Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
MARCH 5-11
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 20-21
“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenela Kukhala Mtumiki Wanu”
nwtsty zithunzi
Pamsika
Misika ina, monga umene waonetsedwa pano, inali kupezeka m’mbali mwa mseu. Nthawi zambili amalonda anali kuika katundu na m’njila momwe cakuti anthu anali kusoŵa kopitila. Anthu a kumeneko anali kugula katundu wamba wa m’nyumba, zoumbiwa na dothi, ziwiya za gilasi zodula, komanso zakudya zimene zangofika kumene. Popeza kunalibe mafiliji pa nthawiyo, anthu anali kufunika kupita ku msika tsiku lililonse kuti akagule zinthu. Ku msika kumeneko, ogula zinthu anali kumvetsela nkhani zokambiwa na ogulitsa kapena alendo ena. Ana anali kuseŵelela, ndipo osakila nchito anali kuyembekezela kumeneko kuti apezeko ganyu. Ku msika, Yesu anacilitsa odwala ndipo Paulo anali kulalikilako. (Mac. 17:17) Mosiyana na amenewa, alembi na Afarisi onyada anali kukonda kuimilila m’malo ngati amenewa kuti azipatsiwa moni.
nwtsty mfundo zounikila pa Mat. 20:20, 21
mkazi wa Zebedayo: Uyu anali mayi wa mtumwi Yakobo na Yohane. Malinga na buku la Maliko, Yakobo na Yohane ndiwo anafikila Yesu. Zioneka kuti iwo ndiwo anapeleka pempho, koma anapempha kupitila mwa amayi ŵawo a Salome, amene ayenela kuti anali anti ake a Yesu.—Mat. 27:55, 56; Maliko 15:40, 41; Yoh. 19:25.
mmodzi kudzanja lanu lamanja, wina kumanzele kwanu: Apa malo onse ni olemekezeka komanso a ulamulilo. Koma malo olemekezeka kwambili ni a ku dzanja la manja.—Sal. 110:1; Mac. 7:55, 56; Aroma 8:34.
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 20:26, 28
mtumiki: kapena “kapolo.” Nthawi zambili Baibo imaseŵenzetsa liu la Cigiriki lakuti di·aʹko·nos kutanthauza munthu amene saleka kutumikila ena modzicepetsa. Liuli limaseŵenzetsewa pokamba za Khristu (Aroma 15:8), atumiki kapena akapolo a Khristu (1 Akor. 3:5-7; Akol. 1:23), atumiki othandiza (Afil. 1:1; 1 Tim. 3:8), komanso anchito apanyumba (Yoh. 2:5, 9) ndi akulu-akulu a boma (Aroma 13:4).
sanabwele kudzatumikilidwa, koma kudzatumikila: Kapena “osati kuti amutumikile, koma kuti atumikile.”
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 21:9
M’pulumutseni: Liu lake leni-leni ni “Hosana.” Liu la Cigiriki limeneli linacokela ku liu la Ciheberi limene limatanthauza “m’pulumutseni” kapena kuti “conde tipulumutseni.” Pano, liuli laseŵenzetsewa monga pempho locondelela Mulungu kuti apeleke cipulumutso kapena cipambano. M’mau ena tingakambe kuti “conde, m’pulumutseni cite.” M’kupita kwa nthawi, liu limeneli linali kuseŵenzetsewa popemphela na potamanda. Liu la Ciheberi limeneli lipezeka pa Sal. 118:25, imene inali mbali ya nyimbo za masalimo zoimbiwa pa nyengo ya cikondwelelo ca Pasika. Conco, anthu anali kukumbukila mau amenewa pa cocitika cimeneci. Njila imodzi imene Mulungu anayankhila pempho limeneli lakuti m’pulumutseni Mwana wa Davide, ni mwa kuukitsa Yesu kwa akufa. Pa Mat. 21:42, Yesu iye mwini anagwila mau Sal. 118:22, 23 okamba za Mesiya.
Mwana wa Davide: Mau awa aonetsa kuti anthuwo anali kuudziŵa mzela wobadwila wa Yesu, na udindo wake monga Mesiya wolonjezedwa.
