LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • kr nkhani 220-221
  • Malonjezo a Ufumu—Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malonjezo a Ufumu—Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Nkhani Zofanana
  • Ufumu Ukwanilitsa Cifunilo ca Mulungu Padziko Lapansi
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • Yehova Amakwanilitsa Malonjezo Ake Nthawi Zonse
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
kr nkhani 220-221
1. Mlongo wacitsikana akulila amai ake amene amwalila kumene, ndipo waima kumbali kwa bedi; 2. Mlongo mmodzi modziyo akolola ma apulo ndi amai ake amene aukitsidwa ndipo aoneka acitsikana ndi athanzi

Kodi mumalakalaka kuona malonjezo a Ufumu akukwanilitsidwa?

CIGAWO 7

Malonjezo a Ufumu—Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano

TAYELEKEZELANI kuti mwathyola apulo lalikulu lakupsa mu mtengo. Musanaliike m’basiketi mmene muli kale ma apulo ena ambili, mukuinunkhiza ndi kumva kafungo kake kokoma. Mwakhala mukugwila nchitoyi kwa maola ambili, koma simukutopa ndipo mukufuna kupitilizabe kugwila nchito imeneyi. Mukuona amai anu amene ali pamtengo wina umene uli capafupi. Iwo akugwila nchito yokolola mosangalala ndipo akuceza ndi anthu ena a m’banja lanu ndi anzanu amene akuwathandiza nchitoyo. Amai anu akuoneka acitsikana monga mmene anali kuonekela zaka zambili zapitazo pamene inu munali mwana. Zinali zomvetsa cisoni kuwaona akukalamba m’dziko lakale limene linapita tsopano. Munawaona akufooka cifukwa ca matenda. Mukukumbukila kuti munawagwila dzanja pamene anali kumwalila, ndipo munalila kwambili ku manda. Tsopano ndinu osangalala kuwaona kuti ali ndi moyo pamodzi ndi anthu ena ambili, ndipo ali ndi thanzi labwino.

Tili ndi cikhulupililo cakuti zotelezi zidzacitikadi. Zili conco cifukwa cakuti nthawi zonse malonjezo a Mulungu amakwanilitsidwa. M’cigawo cino, tikambilana za maulosi ena okhudza Ufumu amene adzakwanilitsidwa posacedwapa. Zimenezo ndi zimene zidzatsogolela ku nkhondo ya Aramagedo. Tidzakambilananso malonjezo ocititsa cidwi okhudza Ufumu amene adzakwanilitsidwa pambuyo pa Aramagedo. Tidzasangalala kwambili Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila dziko lonse lapansi ndi kupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani