LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr18 December masa. 1-7
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
  • Tumitu
  • DECEMBER 3-9
  • DECEMBER 10-16
  • DECEMBER 17-23
  • DECEMBER 24-30
  • DECEMBER 31–JANUARY 6
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu (2018)
mwbr18 December masa. 1-7

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu

DECEMBER 3-9

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 9-11

“Wozunza Akhristu Mwankhaza Akhala Mlaliki Wokangalika”

bt peji 60 pala. 1-2

Mpingo “Unaloŵa M’nyengo Yamtendele”

ANTHU okwiyawo anali pa ulendo wopita kumzinda wa Damasiko kuti akacite zinthu zinazake zankhanza. Iwo ankafuna kuti akagwile, kumanga ndi kuzunza ophunzila a Yesu amene ankadana nawo kwambili, kenako n’kupita nawo ku Khoti Lalikulu la Ayuda ku Yerusalemu kuti akawapatse cilango.

2 Saulo yemwe anali mtsogoleli wa anthuwo, anali kale ndi mlandu wamagazi. Iye ankadana kwambili ndi ophunzila a Yesu ndipo masiku angapo m’mbuyomu, ankaonelela pamene anzake amenenso ankadana ndi ophunzilawo, ankaponya miyala ndi kupha Sitefano, wophunzila wa Yesu amene anali wodzipeleka kwambili polambila Mulungu. (Mac. 7:57–8:1) Saulo sanakhutile ndi kuzunza otsatila a Yesu a ku Yerusalemu, ndipo anali wokonzeka kupitiliza kuzunza ophunzilawo m’madela enanso. Iye ankafuna kuthetselatu gulu la anthu limene ankaliona ngati losokoneza kwambili, lomwe linkadziŵika kuti “Njilayo.”—Mac. 9:1, 2; onani bokosi lakuti “Saulo Anali ndi Mphamvu Zomanga Akhristu ku Damasiko,” patsamba 61.

w16.06 peji 4 pala. 4

Yehova Amatiumba

4 Yehova saona anthu mmene ife timawaonela. M’malomwake, amaona mumtima ndipo amaona mmene aliyense wa ife alili. (Ŵelengani 1 Samueli 16:7b.) Yehova anacita zimenezi pamene anali kukhazikitsa mpingo wacikhiristu. Mulungu anakokela kwa iye ndi kwa Mwana wake anthu ambili amene anali kuonedwa otsika. (Yoh. 6:44) Mwacitsanzo, mmodzi wa anthu amenewo anali Mfarisi wina dzina lake Saulo, amene anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe.” (1 Tim. 1:13) Koma Yehova anayesa mtima wa Saulo ndipo sanamuone monga dothi lacabe-cabe. (Miy. 17:3) M’malomwake, Yehova anaona kuti Saulo angaumbidwe ndi kukhala ‘ciwiya cocita kusankhidwa’ kuti akalalikile “kwa anthu a mitundu ina, komanso kwa mafumu ndi ana a Isiraeli.” (Mac. 9:15) Yehova anasankhanso anthu ena ndi kuwaumba kuti akhale ‘ziwiya zolemekezeka.’ Pa anthu amenewo panali ena amene kale anali kuledzela, kucita zaciwelewele, ndi kuba. (Aroma 9:21; 1 Akor. 6:9-11) Pamene anali kuphunzila Malemba, analimbitsa cikhulupililo cawo mwa Yehova ndipo anamulola kuti awaumbe.

bt peji 64 pala. 15

Mpingo “Unaloŵa M’nyengo Yamtendele”

Saulo atayamba kulalikila za Yesu m’masunagoge, khamu la anthu linadabwa komanso linakwiya kwambili. Anthuwo anafunsa kuti: “Kodi munthu uyu si uja anavutitsa koopsa oitana pa dzina limeneli a ku Yerusalemu?” (Mac. 9:21) Pofotokoza zimene zinam’pangitsa kuti asinthe n’kuyamba kulalikila za Yesu, Saulo anawauza “mfundo zomveka zotsimikizila kuti Yesu ndiyedi Khristu.” (Mac. 9:22) Komabe sikuti mfundo zogwila mtima zingasinthe anthu onse. Mwacitsanzo, anthu amene amaumilila kutsatila miyambo kapena amene safuna kusintha cifukwa conyada, sangasinthe maganizo awo cifukwa cakuti amva mfundo zogwila mtima. Komabe, Saulo sanagwe ulesi.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

bt peji 60-61 pala. 5-6

Mpingo “Unaloŵa M’nyengo Yamtendele”

5 Pamene Yesu anaimitsa Saulo panjila yopita ku Damasiko, sanamufunse kuti: “N’cifukwa ciani ukuzunza ophunzila anga?” Koma monga taonela kale, anamufunsa kuti: “N’cifukwa ciani ukundizunza?” (Mac. 9:4) Zoonadi, otsatila a Yesu akamazunzidwa, Yesu amaona kuti akuzunzidwa ndi iyeyo.—Mat. 25:34-40, 45.

6 Ngati mukuzunzidwa cifukwa cakuti mumakhulupilila Khristu, dziŵani kuti Yehova ndi Yesu akudziŵa zimenezo. (Mat. 10:22, 28-31) Panopa mwina Yehova sangacotse mayeselowo, ndipo kumbukilani kuti Yesu ankaona zimene Saulo ankacita povomeleza kuphedwa kwa Sitefano. Iye ankaonanso pamene Saulo ankapita kunyumba za ophunzila okhulupilika ku Yerusalemu kuti akawagwile ndi kuwaponya m’ndende. (Mac. 8:3) Koma Yesu sanaloŵelele pa nthawiyo. Komabe, Yehova, kudzela mwa Khristu, anapatsa mphamvu Sitefano ndi ophunzila enawo kuti akhalebe okhulupilika.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 10:6

Simoni wina wofufuta zikopa: Munthu wofufuta zikopa za nyama (vikumba), anali kuseŵenzetsa madzi a laimu kuti acotse ubweya kapena tunyama tokhalila na mafuta ku cikumbaco. Akatelo, anali kuviika cikumbaco m’mankhwala ocoka ku mitengo ina kapena zomela zina kuti cifeŵe bwino. Cifukwa vinali kununkha kwambili, ndipo vinali kufuna madzi ambili, ndiye cifukwa cake Simoni anakakhala m’mbali mwa nyanja, ca kumalile kwa mzinda wa Yopa. Malinga na Cilamulo ca Mose, munthu amene anali kugwila nyama zakufa anali wodetsedwa. (Lev. 5:2; 11:39) Conco, Ayuda ambili anali kuona kuti anthu ofufuta vikopa anali otsika, ndipo anali kuyopa kukhala nawo pamodzi. Buku yochedwa Talmud, inaonetsa kuti nchito yofufuta zikopa kapena vikumba inali yotsikilapo kuposa yotaya vinyalala. Komabe, Petulo sanalole kuti maganizo a tsankho amenewo amulepheletse kukakhala kunyumba kwa Simoni. Cifukwa ca maganizo ake opanda tsankho, Petulo anali wokonzeka kulandila utumiki wotsatila—wopita kunyumba ya munthu amene sanali Myuda. Akatswili ena amaona kuti liwu la Cigiriki lakuti “wofufuta” (byr·seusʹ) n’limene anali kumuchula nalo Simoni.