MARCH 12-18
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 22-23
“Muzitsatila Malamulo Aŵili Aakulu a m’Cilamulo”
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 22:37
mtima: Liuli likaseŵenzetsewa mophiphilitsa, limatanthauza umunthu wonse wamkati. Koma likatomolewa pamodzi na “moyo” na “maganizo,” mwacionekele limakhala na tanthauzo lacindunji ndipo kambili limatanthauza zolaka-laka za munthu, na mmene amvelela. Mau atatu amene anaseŵenzetsewa pa vesiyi (mtima, moyo, na maganizo) amayendela pamodzi; ndipo matanthauzo ake nawonso amafananako. Mawuwa awachulila pamodzi pofuna kutsindika mwamphamvu mfundo yakuti tifunika kum’konda kwambili Mulungu.
moyo: Kapena kuti “moyo wonse”
maganizo: Kutanthauza nzelu zonse. Munthu afunika kuseŵenzetsa nzelu zake kuti adziŵe Mulungu na kuti akulitse cikondi cake pa iye. (Yoh. 17:3, Aroma 12:1) M’malemba a Ciheberi, pa Deut. 6:5, anaseŵenzetsa mau atatu akuti ‘mtima, moyo, na mphamvu.’ Koma m’malemba a Cigiriki, malinga na mmene buku la Mateyu lionetsela, anaseŵenzetsa liu lakuti “maganizo” m’malo mwa liu lakuti “mphamvu.” Pangakhale zifukwa zambili zimene anaseŵenzetsela mau osiyana. Coyamba, ngakhale kuti m’Ciheberi cakale munalibe liu leni-leni lakuti “maganizo,” tanthauzo lake linali kumvekela mu liu la Ciheberi lakuti “mtima”. Liuli likaseŵenzetsewa mophiphilitsa limatanthauza umunthu wonse wamkati, kuphatikizapo kaganizidwe ka munthu, mmene amvelela, khalidwe lake, na zocita zake. (Deut. 29:4; Sal. 26:2; 64:6; onani mfundo younikila pa mtima mu vesi ino.) Pa cifukwa ici, pa mavesi a m’Ciheberi pamene anaseŵenzetsa liu lakuti “mtima,” mu Septuagint ya Cigiriki mwambili anaseŵenzetsa liu la Cigiriki lakuti “maganizo.” (Gen. 8:21; 17:17; Miy. 2:10; Yes. 14:13) Cifukwa cina cimene Mateyu anaseŵenzetsela liu la Cigiriki lakuti “maganizo” m’malo mwa liu lakuti “mphamvu” pogwila mau Deut. 6:5, n’cakuti liu la Ciheberi lomasulidwa kuti “mphamvu” [kapena kuti “mphamvu zonse,”] lingaphatikizepo zonse ziŵili, mphamvu na nzelu kapena kuti luso la kuganiza. Mulimonsemo, kufanana kwa lingalilo la mau a Ciheberi ndi a Cigiriki, kungatithandize kufotokoza cifukwa cake olemba Mauthenga Abwino pogwila mau Deuteronomo sanaseŵenzetse mau ofanana ndendende.
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 22:39
Laciŵili: Pa Mat. 22:37, pali yankho limene Yesu anapeleka mwacindunji kwa Mfarisi. Koma Yesu anapitiliza kumuyankha na kugwila mau lamulo laciŵili (Lev. 19:18), pofuna kuphunzitsa kuti malamulo aŵili amenewa ni ogwilizana, ndi kuti Cilamulo conse cagona pa malamulo aŵili amenewa kuphatikizanso zolemba za Aneneli.—Mat. 22:40.
mnzako: Liu la Cigiriki lakuti “mnzako” (mau ake eni-eni, “amene ali pafupi”) angaphatikizepo anthu amene simukhala nawo pafupi. Angatanthauze aliyense amene munthu amayanjana naye.—Luka 10:29-37; Aroma 13:8-10.
