela. Baibulo imakamba kuti muyenela ‘kuvula umunthu wakale’ ndi kuvala “umunthu watsopano.” (Akolose 3:9, 10) Ngakhale kuti kusintha kungakhale kovuta, tikasintha ndi kumvela Yehova, iye adzatipatsa “mphoto yaikulu.” (Salimo 19:11) Conco, sankhani kumvela Yehova ndi kuonetsa kuti Satana ni wabodza. Tumikilani Yehova, osati cifukwa congofuna madalitso a mtsogolo iyai, koma cifukwa comukonda. Mukacita zimenezi, mudzakhala bwenzi la Mulungu la pamtima.
a Pano sititanthauza kuti Satana ndiye amangena mwa anthu amene amayesa kukuletsani kuphunzila Baibulo, iyai. Koma mfundo yake ni yakuti, Satana ni “mulungu wa nthawi ino,” ndipo ‘dziko lonse lili m’manja mwake.’ Conco tisadabwe ngati anthu ena ayesa kutilepheletsa kutumikila Yehova.—2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19.