DECEMBER 10-16

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 12-14

“Paulo na Baranaba Apanga Ophunzila Kumadela Akutali”

bt peji 86 pala. 4

‘Anadzazidwa ndi Cimwemwe Ndiponso Mzimu Woyela’

4 Komabe, kodi n’cifukwa ciani mzimu woyela unauza mpingo kuti upatule Baranaba ndi Saulo “kuti agwile nchito” yapadela? (Mac. 13:2) Baibulo silinena cifukwa cake. Koma timadziŵa kuti mzimu woyela ndi umene unatsogolela mpingowo kuti usankhe amuna amenewa. Komabe zikuoneka kuti aneneli ndi aphunzitsi ena a ku Antiokeya sanatsutse maganizo amenewa. M’malomwake, iwo anagwilizana kwambili ndi kusankhidwa kwa amuna aŵiliwa. Taganizani mmene Baranaba ndi Saulo anamvela pamene Akhristu anzawo, mopanda nsanje, ‘anasala kudya ndi kupemphela, kenako n’kuwaika manja ndi kuwalola kuti apite.’ (Mac. 13:3) Ifenso tiyenela kuthandiza anthu amene apatsidwa utumiki mumpingo wacikhristu, monga amuna amene asankhidwa kuti aziyang’anila mumpingo. M’malo mocita nsanje ndi anthu amene alandila utumiki umenewu, tiyenela ‘kuwapatsa ulemu waukulu mwacikondi cifukwa ca nchito yawo.’ —1 Ates. 5:13.

bt peji 95 pala. 5

‘Analankhula Molimba Mtima Cifukwa ca Mphamvu ya Yehova’

5 Coyamba, Paulo ndi Baranaba anaima mumzinda wa Ikoniyo. Mzindawu unali umodzi mwa mizinda yofunika kwambili ya Aroma ya m’cigawo ca Galatiya, ndipo anthu ake ankatsatila cikhalidwe ca Agiriki. Mumzindawu munkakhala Ayuda ambili komanso anthu ambili amitundu ina amene analoŵa cipembedzo caciyuda. Mwa cizoloŵezi cawo, Paulo ndi Baranaba analoŵa m’sunagoge ndi kuyamba kulalikila. (Mac. 13:5, 14) Iwo “analankhula bwino kwambili moti khamu lalikulu la Ayuda limodzi ndi Agiriki anakhala okhulupilila.”—Mac. 14:1.

w14 9/15 peji 13 mapa. 4-5

Tumikilani Mulungu Mokhulupilika Panthawi ya “Masautso Ambili”

4 Paulo ndi Baranaba atacoka ku Debe, “anabwelela ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya. M’malo onsewa anali kulimbitsa mitima ya ophunzila ndi kuwalimbikitsa kuti akhalebe m’cikhulupililo. Anali kuwauza kuti: ‘Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.’” (Mac. 14:21, 22) Mawu amenewa ukangowamva samveka olimbikitsa. Mfundo yakuti anayenela kukumana ndi “masautso ambili” inaoneka kukhala yokhumudwitsa, osati yolimbikitsa. Nanga n’cifukwa ciani Paulo ndi Baranaba ‘analimbikitsa ophunzila’ mwa kuwauza kuti adzakumana ndi masautso ambili?

5 Tingapeze yankho mwa kupendanso bwino-bwino mawu a Paulo. Iye sanangokamba kuti: “Tiyenela kupilila masautso ambili.” M’malo mwake, anati: “Tiyenela kukumana ndi masautso ambili kuti tikaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Conco, Paulo analimbikitsa ophunzila pogogomezela kuti kukhulupilika kumabweletsa mphoto. Mphoto imeneyo si loto cabe. Ndiye cifukwa cake Yesu anati: “Yekhayo amene adzapilile mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”—Mat. 10:22.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w08 5/15 peji 32 pala. 7

Mfundo Zazikulu za M’buku la Machitidwe

12:21-23; 14:14-18. Herode sanakane kulandila ulemelelo womwe unafunika kupita kwa Mulungu yekha basi. Mosiyana ndi Herode, Paulo ndi Baranaba anakanitsitsa kutamandidwa ndi kupatsidwa ulemu wosawayenelela. Tisamafune ulemelelo pa zilizonse zimene tingacite potumikila Yehova.

