BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
Ndinali wodzikonda
CAKA COBADWA: 1951
DZIKO: GERMANY
MBILI YANGA: WONYADA, WAMTIMA WOSAFUNA KUUZIDWA ZOCITA
KUKULA KWANGA:
Pamene ndinali mwana kwambili, banja langa linali kukhala pafupi ndi mzinda wa Leipzig, Kum’mawa kwa Germany capafupi ndi malile a mayiko a Czechoslovakia ndi Poland. Ndili ndi zaka 6, banja lathu linasamukila ku Brazil kenako ku Ecuador cifukwa ca nchito ya atate.
Ndili ndi zaka 14, ananditumiza kusukulu ya boding’i ku Germany. Popeza kuti makolo anga anali kukhala ku South America, ndinali kuzisamalila ndekha. Ndinali wozidalila kwambili. Ndinalibe nazo nchito kuti kaya anthu akukhudzidwa bwanji ndi zocita zanga.
Pamene ndinali ndi zaka 17, makolo anga anabwelela ku Germany. Poyamba ndinali kukhala pakhomo pao. Koma cifukwa cokhala ndi mzimu wosafuna kuuzidwa zocita, zinandivuta kugwilizana ndi banja langa. Ndinacoka panyumba ndili ndi zaka 18.
Ndinayamba kufufuza colinga ca moyo, ndipo zimenezo zinandipangitsa kulephela kukhazikika pamalo amodzi. Nditaona zikhalidwe zosiyanasiyana ndi mabungwe osiyanasiyana, ndinakhala wotsimikiza mtima kuti cinthu cabwino kwambili cimene ndingacite paumoyo wanga ndi kuzungulila dziko lapansili lokongola, anthu asanaliononge.
Ndinasamuka kucoka ku Germany, ndi kupita ku Africa pa njinga yamoto. Koma posapita nthawi, ndinabwelelanso ku Ulaya kukakonzetsa njinga yamoto imeneyo. Nthawi yocepa, ndinafika m’mbali mwa nyanja ku Portugal. Ndinaganiza zosiya kuyenda pa njinga yanga ya moto ndikuyamba kuyenda pabwato.
Ndinagwilizana ndi gulu la acinyamata amene anali kukonzekela kuolokela tsidya lina la Nyanja ya Atlantic. Pakati pa acinyamatawo panali mtsikana wina dzina lake Laurie, amene anadzakhala mkazi wanga. Coyamba tinafika m’zilumba za m’nyanja za Caribbean. Ndiyeno titakhala kwa nthawi yocepa ku Puerto Rico, tinabwelela ku Ulaya. Tinali kufunitsitsa kupeza boti loyendela mphepo kuti tilisandutse kukhala boti la injini lakuti tizikhalamo. Koma pambuyo poifufuza kwa miyezi itatu cabe, panabwela za mwadzidzidzi zimene zinasokoneza nchitoyo. Ndinalembedwa nchito ya usilikali ku Germany.
Ndinali m’gulu la Asilikali apanyanja a ku Germany kwa miyezi 15. Mkati mwa nthawi imeneyi m’pamene ine ndi Laurie tinakwatilana, ndipo tinali kufuna kupitiliza umoyo wathu wozungulila dziko. Ndisanaloŵe usilikali, ine ndi mkazi wanga tinagula boti lopulumutsila anthu limene linali loonongeka. Pamene ndinali kugwila nchito ya usilikali, pang’onopang’ono tinayamba kusintha boti loonongekalo kuti likhale boti laling’ono la injini. Colinga cathu cinali kukhala mu botilo ndi kuligwilitsila nchito pozungulila dziko lapansi lokongolali. Nditasiya nchito ya usilikali, koma ndisanamalize kukonza botilo, ndi pamene ndinakumana ndi Mboni za Yehova ndi kuyamba kuphunzila Baibulo.
MMENE BAIBULO LINASINTHILA UMOYO WANGA:
Poyamba sindinali kuona ubwino wopanga masinthidwe alionse paumoyo wanga. Ndinali nditakwatila mkazi amene ndinali kukhala naye, ndipo ndinali nditasiya kale kukoka fodya. (Aefeso 5:5) Ndinali kuganiza kuti kuona cilengedwe codabwitsa ca Mulungu ndi kumene kunali kofunika kwambili. Ndiye cifukwa cake ine ndi mkazi wanga tinayamba kuzungulila dziko lapansi.
