Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu
JUNE 3-9
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AGALATIYA 4-6
“Nkhani ‘Yophiphilitsila’ Yokhala na Tanthauzo kwa Ife”
it-1 1018 ¶2
Hagara
Malinga na zimene mtumwi Paulo anakamba, Hagara, wochulidwa m’nkhani yophiphilitsilayo anaimila mtundu wa Aisiraeli akuthupi, amene anali m’pangano la Cilamulo na Yehova limene linakhazikitsidwa pa Phili la Sinai. Pangano limeneli linapangitsa ‘ana [ake] kukhala akapolo.’ Popeza kuti anthu a mtunduwo anali ocimwa, analephela kusunga malamulo a pangano limenelo. Pokhala m’pangano limenelo, mtundu wa Aisiraeli sunali womasuka. Unali wocimwa woyenela imfa; inde unali mu ukapolo. (Yoh. 8:34; Aroma 8:1-3) Yerusalemu wa m’nthawi ya Paulo, anafanana ndi Hagara cifukwa Yerusalemu amene anali likulu la mtundu wa Aisiraeli akuthupi, anakhala mu ukapolo pamodzi na ŵana ŵake. Akhristu odzozedwa, ni ŵana ŵa ‘Yerusalemu wakumiyamba,’ mkazi wophiphilitsa wa Mulungu. Mofanana na Sara amene anali mfulu, Yerusalemu ameneyu sanakhaleko mu ukapolo. Monga mmene Isimaeli anazunzila Isaki, nawonso ŵana ŵa Yerusalemu amene anali mu ukapolo anazunza ŵana ŵa ‘Yerusalemu wakumiyamba,’ amene anamasulidwa na Mwanayo. Ngakhale n’conco, Hagara na mwana wake anathamangitsidwa. Zimenezi zinaimila Yehova pamene anakana mtundu wa Aisiraeli akuthupi.—Agal. 4:21-31; onaninso Yoh. 8:31-40.
Khalani ndi Cikhulupililo Cosagwedela mu Ufumu
11 Pangano la Abulahamu linakwanilitsidwa koyamba kwa mbadwa zake, pamene zinaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Komabe, Malemba amaonetsa kuti mbali ina ya pangano limeneli ili na kukwanilitsidwa kwa kuuzimu. (Agal. 4:22-25) Komabe, pa kukwanilitsidwa kwakukulu kwa ulosi umenewu, monga mmene mtumwi Paulo anafotokozela mouzilidwa, mbali yoyamba ya mbewu ya Abulahamu ni Khristu. Ndipo mbali yaciŵili ni Akhristu a 144,000 odzozedwa na mzimu. (Agal. 3:16, 29; Chiv. 5:9, 10; 14:1, 4) Mkazi amene akubeleka mbewu ni ‘Yerusalemu wakumiyamba’ amene ni gawo lakumwamba la gulu la Mulungu, la angelo onse okhulupilika. (Agal. 4:26, 31) Malinga ndi pangano la Abulahamu, mbewu ya mkazi idzabweletsa madalitso pa mtundu wa anthu.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w09 4/1 13
Kodi Mukudziŵa?
N’cifukwa ciani Yesu popemphela anachula Yehova kuti “Abba, Atate”?
Mawu a Cialamu akuti ʼab·baʼʹ amatanthauza “Atate.” Mawuwa amapezeka malo atatu m’Baibulo ndipo anagwilitsidwa nchito m’pemphelo pochula Atate wakumwamba, Yehova. Kodi mawuwa anali kutanthauza ciani?
Buku lina limati: “M’nthawi ya Yesu, mawu akuti ʼabbāʼ anali kugwilitsidwa nchito kwambili ndi ana poitana bambo awo mwaulemu ndiponso mwacikondi.” (The International Standard Bible Encyclopedia) Mawuwa anali ena mwa mawu oyamba amene mwana anali kulankhula pophunzila kulankhula. Yesu anagwilitsa nchito mawuwa popemphela kwa Atate ake mocokela pansi pamtima. Ali m’munda wa Getsemane patangotsala maola ocepa kuti aphedwe, Yesu popemphela anachula Yehova kuti, “Abba, Atate.”—Maliko 14:36.
Buku lija limanenanso kuti: “Mawu ochulila Mulungu akuti ʼAbbāʼ sapezeka kaŵili-kaŵili m’mabuku a Ayuda a m’nthawi ya ulamulilo wa Agiriki ndi Aroma. Izi zinali conci cifukwa iwo anali kuona kuti n’kupanda ulemu kuchula Mulungu ndi mawu amenewa.” Komabe bukuli limanenanso kuti; “Yesu . . . anagwilitsa nchito mawu amenewa m’pemphelo pofuna kutsimikizila kuti iye amagwilizana kwambili ndi Mulungu.” Mawu akuti “Abba” amapezekanso m’mabuku aŵili a m’Baibulo omwe analembedwa ndi mtumwi Paulo ndipo amasonyeza kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi anali kuchula mawuwa popemphela.—Aroma 8:15; Agalatiya 4:6.
w10 11/1 15
Kodi Mudziŵa?
Kodi mtumwi Paulo anali kutanthauza ciani ponena kuti thupi lake linali ndi “zipsela za cizindikilo ca kapolo wa Yesu?”—Agalatiya 6:17.
▪ N’kutheka kuti anthu a m’nthawi ya atumwi anaganiza zinthu zingapo zosiyanasiyana atamva mawu a Paulowo. Mwacitsanzo, kale akaidi ogwidwa ku nkhondo, anthu amene aba zinthu m’kacisi komanso akapolo amene athaŵa ambuyawo anali kudindidwa cizindikilo pogwilitsa nchito citsulo cotentha ndi colinga cakuti azitha kuwazindikila. Anthu anali kuona kuti kuikidwa cizindikilo coteleci cinali cinthu cocititsa manyazi.
Komabe sinthawi zonse pamene munthu wodindidwa cizindikilo anali kuonedwa kuti ndi wonyozeka. Anthu ambili m’nthawi imeneyo anali kudindidwa cizindikilo cosonyeza mtundu wawo kapena cipembedzo cawo. Malinga ndi zimene buku lina lotanthauzila mawu a m’Baibulo linanena, “Pofuna kupeleka ulemu kwa milungu yonyenga Hadadi ndi Atarigatisi, Asiriya anali kudzidinda cizindikilo pamkono kapena m’khosi . . . Ndiponso anthu otsatila mulungu Diyonisiyo pathupi lawo anali kukhala ndi cizindikilo ca tsamba la mtengo winawake woyanga.”—Theological Dictionary of the New Testament.
Anthu ena oikila ndemanga nkhani za m’Baibulo amaganiza kuti Paulo anali kunena za zipsela zimene anali nazo cifukwa ca nkhanza zimene ena anamucitila pa maulendo ake aumishonale. (2 Akorinto 11:23-27) Koma n’kuthekanso kuti Paulo sanali kutanthauza zipsela zeni-zeni, koma khalidwe limene anali, limene linali kumudziŵikitsa kuti ndi Mkhristu.
JUNE 10-16
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AEFESO 1-3
“Colinga ca Dongosolo la Mulungu”
it-2 837 ¶4
Cinsinsi Copatulika
Ufumu wa Mesiya. M’makalata ake, Paulo anapeleka cithunzi cokwanila cokhudza kuululidwa kwa cinsinsi copatulika ca Khristu. Pa Aefeso 1:9-11, iye anakamba kuti Mulungu anaulula “cinsinsi copatulika” ca cifunilo cake. Anati: “Cinsinsico n’cogwilizana ndi zokomela mwiniwakeyo ndiponso zimene anafuna mumtima mwake kuti akakhazikitse dongosolo lake, ikadzatha nyengo yonse ya nthawi zoikidwilatu. Dongosolo limenelo ndilo kusonkhanitsanso zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi. Inde, kuzisonkhanitsanso mwa iye. Mogwilizana ndi iyeyo tinaikidwa kukhala odzalandila colowa, pakuti anatisankhilatu mwa kufuna kwake, iye amene amayendetsa zinthu zonse mogwilizana ndi cifunilo cake.” Ufumu wa Mulungu wa Mesiya ni mbali ya “Cinsinsi copatulika” cimeneci. “Zinthu zakumwamba,” zimene Paulo anali kukambapo, ni anthu oyembekezela kulandila colowa ca Ufumu wa Kumwamba wolamulidwa na Khristu. Ndipo “zinthu zapadziko” ni anthu amene adzakhala padziko lapansi mu Ufumuwo. Yesu anauza ophunzila ake kuti cinsinsi copatulika, ciyenela kukhala cokhudzana na Ufumuwo pamene anati: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikila cinsinsi copatulika ca ufumu wa Mulungu.”—Maliko 4:11.