nwtsty mfundo zounikila pa Mac. 13:9

Saulo, wochedwanso Paulo: Kuyambila apa kupita m’tsogolo, Saulo anayamba kudziŵika na dzina lakuti Paulo. Mtumwiyu, mwacibadwa anali Mheberi komanso nzika ya Roma. (Mac. 22:27, 28; Afil. 3:5) Conco, n’kutheka kuti kucoka pa ubwana wake, Paulo anali kudziŵika na maina onse aŵili, la Ciheberi lakuti Saulo, komanso la Ciroma lakuti Paulo. Panthawiyo, zinali zofala Ayuda kukhala na maina aŵili, maka-maka amene sanali kukhala mu Isiraeli. (Mac. 12:12; 13:1) Acibululu ena a Paulo analinso na maina a Ciroma kapena a Cigiriki. (Aroma 16:7, 21) Pokhala “mtumwi weni-weni wotumidwa kwa mitundu ina,” Paulo anapita kukalengeza uthenga wabwino kwa anthu osakhala Ayuda. (Aroma 11:13) Iye ayenela kuti anasankha kuseŵenzetsa dzina lake la Ciroma, mwina cifukwa cakuti anaona kuti ndilo lingakhale bwino kwa anthu. (Mac. 9:15; Agal. 2:7, 8) Ena amaganiza kuti Paulo anatenga dzinali cifukwa colemekeza Serigio Paulo, zimene n’zokayikitsa, cifukwa Paulo anali kudziŵikabe na dzinali ngakhale pamene anali kucoka ku Kupuro. Ena amakamba kuti Paulo sanafune kuseŵenzetsa dzina lake la Ciheberi, cifukwa kachulidwe kake mu Cigiriki kalingana na liwu la Cigiriki, limene limatanthauza munthu (kapena nyama) amene amayenda motumbama.—Onani mfundo younikila pa Mac. 7:58.

Paulo: Mu Malemba Acigiriki Acikhristu, dzina lakuti Pauʹlos, mu Cilatini Paulus, kutanthauza “Kakang’ono; Kocepa,” analiseŵenzetsa nthawi zokwana 157 pokamba za mtumwi Paulo, komanso kamodzi pokamba za bwanamkubwa wa Kupuro dzina lake Serigio Paulo.—Mac. 13:7.

DECEMBER 17-23

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 15-16

“Cigamulo Cozikidwa pa Mawu a Mulungu”

bt peji 102-103 pala. 8

‘Sanamvane Ndipo Anatsutsana Kwambili’

8 Luka anapitiliza kuti: “Paulo ndi Baranaba sanamvane nawo [“amuna ena” aja] ndipo anatsutsana nawo kwambili. Conco iwo [akulu] anasankha Paulo ndi Baranaba, pamodzi ndi ena mwa iwo, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu, kuti akawauze za kutsutsanako.” (Mac. 15:2) Mfundo yakuti iwo ‘sanamvane ndipo anatsutsana,’ ikusonyeza kuti pa magulu aŵili otsutsanawo, gulu lililonse linkakhulupilila kwambili kuti zimene iwowo akunena n’zoona osati za anzawozo, ndipo mpingo wa ku Antiokeya sukanatha kuthetsa nkhaniyo. Pofuna kuti mtendele ndi mgwilizano usasokonezeke mumpingo, mpingowo unacita zinthu mwanzelu potumiza nkhaniyo kwa “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,” amene anali m’bungwe lolamulila. Kodi tingaphunzile ciani pa zimene akulu a ku Antiokeya anacita?

w12 1/15 peji 5 mapa. 6-7

Akhristu Oona Amalemekeza Mawu a Mulungu

6 Nkhaniyi inathetsedwa pogwilitsa nchito Amosi 9:11, 12. Lembali analigwila mawu pa Machitidwe 15:16, 17 pamene timaŵelenga kuti: “Ndidzabwelela ndi kumanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo ndi kuiimikanso. Ndidzacita zimenezi kuti anthu otsalilawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu ochedwa ndi dzina langa, watelo Yehova.”

7 Koma wina anganene kuti, ‘Lembalitu silikunena kuti anthu a mitundu ina amene anayamba kukhulupilila sanafunike kudulidwa.’ Zimenezo n’zoona koma Akhristu aciyuda anamvetsa zimene lembali linkatanthauza. Iwo ankaona kuti anthu a mitundu ina amene anali odulidwa ndi abale awo. (Eks. 12:48, 49) Mwacitsanzo, m’Baibulo lina, lemba la Esitere 8:17 limati: “Anthu ambili a mitundu ina anadulidwa ndipo anakhala Ayuda.” (Septuagint ya Bagster) Conco zinali zomveka pamene Malemba analosela kuti anthu otsalila a nyumba ya Isiraeli (Ayuda ndi anthu a mitundu ina odulidwa amene analoŵa Ciyuda) pamodzi ndi “mitundu yonse ya anthu” (anthu a mitundu ina osadulidwa) adzakhala anthu ochedwa ndi dzina la Mulungu. Cotelo anthu a mitundu ina amene ankafuna kukhala Akhristu sanafunike kudulidwa.

bt peji 123 pala. 18

“Kulimbitsa Mipingo”

18 Paulo ndi Timoteyo anatumikila Mulungu limodzi kwa zaka zambili. Popeza iwo anali atumiki oyendayenda, anagwila nchito zosiyanasiyana poimila bungwe lolamulila. Nkhani ya m’Baibulo imeneyi imati: “Popitiliza ulendo wawo m’mizinda, anali kupatsa okhulupilila a kumeneko malamulo oyenela kuwatsatila, malinga ndi zimene atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anagamula.” (Mac. 16:4) N’zodziŵikilatu kuti mipingo inatsatila malangizo ocokela kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu. Cifukwa cakuti iwo anamvela, “mipingo inapitiliza kulimba m’cikhulupililo ndipo ciŵelengelo cinapitiliza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.”—Mac. 16:5.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w12 1/15 peji 10 pala. 8

Phunzilani Kukhala Maso Kucokela kwa Atumwi a Yesu

8 Kodi tikuphunzilapo ciani pa nkhani imeneyi? Onani kuti mzimu wa Mulungu unatsogolela Paulo pamene ananyamuka kupita kukalalikila ku Asia. Kenako unamutsogolelanso atayandikila Bituniya. Komanso Paulo atafika ku Torowa, m’pamene mzimuwu unamutsogolela kupita ku Makedoniya. Monga mutu wa mpingo, masiku anonso Yesu angatitsogolele cimodzi-modzi. (Akol. 1:18) Mwacitsanzo, mwina inuyo munaganizapo zotumikila monga mpainiya kapena mumafuna kusamukila kumene kukufunikila olalikila uthenga ambili. Yesu angakuthandizeni pogwilitsa nchito mzimu wa Mulungu koma kokha ngati inuyo mutacitapo kanthu kuti mukwanilitse colinga canuco. Mwacitsanzo, munthu akhoza kukhotetsa galimoto kumanja kapena kumanzele pokha-pokha ngati ikuyenda. N’cimodzimodzinso Yesu. Iye akhoza kutitsogolela pamene tikufuna kuwonjezela utumiki wathu koma pokha-pokha ngati tikucita zinthu zotithandiza kukwanilitsa zolinga zimene tili nazo.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 16:37

ndife Aroma: Kutanthauza, nzika za Roma. Paulo, mwinanso na Sila anali nzika za Roma. Malamulo a Aroma anali kukamba kuti, nzika nthawi zonse zifunika kuweluzidwa mwacilungamo, ndipo sanali kufunika kuzipatsa cilango pagulu zisanaweluzidwe. Munthu akakhala nzika ya Roma anali kupatsidwa maufulu ena ake kulikonse kumene angapite mu ufumuwo. Nzika ya Roma inali pansi pa malamulo a boma la Roma, osati malamulo a m’mizinda. Koma akapezeka na mlandu, anali kuvomela kuweluzidwa kulingana na malamulo mu mzindawo. Ngakhale n’conco, anali kukhalabe na ufulu wokadandaula ku khoti la Aroma. Ngati mlandu wake ni waukulu, anali kupatsidwa ufulu wocita apilo kwa wolamulila. Mtumwi Paulo analalikila m’madela ambili a Ufumu wa Roma. Iye anaseŵenzetsa ufulu wake wokhala nzika ya Roma pa zocitika zitatu. Cocitika coyamba cachulidwa mu vesi ino. Cinacitikila ku Filipi pamene iye anauza woweluza wa ku Filipi kuti amuphwanyila ufulu mwa kum’menya.—Kuti mudziŵe zocitika zina ziŵili, onani mfundo zounikila pa Mac. 22:25; 25:11.

DECEMBER 24-30

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 17-18

“Tengelani Citsanzo ca Mtumwi Paulo Polalikila ndi Kuphunzitsa”

nwtsty mfundo zounikila pa Mac. 17:2, 3

anakambilana: Paulo sanawauze cabe uthenga wabwino. Anali kuufotokoza na kuwaonetsa umboni wolembedwa, wa mfundo za m’Malemba ouzilidwa a Ciheberi. Iye sanali kungoŵelenga cabe Malemba; anali kukambapo, ndipo anali kufotokoza malembawo mogwilizana na omvela ake. Liwu la Cigiriki lakuti di·a·leʹgo·mai itanthauza “kukambitsana mopatsana mpata; kukambilana; kulankhulana.” Limapeleka lingalilo la kukambilana ndi anthu. Liwu la Cigiriki limeneli linaseŵenzetsedwanso pa Mac. 17:17; 18:4, 19; 19:8, 9; 20:7, 9.

kusonyeza umboni wolembedwa: Mawu ake eni-eni mu Cigiriki atanthauza “kuika pa mbali.” Izi zionetsa kuti Paulo anali kuyelekezela mosamala maulosi a m’Malemba a Ciheberi okhudza Mesiya, na zocitika za mu umoyo wa Yesu, poonetsa mmene Yesu anakwanilitsila maulosi amenewo.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 17:17

pamsika: Msikawu unali ku mpoto ca kumadzulo kwa Acropolis. Malo a msika wa Atene, (mu Cigiriki, a·go·raʹ) anali maekala 12 kapena kuposelapo. Misika sinali cabe malo ogulilako zinthu na kugulitsa. Koma kunalinso ku cimake kwa zacuma, zandale, na zacikhalidwe. Anthu a ku Atene anali kukonda kukumana kumeneko kuti azikambilana nkhani zozama za akatswili pa maphunzilo.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 17:22, 23

Kwa Mulungu Wosadziŵika: Mawu a Cigiriki akuti A·gnoʹstoi the·oiʹ anali pa mawu olembedwa pa guwa linalake ku Atene. Anthu a ku Atene anali kuopa kwambili milungu cakuti anali kuimangila akacisi na maguwa. Ngakhale milungu ya m’maganizo cabe monga Kuchuka, Kudzicepetsa, Mphamvu, Kukopa, na Cifundo, anali kuipangila maguwa. Mwina cifukwa coopa kuti angasiye mulungu wina na kuti mulunguyo angawapatse masoka, anapatulila guwa lina “Kwa Mulungu Wosadziŵika.” Mwa kumanga guwa limeneli, anthuwo anali kuvomeleza kuti panali Mulungu wina amene sanali kum’dziŵa. Paulo mwaluso anaseŵenzetsa guwa limeneli monga maziko oyambilapo ulaliki wake wowadziŵitsa za Mulungu woona, amene iwo sanali kum’dziŵa.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w08 5/15 peji 32 pala. 5

