NYIMBO 55
Musaŵayope!
1. Patsogolo, anthu anga,
Musayope adani.
Lalikilani mau,
Anthu onse adziŵe
Kuti mwana wanga Khristu
Lomba alamulila.
Posacedwa adzamanga
Satana mdani wathu.
(KOLASI)
Musayope, anthu anga,
Olo akuyofyeni.
Ine nidzakusungani.
Sinidzakusiyani.
2. Ngakhale adani anu,
Aculuke padziko,
Olo akuyofyeni,
Olo akuzunzeni,
Anthu anga musayope,
Nidzakutetezani.
Nidzakusamalilani
Mpaka mudzapambana.
(KOLASI)
Musayope, anthu anga,
Olo akuyofyeni.
Ine nidzakusungani.
Sinidzakusiyani.
3. Siningakuiŵaleni;
Nidzakulimbitsani.
Ngakhale akupheni,
Nidzakuukitsani.
Anthu anga khulupilikani
Mpaka mapeto.
Ndipo ine nidzakupatsani
Moyo wosatha.
(KOLASI)
Musayope, anthu anga,
Olo akuyofyeni.
Ine nidzakusungani.
Sinidzakusiyani.
(Onaninso Deut. 32:10; Neh. 4:14; Sal. 59:1; 83:2, 3.)