w12 7/15 27-28 ¶3-4
Yehova Akusonkhanitsa Banja Lake
3 Yehova amacita zinthu mogwilizana ndi colinga cake. Conco pa nthawi yake, Mulungu anakhazikitsa “dongosolo” loti agwilizanitse onse a m’banja lake. (Ŵelengani Aefeso 1:8-10.) Dongosolo limeneli lili ndi mbali ziŵili. Mbali yoyamba ndi yokonzekeletsa Akhristu odzozedwa kuti akakhale kumwamba n’kumatsogoleledwa ndi Yesu Khristu. Mbali imeneyi inayamba pa Pentekosite m’caka ca 33 C.E. Pa nthawiyi, Yehova anayamba kusonkhanitsa anthu oti adzalamulile limodzi ndi Yesu kumwamba. (Mac. 2:1-4) Cifukwa ca nsembe ya dipo ya Khristu, Mulungu amaona kuti odzozedwa ndi olungama ndiponso oyenelela moyo. Odzozedwawa amadziŵa kuti iwowo tsopano ndi “ana a Mulungu.”—Aroma 3:23, 24; 5:1; 8:15-17.
Mbali yaciŵili ndi yokonzekeletsa anthu amene adzakhale m’Paradaiso padziko lapansi motsogoleledwa ndi Ufumu wa Mesiya. Anthu a “khamu lalikulu” adzakhala oyamba kukhala m’Paradaiso. (Chiv. 7:9, 13-17; 21:1-5) Mu Ulamulilo wa Zaka 1,000, anthu mabiliyoni ambili adzaukitsidwa kuti adzakhale nawo m’Paradaiso. (Chiv. 20:12, 13) Anthuwa akadzaukitsidwa m’pamene zidzaonekele kwambili kuti ndife ogwilizana. Ku mapeto kwa zaka 1,000 zimenezi, “zinthu zapadziko lapansi,” kapena kuti anthu okhala padziko, adzayesedwa komaliza. Anthu onse okhulupilika nawonso adzakhala “ana a Mulungu” padziko lapansi.—Aroma 8:21; Chiv. 20:7, 8.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
w13 3/1 28 ¶15
Musalole Ciliconse Kukulepheletsani Kupeza Ulemelelo
15 Tikamayesetsa kupilila pocita zimene Yehova amafuna, timathandiza anthu ena kupezanso ulemelelo. Paulo analembela mpingo wa ku Efeso kuti: “Ndikukupemphani kuti musabwelele m’mbuyo poona masautso angawa, amene ndikukumana nawo cifukwa ca inu, pakuti akutanthauza ulemelelo kwa inu.” (Aef. 3:13) Kodi zinatheka bwanji kuti masautso a Paulo ‘atanthauze ulemelelo’ kwa Aefeso? Paulo anali wofunitsitsa kuwatumikilabe ngakhale kuti anali kukumana ndi mayeselo. Izi zinathandiza Aefeso kuzindikila kuti mwayi wawo wotumikila Mulungu unali wamtengo wapatali kwambili. Ngati Paulo akanafooka, iwo akanaona kuti ubwenzi wawo ndi Yehova, utumiki wawo komanso ciyembekezo cawo n’zopanda nchito. Koma kupilila kwa Paulo kunasonyeza kuti Cikhristu ndi cofunika kwambili ndipo munthu ayenela kulolela kutaya ciliconse kuti akhale wophunzila wa Yesu.
cl 299 ¶21
“Kuzindikila Cikondi ca Khristu”
21 Mawu acigiriki omasulidwa kuti “kuzindikila” amatanthauza kuti kudziŵa “mwa zocita, kupyolela mu zimene zikukucitikila.” Tikakhala n’cikondi monga analili Yesu—kudzipeleka mopanda dyela kuti tithandize ena, kuwacitila cifundo pamene akusoŵeka zinthu zina, kuwakhululukila kucokela pansi pamtima—m’pamene tidzamvetsetsadi maganizo ake. M’njila imeneyi, ‘timazindikila cikondi ca Khristu cakuposa mazindikilidwe’ mwa zimene zikuticitikila. Ndipo tisaiŵale kuti pamene tifanana kwambili ndi Khristu, m’pamenenso timayandikana zedi ndi yemwe Yesu anamutsanzila bwino kwambili, Mulungu wathu wacikondi, Yehova.
JUNE 17-23
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AEFESO 4-6
“Valani Zida Zonse Zankhondo Zocokela kwa Mulungu”
Acicepele Cilimikani Polimbana ndi Mdyelekezi
MTUMWI Paulo anayelekezela umoyo wathu wacikhristu na asilikali amene akumenyana moyandikana kwambili. Nkhondo imene tikumenya ni yauzimu osati yakuthupi. Ndipo adani athu Satana na ziŵanda, ni amphamvu. Iwo ni aciyambakale ndiponso ni akatswili pa nkhondoyi. Conco, tingaone kuti n’zosatheka kupambana pa nkhondoyi. Maka-maka Akhristu acicepele ndiwo amaoneka kukhala osatetezeka. Koma kodi iwo angapambane pa nkhondo yolimbana na angelo oipa? Inde, angapambane, ndipo akupambana kumene! Nanga n’ciani cimawathandiza? Iwo ‘akupitiliza kupeza mphamvu kucokela kwa Ambuye.’ Kuwonjezela pamenepo, amavala zovala zomenyela nkhondo. Molingana ndi asilikali ophunzitsidwa bwino, iwo ‘amavala zida zonse zankhondo zocokela kwa Mulungu.’—Ŵelengani Aefeso 6:10-12.
Acicepele Cilimikani Polimbana ndi Mdyelekezi
4 Mofananamo, coonadi cimene timaphunzila m’Mawu a Mulungu cimatiteteza ku ziphunzitso zabodza zimene zikhoza kutiwononga mwauzimu. (Yoh. 8:31, 32; 1 Yoh. 4:1) Ngati timacikonda kwambili coonadi, zimakhala zosavuta kunyamula “codzitetezela pacifuwa,” kutanthauza kutsatila miyezo yolungama ya Mulungu mu umoyo wathu. (Sal. 111:7, 8; 1 Yoh. 5:3) Kuwonjezela apo, kumvetsetsa bwino mfundo za coonadi ca Mawu a Mulungu, kudzatithandiza kukhala wokonzeka kuteteza molimba mtima coonadi kwa otsutsa.—1 Pet. 3:15.
7 Ndithudi! Ici n’cizindikilo coyenelela kwambili coonetsa mmene miyezo yolungama ya Yehova imatetezela mtima wathu wophiphilitsa. (Miy. 4:23) Msilikali sangasinthanitse codzitetezela pacifuwa copangiwa na citsulo colimba n’kutenga cina copangiwa na citsulo cosalimba. Na ise n’cimodzi-modzi. Sitifunika kusinthanitsa miyezo yolungama ya Yehova na miyezo yathu. Sitiyenela kudalila nzelu zathu cifukwa sizingatithandize kukhala otetezeka. (Miy. 3:5, 6) M’malomwake, mofanana ndi msilikali amene anali kuonetsetsa kuti tunsimbi twa codzitetezela pa cifuwa n’togwila bwino, tifunika kuonetsetsa kuti mfundo za Yehova ni zozikika mozama mu mtima mwathu.
