LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb18 January tsa. 8
  • Pita Ukayanjane ndi M’bale Wako Coyamba—Motani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pita Ukayanjane ndi M’bale Wako Coyamba—Motani?
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Nkhani Zofanana
  • Tizithetsa Mikangano Mwamtendele
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Musapunthwitse “Tianati”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • Pitilizani ‘Kumumvela’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
mwb18 January tsa. 8

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Pita Ukayanjane ndi M’bale Wako Coyamba—Motani?

Munthu asiya nsembe yake ku guwa, ndipo apita kukakhazikitsa mtendele na m’bale wake

Yelekezelani kuti mukhala mu mzinda wa Galileya, ni m’nthawi ya Yesu. Ndiye mwapita ku Yerusalemu kukacita Cikondwelelo ca Misasa. Kumeneko, olambila anzanu ocokela kutali ali pilingu-pilingu. Lomba mufuna kupeleka nsembe kwa Yehova. Conco, mwatenga mbuzi na kuuyamba ulendo wopita ku kacisi, ndipo mudutsa m’cigulu ca anthu ambili. Mutafika pakacisi, mupeza kuti pali anthu ambili ofunanso kupeleka nsembe. Kenako, cafika pa imwe kuti mupeleke mbuzi yanu kwa ansembe. Koma mukumbukila kuti m’bale wanu, amene mwina ali m’cigulu ca anthu pakacisipo, kapena kwinakwake mumzindawo, ali namwe cifukwa. Ndiyeno Yesu akuuzani zimene mufunika kucita. (Ŵelengani Mateyu 5:24) Kodi imwe na m’bale wanu amene anakulakwilani mungacite ciani kuti mubwezeletse mtendele potsatila malangizo a Yesu? Pa mndandanda uliwonse uli pansipa, congani yankho loyenelela.

MUYENELA . . .

  • kukamba na m’bale wanu pokhapo ngati mwaona kuti alidi na cifukwa comveka cokhumudwila

  • kuyesa kuwongolela maganizo a m’bale wanu ngati muona kuti ali cabe na mtima wapacala, kapena kuti nayenso analengetsa vutolo

  • kumvetsela modekha pamene m’bale wanu akufotokoza mmene akumvelela. Ndipo ngakhale ngati simunakhutile kweni-kweni na zimene wakamba, m’pepeseni pa kukhumudwa kwake, kapena pa zimene munacita

M’BALE WANU AYENELA . . .

  • kufuna-funa amene angamucilikize mu mpingo mwa kuwauza zimene munamulakwila

  • kukukalipilani, kukamba zonse zimene munamulakwila, na kufuna kuti mpaka muvomeleze colakwa canu

  • kuganizila kudzicepetsa kwanu na kulimba mtima kwanu pomufikila, ndipo akukhululukileni na mtima wonse

Olo kuti masiku ano sitipeleka nsembe za nyama polambila, kodi Yesu anaphunzitsa kuti pali mgwilizano wanji pakati pa kukhala mwamtendele na m’bale wathu na kulambila Mulungu movomelezeka?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani