Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
JUNE 4-10
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MALIKO 15-16
“Kukwanilitsidwa kwa Maulosi Okhudza Yesu”
nwtsty mfundo zounikila pa Maliko 15:24, 29
kugaŵana malaya ake akunja: Pa Yoh. 19:23, 24 pali mfundo zina zimene Mateyu, Maliko, na Luka sanachule: Cioneka kuti asilikali aciroma anacita maele pa zovala zake zakunja na zam’kati; asilikali anagaŵa zovala zake zakunja “m’zigawo zinayi, kuti msilikali aliyense atenge cigawo cimodzi”; iwo sanafune kuti agaŵe malaya ake amkati, conco anacita maele pa malayawo; ndipo kucita maele pa zovala za Mesiya kunakwanilitsa ulosi wa pa Sal. 22:18. Zioneka kuti unali mwambo wa opacika anthu kusunga zovala za munthu wopacikidwa. Conco, anthu amene anali apandu anali kuwavula zovala na kuwalanda zinthu zimene anali nazo asanawapacike. Anali kucita izi n’colinga cakuti awacititse manyazi.
kupukusa mitu yawo: Nthawi zambili anthu anali kupukusa mitu uku akukamba mau. Kucita izi kunali kuonetsa kuti munthu waipidwa, wakalipa, kapena akunyoza. Anthu opita na njila, mosadziŵa anakwanilitsa ulosi wa pa Sal. 22:7.
nwtsty mfundo younikila pa Maliko 15:43
Yosefe: Kusiyana kwa zimene olemba Mauthenga Abwino analemba zokhudza Yosefe, ni umboni wakuti aliyense analemba buku lake payekha. Wokhometsa msonkho Mateyu anaonetsa kuti Yosefe anali ‘munthu wacuma’; Maliko, amene kwakulu-kulu anali kulembela Aroma, anakamba kuti Yosefe anali “munthu wodziŵika wa m’Bungwe Lalikulu la Ayuda” amene anali kuyembekezela Ufumu wa Mulungu; Luka, dokota wacifundo, anakamba kuti Yosefe anali “munthu wabwino ndi wolungama” amene sanavomeleze ciwembu cimene a m’Bungwe Lalikulu la Ayuda anakonzela Yesu; Yohane yekha ndi amene amakamba kuti Yosefe anali “wophunzila wa Yesu koma wamseli cifukwa anali kuopa Ayuda.”—Mat. 27:57-60; Maliko 15:43-46; Luka 23:50-53; Yoh. 19:38-42.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Maliko 15:25
ca m’ma 9 koloko m’maŵa: Kapena kuti “ola lacitatu.” Ena amakamba kuti pali kusiyana kwa nthawi pakati lembali na la Yoh. 19:14-16, limene limakamba kuti “nthawi inali ca m’ma 12 koloko masana,” pamene Pilato anapeleka Yesu kuti apacikiwe. Olo kuti Malemba safotokoza bwino-bwino kusiyana kwake, nazi mfundo zimene tifunika kuganizila: Olemba Uthenga Wabwino onse analemba zogwilizana pa nkhani ya nthawi yokhudza zocitika pa tsiku limene Yesu anaphedwa. Mauthenga onse anayi amaonetsa kuti m’maŵa kutaca, ansembe aakulu komanso akulu anakumana n’kugwilizana zakuti amange Yesu na kukam’peleka kwa bwanamkubwa waciroma, Pontiyo Pilato. (Mat. 27:1, 2; Maliko 15:1; Luka 22:66–23:1; Yoh. 18:28) Mateyu, Maliko, na Luka, onse anakamba kuti pamene Yesu anali pamtengo wozunzikilapo, m’dziko lonselo munacita mdima kuyambila “m’ma 12 koloko masana. . . mpaka m’ma 3 koloko.” (Mat. 27:45, 46; Maliko 15:33, 34; Luka 23:44) Cina cofunika kucikumbukila pa nkhani ya nthawi imene Yesu anaphedwa ni ici: Ena anali kuona kuti kukwapulidwa kunali ngati ciyambi ca kupacikidwa. Nthawi zina munthu anali kukwapuliwa mwankhanza kwambili cakuti anali kufa panthawi yomweyo. Yesu ayenela kuti anakwapuliwa kwambili cakuti analephela kunyamula yekha mtengo wake wozunzikilapo, ndipo munthu wina ni amene anamunyamulila. (Luka 23:26; Yoh. 19:17) Ngati anthu anali kuona kuti kupacika munthu kunali kuyamba na kumukwapula, ndiye kuti mwina panapita nthawi ndithu kuti amukhomelele pa mtengo wozunzikilapo. Pocilikiza mfundo imeneyi, pa Mat. 27:26 komanso pa Maliko 15:15, pali mau onse aŵili, kukwapula na kupacika pa mtengo wozunzikilapo. Conco, nthawi zimene anthu angakambe pa kupacikidwa kwa Yesu zingakhale zosiyana-siyana, malinga ndi pamene ayambila kuŵelenga nthawi. Izi zingatithandize kudziŵa cifukwa cake Pilato anadabwa kuti Yesu anafa mwamsanga atam’khomelela pa mtengo. (Maliko 15:44) Kuwonjezela apo, olemba Baibo kambili anali na cizoloŵezi cogaŵa tsiku m’zigawo zinayi za maola atatu-atatu, monga mmene anali kugaŵila nthawi ya usiku. Kugaŵa tsiku mwa njila imeneyo kumafotokoza cifukwa cake pakukambiwa za 9 koloko m’mawa, 12 koloko, na 3 koloko masana, kuŵelenga kuyambila pamene dzuŵa likutuluka pa 6:00 m’maŵa. (Mat. 20:1-5; Yoh. 4:6; Mac. 2:15; 3:1; 10:3, 9, 30) Cinanso, anthu sanali kudziŵa nthawi yeni-yeni, conco kambili pochula nthawi anali kuikako mau akuti “ca m’ma,” monga mmene Yoh. 19:14 ikuonetsela. (Mat. 27:46; Luka 23:44; Yoh. 4:6; Mac. 10:3, 9) Mwacidule tingakambe kuti: Nthawi imene Maliko analemba inaphatikazapo zonse ziŵili kukwapulidwa na kukhomeleledwa pa mtengo, pamene nthawi imene Yohane analemba inakamba cabe za kukhomeleledwa pa mtengo. Olemba Baibo aŵiliwa ayenela kuti anangochula nthawi yawo moyelekezela. Ndiye cifukwa cake Yohane anaseŵenzetsa mau akuti “ca m’ma” pokamba nthawi yake ya zocitikazi. Mfundo izi zingatithandize kudziŵa cifukwa cake Baibo ikuchula nthawi zosiyana pa nkhani imeneyi. Cothela, pamene Yohane analemba buku lake patapita zaka zambili, anachula nthawi yosiyana na imene Maliko analemba. Zimenezi zionetsa kuti analemba payekha, sanakopele m’Buku la Maliko.
nwtsty mfundo younikila pa Maliko 16:8
cifukwa anagwidwa ndi mantha: Malinga na mipukutu yoyambilila ya mbali yothela ya buku la Maliko, Uthenga Wabwino umenewu umatha na mau opezeka mu vesi 8. Ena amakamba kuti kutha kwa lembali kunangocitika mwadzidzidzi, cakuti sipangakhale pothela pa buku. Komabe, tikaona kalembedwe kacidule ka Maliko, zimenezo sizingakhale zoona kweni-kweni. Cina, akatswili a m’zaka za m’ma 300 C.E., Jerome na Eusebius, anaonetsa kuti mpukutu woyambilila weni-weni umatha na mau akuti “cifukwa anagwidwa ndi mantha.”
Pali mipukutu yambili ya Cigiriki na ma Baibo a vitundu vina amene ali na mau omaliza aafupi kapena aatali owonjezela pambuyo pa vesi 8. Mau omaliza aatali (okhala na mavesi 12 owonjezela) apezeka m’mipukutu yochedwa Codex Alexandrinus, Codex Ephraemi Syri rescriptus, na Codex Bezae Cantabrigiensis, onse analembedwa m’zaka za m’ma 400 C.E. Mau omaliza amenewa amaonekelanso m’ma Baibo ochedwa Vulgate ya cilatini, Curetonian Syriac, na Syriac Peshitta. Komabe, mau aya sapezeka m’mipukutu ya Cigiriki iŵili yoyambilila ya m’zaka za m’ma 300 C.E., yochedwa Codex Sinaiticus na Codex Vaticanus, olo mu Codex Sinaiticus Syriacus ya m’zaka za m’ma 300 C.E. kapena 400 C.E. Sapezekanso ngakhale mu mpukutu woyambilila kwambili wochedwa Sahidic Coptic manuscript of Mark wa m’zaka za m’ma 400 C.E. Mofananamo, mipukutu yakale kwambili ya buku la Maliko m’Baibo ya Ciameniya na Cigeorgiya imatha na mau a mu vesi 8.
Mipukutu ina ya Cigiriki na ma Baibo a vitundu vina amene anapezeka pambuyo pake, ali na mau omaliza aafupi (okhala na ziganizo zoŵelengeka). Mpukutu wochedwa Codex Regius wa m’ma 700 C.E. uli na zonse ziŵili, koma anayambila kulemba mau omaliza aafupi. Mau omaliza aliwonse amayamba na mau akuti mau awa anaseŵenzetsewapo ndi akatswili ena, olo kuti zimene analembazo zilibe umboni wotsimikizilika.
MAU OMALIZA AAFUPI
Mau omaliza aafupi amene analembedwa pambuyo pa Maliko 16:8 saali mbali ya Malemba ouzilidwa. Mauwa amati:
Koma zinthu zonse zimene analamula, iwo anazifotokoza mwachidule kwa amene anali pafupi ndi Petulo. Komanso izi zitatha, Yesu mwiniyo anatumiza uthenga woyera ndi wosawonongeka wa chipulumutso chosatha kudzera mwa ophunzira, kuchokera kum’mawa mpaka kumadzulo.
MAU OMALIZA AATALI
Mau omaliza aatali amene analembedwa pambuyo pa Maliko 16:8 saali mbali ya Malemba ouzilidwa. Mauwa amati:
Atauka m’mawa tsiku loyamba la mlungu, anaonekera choyamba kwa Mariya Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7. 10 Mayiyu anapita ndi kukauza amene anali kukhala ndi Yesu, pakuti anali achisoni ndipo anali kulira. 11 Koma iwo, pamene anamva kuti ali moyo ndi kuti iye wamuona, sanakhulupirire. 12 Komanso, izi zitachitika anaonekera mwamtundu wina kwa awiri a iwo pamene anali kuyenda nawo limodzi popita kumidzi. 13 Pamenepo iwo anabwerera ndi kukauza enawo. Ndipo nawonso sanakhulupirire zimenezo. 14 Koma pambuyo pake anaonekera kwa ophunzira 11 aja pamene anali kudya chakudya patebulo. Pamenepo iye anawadzudzula chifukwa chosowa chikhulupiriro ndi kuuma mitima kwawo, pakuti iwo sanakhulupirire anthu amene anamuona atauka kwa akufa. 15 Iye anawauza kuti: “Pitani m’dziko lonse ndi kukalalikira uthenga wabwino ku cholengedwa chilichonse. 16 Amene adzakhulupirira ndi kubatizidwa adzapulumuka, koma amene sadzakhulupirira adzaweruzidwa. Komanso, okhulupirira adzachita zizindikiro izi: M’dzina langa adzatulutsa ziwanda, ndi kulankhula m’malilime. 18 Adzanyamula njoka ndi manja awo, ndipo akadzamwa chilichonse chakupha sichidzawavulaza ngakhale pang’ono. Adzaika manja awo pa anthu odwala, ndipo adzachira.”
19 Choncho Ambuye Yesu atatsiriza kulankhula nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndi kukakhala kudzanja lamanja la Mulungu. 20 Pamenepo iwo anachoka ndi kupita kukalalikira kwina kulikonse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito limodzi ndi kutsimikizira uthengawo mwa zizindikiro zimene anali kuchita.