10 Nsapato zimene asilikali aciroma anali kuvala zinali zopita nazo ku nkhondo. Koma nsapato zophiphilitsa zimene Akhristu amavala, zimawathandiza polalikila uthenga wa mtendele. (Yes. 52:7; Aroma 10:15) Ngakhale n’conco, Mkhristu amafunika kulimba mtima kuti alalikile pamene mpata wapezeka. Mnyamata wina wa zaka 20, dzina lake Bo, anati: “N’nali kuyopa kulalikila anzanga a m’kilasi. N’nali kucita manyazi. Koma niona kuti panalibe cifukwa cocitila manyazi. Lomba, nimakondwela kulalikila anzanga.”
Acicepele Cilimikani Polimbana ndi Mdyelekezi
13 Mivi ina “yoyaka moto” imene Satana angakuponyeleni ndiyo kufalitsa mabodza akuti Yehova sakuonani monga ofunika ndiponso sakukondani. Ida wa zaka 19, wakhala akuvutika na maganizo odziona monga wosafunika. Iye anati: “Nthawi zambili, nimaona ngati kuti Yehova ali nane patali ndipo safuna kukhala Mnzanga.” Kodi Ida amacita ciani polimbana na vuto imeneyi? Iye anati: “Misonkhano imalimbitsa kwambili cikhulupililo canga. Kale, n’nali kungopezeka pa misonkhano koma osayankhapo, poganiza kuti palibe aliyense amene angamvetsele zokamba zanga. Koma lomba nimakonzekela misonkhano na kuyesetsa kuyankhapo, kaŵili kapena katatu. Zimanivuta, koma nimamvela bwino kwambili nikayankhapo. Komanso, abale na alongo amanilimbikitsa maningi. Conco, nthawi zonse pamene nicoka ku misonkhano, nimakhala wotsimikiza kuti Yehova amanikonda.”
16 Monga mmene cisote cimatetezela mutu na ubongo wa msilikali, “ciyembekezo cacipulumutso” cimateteza maganizo athu, na kutithandiza kuti tiziganiza bwino. (1 Ates. 5:8; Miy. 3:21) Ciyembekezo cimatithandiza kuikabe maganizo athu pa malonjezo a Mulungu. Cimatithandizanso kuona mavuto moyenelela. (Sal. 27:1, 14; Mac. 24:15) Koma kuti ‘cisote’ cathu cimeneci cititeteze bwino, tifunika kucivala osati kucinyamula kumanja.
20 Paulo anakamba kuti Mawu a Mulungu amene Yehova watipatsa ali monga lupanga. Komabe, tifunika kuphunzila mmene tingaseŵenzetsele mwaluso lupanga limeneli poikila kumbuyo zikhulupililo zathu, kapena powongolela maganizo athu. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 2:15) Kodi tingakulitse bwanji luso la mmene timaseŵenzetsela Mawu a Mulungu? Sebastian, wa zaka 21, anati: “Pamene niŵelenga Baibo, nimalemba vesi imodzi m’caputa iliyonse, na kuika pamodzi mavesi anga a pamtima. Izi zathandiza kuti maganizo anga akhale ogwilizana kwambili na maganizo a Yehova.” Komanso Daniel, amene tamuchula kuciyambi, anati: “Poŵelenga Baibo, nimasankha mavesi amene niona kuti adzakhala othandiza kwa anthu amene nimakumana nawo mu ulaliki. Naona kuti anthu amamvetsela kwambili akazindikila kuti umaikonda Baibo komanso umayesetsa kuwathandiza.”