Kunena zoona ndinali kufunikila kupanga masinthidwe aakulu, makamaka umunthu wanga. Popeza ndinali wonyada kwambili ndipo sindinali kufuna kuuzidwa zocita, ndinatengeka kwambili ndi maluso anga ndi zinthu zina zimene ndinali kucita. Ndinali kungoganizila za ine ndekha basi.
Tsiku lina ndinaŵelenga ulaliki wochuka wa Yesu wa pa Phili. (Mateyo macaputala 5-7) Poyamba sindinali kumvetsetsa zimene Yesu anatanthauza pamene anakamba kuti “odala.” Mwacitsanzo, iye anakamba kuti odala ndi anthu amene ali ndi njala ndi ludzu. (Mateyu 5:6) Ndinali kudabwa kuti munthu angakhale bwanji wodala pamene ali wosoŵa. Pamene ndinapitiliza kuphunzila Baibulo, ndinazindikila kuti tonse ndife osoŵa mwa kuuzimu, ndi kuti tiyenela kukhala odzicepetsa kuti tipeze zosoŵa zathu. Mwacitsanzo, Yesu anakamba kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu, cifukwa ufumu wakumwamba ndi wao.”—Mateyu 5:3.
Titayamba kuphunzila Baibulo ku Germany, ine ndi Laurie tinasamukila ku France, patapita nthawi tinasamukila ku Italy. Kulikonse kumene tinali kusamukila, tinali kupeza a Mboni za Yehova. Ndinacita cidwi kwambili ndi cikondi ceniceni cimene cili pakati pao ndiponso mgwilizano wao. Ndinazindikila kuti a Mboni amapangadi gulu lonse la abale padziko lapansi. (Yohane 13:34, 35) M’kupita kwa nthawi, ine ndi Laurie tinabatizidwa kukhala a Mboni za Yehova.
Nditabatizidwa, ndinapitilizabe kusintha umunthu wanga. Ine ndi Laurie tinayamba ulendo wopita ku Africa, m’mphepete mwa nyanja, kenako kuoloka Nyanja ya Atlantic kupita ku United States. Titayenda makilomita ambilimbili, tinafika pakati penipeni pa nyanja. Tili aŵiliŵili m’boti laling’ono pakati pa nyanjapo, ndi pamene ndinazindikila kuti ndine wamng’ono kwambili kuyelekezela ndi Mlengi wathu wamkulu. Popeza ndinalibe zocita zambili pakati pa nyanjapo, ndinagwilitsila nchito nthawi yanga yambili kuŵelenga Baibulo. Ndinalimbikitsidwa kwambili ndi nkhani zokhudza umoyo wa Yesu ali pa dziko lapansi. Iye anali munthu wangwilo ndipo anali ndi maluso abwino kwambili kuposa munthu wina aliyense, koma sanali wodzikweza. Sanali kuganizila za iye yekha basi, koma anali kuganizila kwambili za Atate wake wakumwamba.
Ndinazindikila kuti Ufumu wa Mulungu uyenela kukhala cinthu cofunika kwambili m’moyo wanga
Pamene ndinali kusinkhasinkha za citsanzo ca Yesu, ndinazindikila kuti Ufumu wa Mulungu uyenela kukhala cinthu cofunika kwambili m’moyo wanga, m’malo mosakaniza zinthu za ufumu ndi zinthu zina zimene ndinali kukonda. (Mateyu 6:33) Pamene ine ndi Laurie tinafika ku United States, tinaganiza zoleka kuzungulila dziko ndi kukhazikika kumeneko n’colinga cakuti tiike patsogolo zinthu zokhudza kulambila.
MAPINDU AMENE NDAPEZA:
Pamene ndinali ndi mzimu wodzikonda, sindinali kukhala wotsimikiza popanga zosankha. Koma panopa, ndapeza gwelo labwino kwambili la nzelu zonditsogolela. (Yesaya 48:17, 18) Tsopano umoyo wanga wakhala ndi colinga cimene ndinalibe poyamba. Colingaco ndi kulambila Mulungu ndi kuthandiza ena kuphunzila za iye.
Ukwati wathu wakhala wolimba kwambili cifukwa tonse aŵili timagwilitsila nchito malangizo a m’Baibulo. Mulungu anatidalitsanso ndi mwana wamkazi wokongola amenenso amadziŵa Yehova ndi kum’konda.
Si kuti umoyo wathu nthawi zonse wakhala wopanda mavuto. Koma ndi thandizo la Yehova, ndife okonzeka kupilila ndi kupitiliza kumukhulupilila.—Miyambo 3:5, 6.