JUNE 11-17
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 1
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila pa Luka 1:69
nyanga yacipulumutso: Kapena kuti “mpulumutsi wamphamvu.” M’Baibo, nyanga za nyama kambili zimaimila mphamvu, kugonjetsa, na cipambano. (1 Sam. 2:1; Sal. 75:4, 5, 10; 148:14; onani mau amunsi.) Cina, olamulila abwino na oipa omwe amaimilidwa ndi nyanga, ndipo kugonjetsa kwawo pankhondo kunali kuyelekezedwa na kugunda ndi yanga. (Deut. 33:17; Dan. 7:24; 8:2-10, 20-24) Pa vesiyi, mau akuti “nyanga yacipulumutso” atanthauza Mesiya monga munthu wokhala na mphamvu zopulumutsa, mpulumutsi wamphamvu.
nwtsty mfundo zounikila pa Luka 1:76
udzatsogola pamaso pa Yehova: Yohane M’batizi ‘anatsogola pamaso pa Yehova’ m’lingalilo lakuti anali kudzakhala kalambula bwalo wa Yesu amene anali kudzaimila Atate wake, ndiponso amene anali kudzabwela m’dzina la Atate wake.—Yoh. 5:43; 8:29; onani mfundo zounikila pa Yehova mu vesi ino.
JUNE 18-24
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 2-3
“Acicepele—Kodi Mukukula Mwauzimu?”
nwtsty mfundo younikila pa Luka 2:41
makolo ake anali kukonda: M’cilamulo munalibe lamulo lakuti akazi azicitako cikondwelelo ca Pasika. Ngakhale n’conco, Mariya anali kukonda kupelekeza Yosefe ku Yerusalemu kukacita cikondwelelo cimeneci caka ciliconse. (Eks. 23:17; 34:23) Caka ciliconse, iwo pamodzi na banja lawo lalikulu anali kuyenda ulendo wa makilomita pafupi-fupi 300, kupita na kubwelako.
nwtsty mfundo zounikila pa Luka 2:46, 47
kuwafunsa mafunso: Zimene anthu amene anali kumvetsela Yesu anacita, zionetsa kuti iye sanali kufunsa mafunso monga kamwana kofuna cabe kudziŵa zinthu zimene kacita nazo cidwi. (Luka 2:47) Liu la Cigiriki limene analimasulila kuti “kufunsa . . . mafunso,” pa nkhani zina lingatanthauze mtundu wa mafunso na kafunsidwe kamene amaseŵenzetsa poweluza munthu. (Mat. 27:11; Maliko 14:60, 61; 15:2, 4; Mac. 5:27) Akatswili a mbili yakale amakamba kuti atsogoleli ena acipembedzo olemekezeka anali kukonda kutsalila pa kacisi pa khonde lina lalikulu cikondwelelo cikatha, kuti aziphunzitsa anthu. Anthu anali kukhala pansi n’kumawamvetsela na kuwafunsa mafunso.
anadabwa kwambili: Pa vesiyi kalembedwe ka Cigiriki ka liu lakuti “kudabwa,” kangapeleke lingalilo la kupitiliza kapena kudabwa mobweleza-bweleza.
nwtsty mfundo younikila pa Luka 2:51, 52
anapitiliza kuwamvela: Kapena kuti “anakhalabe wogonjela; anakhalabe womvela.” Liu la Cigiriki lakuti anapitiliza, lionetsa kuti pambuyo pakuti Yesu wadabwitsa aphunzitsi pa kacisi cifukwa ca kudziŵa kwake Mau a Mulungu, anapita kunyumba na kupitiliza kumvela makolo ake modzicepetsa. Iye anali womvela kwambili kuposa mwana wina aliyense; iye anakwanilitsa kothelatu Cilamulo ca Mose.—Eks. 20:12; Agal. 4:4.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo zounikila pa Luka 2:14
ndipo pansi pano mtendele pakati pa anthu amene iye amakondwela nawo: M’mipukutu ina muli mau akuti “ndipo pansi pano mtendele kwa anthu amene iye amakondwela nawo.” Mau amenewa amapezekanso m’ma Baibo ena. Koma zimene zili mu Baibulo la Dziko Latsopano, zili na umboni wokwanila wolembedwa wocilikiza mau amenewa. Mau a mngelo amenewa satanthauza kuti Mulungu amakondwela na munthu aliyense mosasamala kanthu za khalidwe lake kapena zocita zake ayi. Koma, atanthauza anthu amene adzayanjidwa na Mulungu cifukwa cokhala na cikhulupililo mwa iye, na kukhala otsatila a Mwana wake.—Onani mfundo younikila pa anthu amene iye amakondwela nawo mu vesi ino.