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 22:40
Cilamulo . . . zolemba za Aneneli: “Cilamulo” citanthauza mabuku a m’Baibo kuyambila Genesis mpaka Deuteronomo. “Zolemba za Aneneli” zitanthauza mabuku a ulosi a Malemba a Ciheberi. Komabe, mauwa akakambiwa pamodzi, angatanthauze Malemba onse a Ciheberi.—Mat. 7:12; 22:40; Luka 16:16.
cagona: Liu lake leni-leni m’Cigiriki litanthauza “kukoloŵeka pa.” Apa analiseŵenzetsa m’lingalilo lophiphilitsa kutanthauza “cidalila pa, kapena cazikidwa pa.” Yesu anaonetsa kuti si Cilamulo ca Malamulo Khumi cabe, koma Malemba onse a Ciheberi amene azikidwa pa cikondi.—Aroma 13:9.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 22:21
zinthu za Kaisara kwa Kaisara: Mau a Yesu pa vesiyi apezekanso pa Maliko 12:17 na pa Luka 20:25, ndipo ni pamenepa cabe m’Baibo yonse pamene Yesu anachulako za Mfumu ya Roma. Zinthu za Kaisara” ziphatikizapo kulipila misonkho ku boma kaamba ka nchito zimene imacita, ndiponso kulemekeza na kugonjela olamulila moyenelela.—Aroma 13:1-7.
zinthu . . . za Mulungu kwa Mulungu: Zinthu “za Mulungu” ziphatikizapo kulambila Mulungu na mtima wonse, kumukonda mocokela pansi pa mtima, na kumumvela mokhulupilika.—Mat. 4:10; 22:37, 38; Mac. 5:29; Aroma 14:8.
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 23:24
amene mumasefa zakumwa zanu kuti mucotsemo kanyelele koma mumameza ngamila: Nyelele na ngamila zinali zina mwa zolengedwa zazing’ono ndi zazikulu zodetsedwa zimene Aisiraeli anali kuzidziŵa. (Lev. 11:4, 21-24) Yesu anaseŵenzetsa mau okokomeza pokamba kuti atsogoleli a cipembedzo amasefa zakumwa zawo n’colinga cakuti asakhale odetsedwa mwamwambo na kanyelele, koma amanyalanyaza zinthu zofunika za m’Cilamulo, cinthu cimene cifanana na kumeza ngamila.
MARCH 19-25
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 24
“Khalanibe Ogalamuka m’Masiku Otsiliza Ano”
it-2 279 pala. 6
Cikondi
Cikondi ca Anthu Cidzazilala. Yesu Khristu pouza ophunzila ake zinthu zimene zidzacitika m’tsogolo, anaonetsa kuti cikondi (a·gaʹpe) ca anthu ambili amene amakamba kuti akhulupilila Mulungu cidzazilala. (Mat. 24:3, 12) Mtumwi Paulo anakamba kuti monga cizindikilo ca nthawi yovuta imene ikubwela, anthu adzakhala “okonda ndalama.” (2 Tim. 3:1, 2) Conco, n’zoonekelatu kuti munthu angalephele kuona mfundo zolungama, ndipo cikondi cimene anali naco cingayambe kusila pang’ono-pang’ono. Izi zimaonetsa kufunika kopitiliza kuonetsa cikondi na kucikulitsa mwa kusinkha-sinkha Mau a Mulungu ndi mwa kuumba umunthu wathu mogwilizana na mfundo za Mulungu.—Aef. 4:15, 22-24.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 24:8
zoŵaŵa za pobeleka: Liu leni-leni la Cigiriki litanthauza ululu waukulu kwambili umene mayi amamvela pobeleka. Ngakhale kuti pano liuli laseŵenzetsedwa potanthauza mavuto, kuŵaŵa, na kuvutika kwa mtundu uliwonse, liuli litipatsa cithunzi cakuti monga zoŵaŵa za pobeleka, mavuto amene anakambiwilatu adzaculukila-culukila na kukulila-kulila cisautso cacikulu cochulidwa pa Mat. 24:21 cisanayambe.
nwtsty mfundo younikila pa Mat. 24:20
nyengo ya cisanu: M’nyengo imeneyi kunali kugwa mvula yamphamvu, madzi anali kusefukila, ndipo kunali kukhala kozizila kwambili. Cifukwa ca izi, anthu anali kulephela kuyenda maulendo, kupeza cakudya, na kupeza malo okhala.—Ezara 10:9, 13.
pa tsiku la sabata: M’cigawo monga ca Yudeya, malamulo okhudzana na lamulo la Sabata anali kulepheletsa munthu kuyenda maulendo atali-atali na kunyamula katundu. Komanso, zipata za mizinda zinali kukhala zotseka pa tsiku la Sabata.—Onani Mac. 1:12 ndi pa cigawo 16 m’kabuku kakuti Buku Lothandiza Pophunzila Mau a Mulungu.