Mfundo Zazikulu za M’buku la Machitidwe

18:18—Kodi Paulo analumbila ciani? Akatswili ena amati Paulo analumbila zokhala Mnaziri. (Num. 6:1-21) Komabe Baibulo silinena zimene Paulo analumbila. Ndiponso Malemba sanena ngati Paulo anapanga lumbilo lakelo asanatembenuke kapena atatembenuka, kapena ngati iye anali kuyamba kucita zimene analumbilazo kapena kusiya. Mulimonsemo, kupanga lumbilo limeneli sikunali kulakwa.

nwtsty mfundo younikila pa Mac. 18:21

Yehova akalola: Mawu amenewa atsindika za kufunika koganizila cifunilo ca Mulungu pamene ticita zinthu kapena pamene tiganizila kucita zinthu zina. Mtumwi Paulo anali kuikonda ngako mfundo imeneyi. (1 Akor. 4:19; 16:7; Aheb. 6:3) Nayenso wophunzila Yakobo anatilimbikitsa kuti tizikamba kuti: “Yehova akalola, tikhala ndi moyo, ndi kucita zakuti-zakuti.” (Yak. 4:15) Mawu otelo safunika kukambiwa popanda colinga; aliyense amene amakamba mocokela pansi pa mtima kuti “Yehova akalola,” ayenela kuyesetsa kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Yehova. Si nthawi zonse pamene timacita kuchula mawu amenewa. Nthawi zambili timangowakambila mu mtima. Onani mfundo zounikila pa Mac. 21:14; 1 Akor. 4:19; Yak. 4:15.

DECEMBER 31–JANUARY 6

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 19-20

“Mukhale Chelu ndi Kuyang’anila Gulu Lonse la Nkhosa”

w11 6/15 mape. 20-21 pala. 5

“Wetani Gulu la Nkhosa za Mulungu Lomwe Analisiya M’manja Mwanu”

5 Mtumwiyu analemba kuti akulu ayenela ‘kuŵeta gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwawo.’ Iwo amafunikila kuzindikila kuti nkhosazo ndi za Yehova ndi Yesu Khristu. Analembanso kuti akulu adzayankha mlandu cifukwa ca zimene amacita poyang’anila nkhosa za Mulungu. Tayelekezani kuti mnzanu wapamtima wakupemphani kuti mum’sungile ana ake iye akacoka. Kodi simungawasamalile bwino ndiponso kuwapatsa cakudya? Ngati mwana wina wadwala, kodi simungapite naye kucipatala? Mofanana ndi zimenezi, akulu mu mpingo ayenela ‘kuweta mpingo, umene Mulungu anaugula ndi magazi a Mwana wake weni-weni.’ (Mac. 20:28) Akulu amakumbukila kuti nkhosa iliyonse inagulidwa ndi magazi amtengo wapatali a Khristu Yesu. Podziŵa kuti adzayankha mlandu, iwo amadyetsa, kuteteza ndiponso kusamalila gulu la nkhosa.

w13 2/1 peji 31 pala. 15

Akulu Acikhristu Ndi Anchito Anzathu Otipatsa Cimwemwe

15 Akulu amakhala ndi nchito yambili. Nthawi zina usiku, iwo sagona cifukwa codela nkhawa abale ndi alongo, kuwapemphelela kapena kuwathandiza. (2 Akor. 11:27, 28) Komabe iwo amagwila nchito yawo mosangalala ndiponso mwakhama ngati mmene ankacitila Paulo. Iye analembela Akorinto kuti: “Ndidzagwilitsa nchito zinthu zanga zonse ndipo ndidzadzipeleka ndi moyo wanga wonse cifukwa ca miyoyo yanu.” (2 Akor. 12:15) Cifukwa cokonda abale ake, Paulo ankadzipeleka kwambili kuti awathandize. (Ŵelengani 2 Akorinto 2:4; Afil. 2:17; 1 Ates. 2:8) M’pake kuti abale ankamukonda kwambili Paulo.—Mac. 20:31-38.