anthu amene iye amakondwela nawo: Mau akuti “amene iye amakondwela nawo” anacokela ku liu la Cigiriki lakuti eu·do·kiʹa. Liu limeneli lingatanthauzenso “kukonda; kusangalala; kuyanja.” Liu lina lofanana nalo lakuti eu·do·keʹo analiseŵenzetsa pa Mat. 3:17; Maliko 1:11; Luka 3:22 (onani mfundo zounikila pa Mat. 3:17; Maliko 1:11), pamene Mulungu anakamba na Mwana wake atangobatizika. Liu limeneli limapeleka lingalilo la “kumuyanja; kukondwela naye; kumucitila zinthu mokoma mtima; kusangalala naye.” Mogwilizana na mmene mau amenewa aseŵenzetsedwela, mau akuti “anthu amene iye amakondwela nawo” (an·throʹpois eu·do·kiʹas) atanthauza anthu amene akuwanja ndi kukondwela nawo, ndipo tingawakambenso kuti “anthu amene iye amawayanja; anthu amene iye amakondwela nawo.”
JUNE 25–JULY 1
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 4-5
“Kanizani Ziyeso Mmene Yesu Anacitila”
nwtsty zithunzi
Pamwamba pa Cipupa ca Mpanda wa Kacisi
N’kutheka kuti Satana anatenga Yesu mwacindunji n’kupita naye “pamwamba [kapena kuti papatali kwambili] pa cipupa ca mpanda wa kacisi” na kumuuza kuti adziponye pansi. Koma malo eni-eni amene Yesu anaimililapo sadziŵika. Popeza kuti mau akuti “kacisi” amene aseŵenzetsedwa mu vesi ino angatanthauze cimango conse ca kacisi, Yesu ayenela kuti anaimilila pakona ya kum’mwela ca kum’maŵa (1) kwa kacisi. N’kuthekanso kuti mwina Yesu anaimilila pa kona ina ya cimango ca kacisi. Kugwa kucoka pamwamba pa kacisi mosakayikila kukanacititsa imfa, kupatulapo ngati Yehova wacitapo kanthu.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
nwtsty mfundo younikila Luka 4:17
mpukutu wa mneneri Yesaya: Mpukutu wa Yesaya umene unapezeka ku Nyanja Yakufa unapangiwa na zidutswa zogwilana zokwanila 17. Mpukutuwo unali wokwana mamita 7.3 m’litali ndipo unali na madanga 54. Mpukutu umene anali kuseŵenzetsa m’sunagoge ku Nazareti uyenela kuti unali wautali kulingana na umenewu. Mipukutu ya m’zaka 100 zoyambilila inalibe manamba a macaputa na mavesi. Conco Yesu anafunika kupeza mau amene anali kufuna kuŵelenga. Koma popeza kuti anakwanitsa kupeza pamene mau aulosi analembewa, zinaonetsa kuti iye anali kuwadziŵa bwino Mau a Mulungu.
nwtsty mfundo younikila pa Luka 4:25
zaka zitatu ndi miyezi 6: Malinga na lemba la 1 Maf. 18:1, Eliya analengeza za kutha kwa cilala “m’caka cacitatu.” Koma ena amakamba kuti zimene Yesu anakamba zitsutsana na zimene zinalembewa m’buku la 1 Mafumu. Komabe, zimene zinalembewa m’Malemba a Ciheberi, sizionetsa kuti cilala cinatha pa zaka zosacepela zitatu. Mau akuti “m’caka cacitatu” aonetsa kutalika kwa nthawi imene inayamba kucokela pamene Eliya analengeza koyamba za cilala kwa Ahabu. (1 Maf. 17:1) Iye ayenela kuti analengeza izi m’nyengo yotentha (m’malanga), imene kweni-kweni inali kutha pambuyo pa miyezi 6. Koma panthawiyi iyenela kuti inapyola pa miyezi 6. Kuwonjezela apo, cilala sicinathe pa nthawi imene Eliya anaonekelanso kwa Ahabu “m’caka cacitatu,” koma cinatha pambuyo pa moto umene unatsika kucokela kumwamba pa Phili la Karimeli. (1 Maf. 18:18-45) Conco, mau a Yesu amene analembewa m’vesiyi, pamodzi na mau ena a m’bale wake wa Khristu a pa Yak. 5:17, agwilizana na zimene zili pa 1 Maf. 18:1.