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-1 1128 ¶3
Ciyelo
Mzimu woyela. Mphamvu ya Yehova yogwila nchito kapena kuti mzimu, ni imene amaseŵenzetsa pokwanilitsa colinga cake. Mzimuwu ni woyela, wosadetsedwa, ndiponso wopatulika. Inde, Mulungu anaupatula kuti aziuseŵenzetsa moyenelela. Conco m’pomveka kuti umachedwa “mzimu woyela” komanso kuti “Mzimu wa ciyelo.” (Sal. 51:11; Luka 11:13; Aroma 1:4 [Buku Lopatulika]; Aef. 1:13) Mzimu woyela ukamagwila nchito mwa munthu, umamusonkhezela kucita zinthu mwaciyelo. Kucita conyansa kapena coipa ca mtundu uliwonse kumatsutsana na mphamvuyo kapena kuti kumamvetsa “cisoni mzimu woyela” umenewo. (Aef. 4:30) Ngakhale kuti mzimu woyela si munthu, umaonetsa umunthu woyela wa Mulungu. Conco n’zotheka mzimuwo kucita “cisoni.” Kukhala na cizoloŵezi cocita zoipa za mtundu uliwonse kumazimitsa “moto wa mzimu.” (1 Ates. 5:19) Munthu akapitiliza kucita zoipazo, m’kupita kwa nthawi, mzimu woyela wa Mulungu ‘umakhumudwa,’ ndipo izi zingacititse kuti Mulungu asinthe n’kukhala mdani wa munthu wopandukayo. (Yes. 63:10) Munthu amene amamvetsa cisoni mzimu woyela angafike mpaka pounyoza, chimo limene Yesu Khristu anakamba kuti silidzakhululukidwa kaya m’nthawi ino kapena imene ikubwelayo.—Mat. 12:31, 32; Maliko 3:28-30.
it-1 1006 ¶2
Umbombo
Umaonekela m’Zocita. Umbombo umaonekela m’zocita za munthu. Zocitazo zimaonetsa poyela cilako-lako cake colakwika cosalamulilika. Wolemba Baibo Yakobo, anakamba kuti cilako-lako coipa cikatenga pakati, cimabala chimo. (Yak. 1:14, 15) Conco, munthu waumbombo tingamudziŵe mwa zocita zake. Mtumwi Paulo anakamba kuti munthu waumbombo ni wolambila mafano. (Aef. 5:5) Cifukwa colaka-laka kwambili cinthu cimene afuna, munthu waumbombo amapanga cinthuco kukhala mulungu wake. Amaika cinthuco patsogolo pa utumiki na kulambila kwake Mlengi.—Aroma 1:24, 25.
JUNE 24-30
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AFILIPI 1-4
“Musamade Nkhawa ndi Kanthu Kalikonse”
“Mtendele wa Mulungu . . . Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”
10 N’ciani cingatithandize kuti tisamade nkhawa ndi ciliconse ndi kuti tizikhala na “mtendele wa Mulungu”? Mawu amene Paulo analembela Akhristu a ku Filipi aonetsa kuti cimene cingacepetse nkhawa ni pemphelo. Conco, tikakhala na nkhawa, tifunika kumuuza Yehova nkhawa zathuzo m’pemphelo. (Ŵelengani 1 Petulo 5:6, 7.) Tizipemphela kwa Yehova ndi cikhulupililo conse, podziŵa kuti iye amasamala za ife. Tizipeleka mapemphelo oyamikila pa zabwino zimene amaticitila. Cidalilo cathu mwa Yehova cidzakula ngati tikumbukila mfundo yakuti iye angathe “kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza.”—Aef. 3:20.
“Mtendele wa Mulungu . . . Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”
7 Mosakayikila, pamene abale a ku Filipi anaŵelenga kalata imene Paulo anawalembela, anakumbukila mavuto amene iye anakumana nawo, ndiponso zinthu zosayembekezeleka zimene Yehova anamucitila. Kodi pamenepa Paulo anali kuwaphunzitsa mfundo yanji? Mfundo yakuti sanafunike kuda nkhawa, koma anafunika kupemphela kuti alandile mtendele wa Mulungu. Paulo anawauza kuti “mtendele wa Mulungu . . . umaposa kuganiza mozama kulikonse.” Kodi zimenezi zitanthauza ciani? Pomasulila mawu amenewa, omasulila ena amati, mtendele wa Mulungu “umaposa zonse zimene tingayembekezele,” kapena kuti “umaposa nzelu zonse zimene munthu angakhale nazo.” Pamenepa, tinganene kuti Paulo anali kukamba kuti “mtendele wa Mulungu” ni wosangalatsa kwambili kuposa mmene tingaganizile. N’zoona kuti nthawi zina tingaone kuti mavuto athu sangathe. Koma Yehova amadziŵa mmene angawathetsele, ndipo angatithandize m’njila imene sitinali kuyembekezela.—Ŵelengani 2 Petulo 2:9.
“Mtendele wa Mulungu . . . Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse”
16 Kodi timapindula bwanji ngati tili na “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse”? Baibo imakamba kuti mtendelewo ‘udzateteza mitima yathu ndi maganizo athu mwa Khristu Yesu.’ (Afil. 4:7) Mawu a cinenelo coyambilila amene anatembenuzidwa kuti “kuteteza,” anali kugwilitsidwa nchito pokamba za asilikali. Anali kutanthauza gulu la asilikali amene anali kutumidwa kuti akateteze mzinda wokhala na mpanda wolimba kwambili. Filipi unali umodzi mwa mizinda yaconco. Anthu a ku Filipi anali kugona mwamtendele usiku, cifukwa anali kudziŵa kuti asilikali akulonda pa zipata za mzindawo. Mofananamo, ifenso tikakhala na “mtendele wa Mulungu,” mitima na maganizo athu zimakhala m’malo. Timadziŵa kuti Yehova amatikonda ndipo amafuna kuti zinthu zizitiyendela bwino. (1 Pet. 5:10) Kudziŵa zimenezi kumatithandiza kuti tisakhale na nkhawa kwambili, ndi kuti tisafooke tikakumana ndi mavuto.
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu
it-2 528 ¶5
Nsembe
Nsembe ya cakumwa. Nsembe ya cakumwa inali kupelekedwa pamodzi na nsembe zina, maka-maka kucokela pa nthawi imene Aisiraeli analoŵa mu Dziko Lolonjezedwa. (Num. 15:2, 5, 8-10) Nsembeyi inali vinyo (“moŵa”) ndipo anali kuithila pa guwa lansembe. (Num. 28:7, 14; yelekezelani na Eks 30:9; Num. 15:10). Mtumwi Paulo analembela Akhristu a ku Filipi kuti: “Ngakhale kuti ndikudzipeleka ngati nsembe yacakumwa imene ikuthilidwa pansembe ndi pa nchito yotumikila anthu imene cikhulupililo cakupatsani, ndine wokondwa.” Apa Paulo anaseŵenzetsa mawu ophiphilitsa akuti nsembe ya cakumwa, pofuna kuonetsa kuti anali wofunitsitsa kudzipeleka kuti atumikile Akhristu anzake. (Afil. 2:17) Paulo atatsala pafupi kumwalila, analembela Timoteyo kuti: “Ine ndayamba kale kukhuthulidwa ngati nsembe ya cakumwa, ndipo nthawi yakuti ndimasuke yatsala pang’ono kukwana.”—2 Tim. 4:6.
w07 1/1 26-27 ¶5
“Kuuka Koyamba” Kuli M’kati Panopa!
5 Kenaka, anthu odzozedwa a “Isiraeli wa Mulungu” ayenela kukakumana ndi Ambuye Yesu Khristu mu ulemelelo wa kumwamba, kumene ‘azikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.’ (Agalatiya 6:16; 1 Atesalonika 4:17) Kuuka kumeneku kumachedwa “kuuka koyambilila” kapena “kuuka koyamba.” (Afilipi 3:10, 11; Chivumbulutso 20:6) Kuuka kumeneko kukadzatha, idzakhala nthawi yoti anthu mamiliyoni ambili aukitsidwile pa dziko lapansi n’ciyembekezo cokhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso. Conco, kaya ciyembekezo cathu n’cakumwamba kapena n’capadziko lapansi, tili ndi cidwi kwambili ndi “kuuka koyamba.” Kodi kuuka kumeneku ndi kotani? Kodi kudzacitika liti?