bt peji 172 pala. 20

“Ndine Woyela pa Mlandu wa Magazi a Anthu Onse”

20 Moyo wa Paulo unali wosiyana kwambili ndi moyo wa anthu amene anadzayamba kutsogolela mpingo, omwe ankangodyela nkhosa masuku pamutu. Paulo ankagwila nchito kuti azipeza yekha zinthu zofunika pamoyo wake n’colinga coti asakhale mtolo wolemela kwa Akhristu mumpingo. Zimene Paulo ankacita pothandiza abale mumpingo, sankazicita n’colinga coti apeze phindu ayi. Conco, Paulo analimbikitsa akulu a ku Efeso kuti nawonso azisonyeza mtima wodzimana. Iye anawauza kuti: “Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukila mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.’”—Mac. 20:35.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

bt peji 161 pala. 11

“Mawu a Yehova Anapitiliza Kufalikila ndi Kugonjetsa Zopinga Zambili”

11 N’kutheka kuti Paulo ankaphunzitsa muholo pasukuluyo tsiku lililonse, kuyambila 11 koloko m’maŵa mpaka 4 koloko madzulo. (Mac. 19:9) Nthawi imeneyi iyenela kuti inali yabwino cifukwa sikunkakhala phokoso lambili ndipo anthu ambili ankakhala ataweluka kunchito zawo kuti apume ndi kudya. Komabe, pa nthawiyi kunja kunkatentha kwambili. Ngati Paulo ankacita zimenezi tsiku ndi tsiku kwa zaka ziŵili zathunthu, ndiye kuti anaphunzitsa kwa maola oposa 3,000, ndipo zimenezi zikutanthauza kuti mwezi uliwonse ankaphunzitsa kwa maola 125. Paulo anagwila nchitoyi mwakhama kwambili ndipo ankasintha ulaliki wake mogwilizana ndi anthu a m’delalo komanso mmene zinthu zinalili pa nthawiyo. Kodi zimenezi zinathandiza bwanji? Nkhaniyi imati: “Onse okhala m’cigawo ca Asia, Ayuda ndi Agiriki omwe, anamva mawu a Ambuye.” (Mac. 19:10) Apa zikuonekelatu kuti Paulo anacitila umboni mokwanila.

bt mape. 162-163 pala. 15

“Mawu a Yehova Anapitiliza Kufalikila ndi Kugonjetsa Zopinga Zambili”

15 Zinthu zocititsa manyazi zimene zinacitikila ana a Sikeva zinacititsa kuti anthu ambili ayambe kuopa Mulungu, ndipo ambili anasiya kukhulupilila mizimu ndipo anakhala Akhristu. Anthu a ku Efeso ankakhulupilila kwambili zamatsenga, ndipo zinthu monga maula, zithumwa komanso mabuku onena zamatsenga zinali zofala kwambili. Koma tsopano anthu ambili a ku Efeso anabweletsa mabuku awo a zamatsenga ndi kuwaocha anthu onse akuona. Iwo anacita zimenezi ngakhale kuti mabukuwo anali okwela mtengo kwambili. Luka analemba kuti: “Conco mawu a Yehova anapitiliza kufalikila ndi kugonjetsa zopinga zambili.” (Mac. 19:17-20) Umenewu unali umboni wamphamvu wosonyeza kuti coonadi cinagonjetsa cinyengo ndiponso ziwanda. Zimene anthu okhulupilikawo anacita zikutipatsa citsanzo cabwino kwambili masiku ano. Ifenso tikukhala m’dziko limene anthu ambili amakhulupilila mizimu. Ngati tadziŵa kuti tili ndi cinacake cimene cikugwilizana ndi zamizimu, tiyenela kuciwocha mwacangu ngati mmene anacitila anthu a ku Efeso. Tisayese dala kukhala ndi ciliconse cokhudzana ndi zamizimu, ngakhale cinthuco citakhala ca ndalama zambili.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani