LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr20 November
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
  • Tumitu
  • NOVEMBER 2-8
  • NOVEMBER 9-​15
  • NOVEMBER 16-​22
  • NOVEMBER 23-​29
  • NOVEMBER 30–DECEMBER 6
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2020
mwbr20 November

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

NOVEMBER 2-8

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | EKISODO 39-​40

“Mose Anatsatila Malangizo Mosamala”

w11 9/15 27 ¶13

Kodi Mumadziŵika Ndi Yehova?

13Mosiyana na Kora, Mose anali “munthu wofatsa kwambili kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:⁠3) Iye anaonetsa kuti anali wofatsa ndiponso wodzicepetsa potsatila malangizo a Yehova nthawi zonse. (Eks. 7:6; 40:16) M’Baibo, palibe paliponse pamene timaŵelenga posonyeza kuti Mose anali kukayikila mmene Yehova amayendetsela zinthu, kapena kunyansidwa na kutsatila malangizo a Yehova. Mwacitsanzo, Yehova analamula Mose kuti apange cihema copatulika. Anamufotokozela cina ciliconse kuphatikizapo zinthu zing’ono-zing’ono monga mtundu wa ulusi ndiponso ciŵelengelo ca zingwe zopota zokolekamo ngowe zogwilitsa nchito polumikiza nsalu za cihema. (Eks. 26:​1-6) Ngati woyang’anila m’gulu la Mulungu amapeleka malangizo ambili-mbili zikhoza kukutopetsani. Yehova ni woyang’ayanila wabwino kwambili amene amagaŵila ena zocita ndiponso kukhulupilila atumiki ake. Ngati akupeleka malangizo ambili-mbili amacita zimenezo pa zifukwa zomveka. Mutha kuona kuti Mose sanakhumudwe cifukwa cakuti Yehova anapeleka malangizo ambili-mbili. Iye sanaganize kuti Yehova akumupeputsa kapena kumuphela ufulu woonetsa luso lake. M’malomwake, Mose anaonetsetsa kuti ogwila nchitowo “anacita zonse” potsatila malangizo amene Mulungu anapeleka. (Eks. 39:32) Apa anaonetsa kudzicepetsa kwambili. Mose anali kudziŵa kuti nchitoyo ni ya Yehova ndipo iye anali kungogwilitsidwa nchito kuti nchitoyo itheke.

w05 7/15 27 ¶3

Kodi Ndinu Wokhulupilika M’zinthu Zonse?

3Monga mtumiki, Mose anali wokhulupilika, imatelo Baibo pa Aheberi 3:⁠5. N’cifukwa ciani Mose anachedwa wokhulupilika? Pomanga cihema, “Mose anacita zonse monga mmene Yehova anamulamulila. Anacitadi momwemo.” (Ekisodo 40:16) Monga olambila Yehova, timaonetsa kukhulupilika mwa kum’tumikila momvela. Zimenezi ziphatikizapo kukhala wokhulupilika kwa Yehova tikakumana na mayeselo ovuta ndiponso aakulu. Komabe, kupambana pa mayeselo aakulu si umboni wokha wa kukhulupilika. Yesu anati: “Munthu wokhulupilika pa cinthu cacing’ono alinso wokhulupilika pa cinthu cacikulu, ndipo munthu wosalungama pa cinthu cacing’ono alinso wosalungama pa cinthu cacikulu.” (Luka 16:10) Tiyenela kukhala okhulupilika ngakhale pa nkhani zimene zimaoneka zazing’ono.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-2 884 ¶3

Cikopa ca Katumbu

Mmene Aisiraeli anali kucipezela. Ngati nyama yochedwa taʹchash imene Baibo imachula, ni mtundu wa katumbu, pangabuke funso lakuti, ‘Kodi Aisiraeli anakwanitsa bwanji kupeza zikopa za akatumbu?’ Akatumbu amakonda kupezeka m’madela ozizila kwambili a kumpoto na kum’mwela kwa dziko lapansi. Ngakhale n’conco, pali akatumbu ena amene amakonda kukhala m’madela otenthelapo. Masiku ano, akatumbu ocepa opanda makutu akali kupezeka m’madela ena a Nyanja ya Mediterranean, komanso m’nyanja zina za m’madela otentha. Pa zaka zambili zimene zapita, akatumbu ambili aphedwa ndi anthu. Conco, n’kutheka kuti m’nthawi ya Baibo, nyama zimenezi zinali kupezeka kwambili m’Nyanja ya Mediterranean komanso m’Nyanja Yofiila. M’caka ca 1832, buku lina lacingelezi lotanthauzila mawu a m’Baibo, lolembedwa na Calmet, (Dictionary of the Holy Bible, peji 139) linati: “Kuzilumba zambili zing’ono-zing’ono za m’Nyanja Yofiila, zakufupi na dela la Sinai, kumapezeka akatumbu.”​—Onaninso buku lakuti The Tabernacle’s Typical Teaching, lolembedwa na A. J. Pollock, London, peji 47.

w15 7/15 21 ¶1

Yehova Amaona Nchito Yanu

Nchito yomanga cihema itatha, “mtambo unayamba kuphimba cihema cokumanako, ndipo ulemelelo wa Yehova unadzaza m’cihemaco.” (Eks. 40:34) Cimeneci cinali cizindikilo cakuti Yehova anasangalala ndi nchitoyo. Muganiza kuti Bezaleli na Oholiabu anamvela bwanji pa nthawiyo? Ngakhale kuti maina awo sanalembedwe pa zinthu zimene anapanga, ayenela kuti anakhutila podziŵa kuti Mulungu wadalitsa nchitoyo. (Miy. 10:22) Patapita zaka zambili, iwo ayenela kuti anali kusangalala kuona kuti zinthu zimene anapanga zikugwilabe nchito mu utumiki wa Yehova. Ndipo akadzaukitsidwa m’dziko latsopano, Bezaleli na Oholiabu adzasangalala kwambili kudziŵa kuti cihema cinagwilitsidwa nchito pa kulambila koona kwa zaka 500.

NOVEMBER 9-​15

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 1–3

“Colinga ca Nsembe”

it-2 525

Nsembe

Nsembe zopseleza. Nsembe zopseleza kapena kuti zonyeketsa zinali kupelekedwa zathunthu kwa Mulungu; wopeleka nsembeyo sanali kutengako mbali iliyonse ya nyamayo. (Yelekezelani na Ower. 11:​30, 31, 39, 40.) Nsembezi zinali kupelekedwa monga njila yocondelela Yehova kuti alandile kapena kuti aonetse kuti walandila nsembe ya macimo imene nthawi zina inali kupelekedwa pamodzi na nsembe zopselezazo. Pokhala “nsembe yopseleza,” Yesu Khristu anadzipeleka kothelatu, yense wathunthu.

it-2 528 ¶4

Nsembe

Nsembe zambewu. Nsembe zambewu zinali kupelekedwa pamodzi na sembe zaciyanjano, nsembe zopseleza, komanso nsembe zamacimo. Zinali kupelekedwanso monga zipatso zoyambilila. Nthawi zinanso, nsembe zambewu zinali kupelekedwa pazokha. (Eks. 29:​40-​42; Lev. 23:​10-​13, 15-​18; Num. 15:​8, 9, 22-​24; 28:​9, 10, 20, 26-​28; capu. 29) Aisiraeli anali kupeleka nsembe zambewu poyamikila Mulungu cifukwa cowadalitsa na kuwapatsa zinthu zambili. Nthawi zambili, ku nsembe zimenezi anali kuthilako mafuta na kuikako lubani. Nsembe zambewu zimene zinali kupelekedwa ni monga ufa wosalala, mbewu zokazinga, mkate wozungulila woboola pakati, kapena mikate yopyapyala yophikila mu uvuni, yophikila m’ciwaya, kapenanso yophikila mumphika wa mafuta ambili. Gawo lina la nsembe yambewu linali kuikidwa pa guwa lansembe zopseleza, gawo lina ansembe anali kudya, ndipo ngati nsembeyo yapelekedwa monga nsembe yaciyanjano, wopeleka nayenso anali kudyako. (Lev. 6:​14-​23; 7:​11-​13; Num. 18:​8-​11) Nsembe zonse zambewu zimene zinali kupelekedwa ku guwa lansembe zinali kukhala zopanda cofufumitsa kapena “uci” (mwacionekele kutanthauza madzi a nkhuyu kapena a zipatso zina), zinthu zimene zingafufume.​—Lev. 2:​1-​16.

it-2 526 ¶1

Nsembe

Nsembe zaciyanjano (kapena kuti nsembe zamtendele). Nsembe zaciyanjano zovomelezeka kwa Yehova zinali kuonetsa kuti munthu ali pamtendele na Mulungu. Wopeleka nsembeyo pamodzi na banja lake anali kudyako zinthu zopelekedwa nsembezo (m’bwalo la cihema; malinga na zimene ena amakamba, tumisasa tunamangidwa, m’mbali mwa nsalu yozungulila bwalo la cihema; ndipo m’kacisi, zipinda zodyela zinali kupelekedwa). Wansembe wopeleka nsembeyo anali kulandilako gawo la nsembeyo, nawonso ansembe amene anali kutumikila panthawiyo anali kulandila gawo lina. Yehova anali kulandila fungo lokoma la mafuta amene anali kuwanyeketsa pamoto. Magazi, amene amaimilako moyo, anali kupelekedwa kwa Mulungu cifukwa ni ake. Conco zinali monga kuti ansembe, anthu opeleka nsembewo, komanso Yehova anali kudyela pamodzi cakudya, kuonetsa ubale wabwino umene unali pakati pawo. Ngati munthu wadyako nsembeyo ali wodetsedwa, (kudetsedwa kulikonse kochulidwa m’Cilamulo), kapena ngati wadya nyama imene yakhalitsa kupitilila nthawi yovomelezeka, (m’dela lotentha limenelo, nyama yotelo inali itayamba kuwonongeka) anali kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake. Kucita zimenezo kunali kudetsa kapena kuipitsa cakudya, cifukwa iye ni wodetsedwa kapena cifukwa wadya cinthu conyansa pamaso pa Yehova Mulungu. Motelo anali kuonetsa kuti salemekeza zinthu zopatulika.​—Lev. 7:​16-​21; 19:​5-8.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w04 5/15 22 ¶2

Mfundo Zazikulu za M’buku la Levitiko

2:​13​—N’cifukwa ciani ‘nsembe iliyonse’ anali kuithila mcele? Sikuti anali kuthila mcele pofuna kukometsa nsembezo. Anthu padziko lonse lapansi amagwilitsa nchito mcele poteteza cinthu kuti cisavunde. Mosakayikila, anali kuika mcele ku zopeleka cifukwa cakuti umatanthauza kuti cinthuco n’cosawonongeka ndiponso cosawola.

it-1 813

Mafuta

Cimene Mulungu anapelekela lamulo loletsa kudya mafuta. M’pangano la Cilamulo, zonse ziŵili magazi na mafuta zinali kuonedwa kuti ni za Yehova yekha. M’magazi ni mmene muli moyo, umene Yehova yekha ndiye angaupeleke. Conco, magazi ni ake. (Lev. 17:​11, 14) Mafuta anali kuonedwa kuti ni mbali yabwino ngako ya nyama. Ngati munthu wapeleka mafuta a nyama monga nsembe anali kuonetsa kuti amazindikila kuti zabwino kwambili ni za Yehova, amene amapatsa mowoloŵa manja. Anali kuonetsanso kuti ali na mtima wofuna kupeleka kwa Mulungu zinthu zabwino koposa. Popeza kuti kupeleka mafuta kunali cizindikilo cakuti munthu wapeleka kwa Yehova zinthu zabwino kwambili, Malemba amakamba kuti mafutawo anali kupsa pamoto monga “cakudya,” komanso monga “fungo lokoma lokhazika mtima pansi” lopita kwa Mulungu. (Lev. 3:​11, 16) Conco, kudya mafuta kunali ngati kudzitengela cinthu cimene cinapatulidwa kuti n’ca Mulungu, kum’landa Yehova cinthu cimene cili cake. Ngati munthu wadya mafuta, cilango cake cinali kuphedwa. Komabe, mosiyana na magazi, nthawi zina mafuta anali kuwagwilitsila nchito zina ngati nyamayo yadzifela kapena ngati yaphedwa na cilombo.​—Lev. 7:​23-​25.

w04 5/15 22 ¶3

Mfundo Zazikulu za M’buku la Levitiko

3:​17. Popeza kuti mafuta anali kuonedwa kuti ndiyo mbali yabwino kwambili ya nyama, mwacionekele kuletsa kuti munthu asadye mafuta kunathandiza Aisiraeli kumvetsa kuti mbali yabwino kwambili ni ya Yehova. (Genesis 45:18) Izi zitikumbutsa kuti tiyenela kupatsa Yehova zinthu zabwino koposa.​—Miyambo 3:​9, 10; Akolose 3:​23, 24.

NOVEMBER 16-​22

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 4-5

“M’patseni Zabwino Koposa Yehova”

it-2 527 ¶9

Nsembe

Nsembe zopalamula. Nsembe zopalamula zinalinso nsembe zopelekedwa cifukwa ca machimo, cifukwa nthawi zonse kupalamula kumabwela cifukwa ca chimo. Nsembezi zinali kupelekedwa ngati munthu wacita chimo limene lamupangitsa kukhala na mlandu winawake. Ndipo zinali kusiyanako pang’ono na nsembe zina zamacimo cifukwa zioneka kuti colinga ca nsembezi kweni-kweni cinali kupeleka kapena kubwezeletsa ufulu winawake. Nsembezi zinali kupelekedwa ngati ufulu wa Yehova kapena wa mtundu wake woyela waphwanyidwa m’njila inayake. Nsembe zopalamula zinali kupelekedwa monga njila yopepesela kwa Yehova kaamba ka ufulu umene waphwanyidwa, kapena pofuna kuthandiza munthu wocimwa amene walapa kukhalanso na ufulu kapena kuti apeze mpumulo ku cilango ca chimo lake.​—Yelekezelani na Yes. 53:⁠10.

w09 6/1 26 ¶3

Amadziŵa Zimene Sitingakwanitse

Posonyeza kuti Yehova ni wacifundo kwambili, Cilamuloco cinafotokoza kuti: “Koma ngati sangakwanitse kupeleka nkhosa, azibweletsa kwa Yehova njiwa ziŵili kapena ana aŵili a nkhunda kuti zikhale nsembe za kupalamula cifukwa ca chimo limene wacita.” (Vesi 7) Mawu akuti “ngati sangakwanitse,” angalembedwenso kuti “dzanja lake likapanda kufikila.” Conco ngati munthu amene wacimwayo ni wosauka kwambili moti sangakwanitse kupeleka nkhosa, Mulungu anali kulandila nsembe imene munthuyo akanakwanitsa, imene ni njiwa ziŵili kapena nkhunda ziŵili.

w09 6/1 26 ¶4

Amadziŵa Zimene Sitingakwanitse

Koma kodi cinali kucitika n’ciani ngati munthuyo sakanakwanitsabe kupeleka mbalame ziŵilizo? Cilamulo cinafotokoza kuti: “Azibweletsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Azibweletsa ufa umenewu monga nsembe yake cifukwa ca chimo limene anacitalo, kuti ukhale nsembe yamacimo.” (Vesi 11) Yehova anali kulola kuti anthu osauka kwambili azipeleka nsembe yamacimo yopanda magazi. Motelo ku Isiraeli, umphawi sicinali cinthu colepheletsa munthu kupeza mwayi wokhululukidwa macimo ake kapena kukhala paubwenzi wabwino na Mulungu.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w16.02 24 ¶14

Tengelani Citsanzo ca Atumiki Okhulupilika a Yehova

14Inunso mungakhale wokhulupilika kwa Yehova ndi kwa ena mwa kukhala wokoma mtima. Mwacitsanzo, mungakhale na umboni wokwanila wakuti Mkhristu wina wacita chimo lalikulu. Pamenepa, mwina mungafune kukhala wokhulupilika kwa iye makamaka ngati ni mnzanu wapamtima kapena wacibale wanu. Koma mukudziŵanso kuti kukhala wokhulupilika kwa Yehova ndiye kofunika kwambili. Ngati zakhala conco, muyenela kumvela Yehova na kucita zinthu mokoma mtima kwa Mkhristuyo monga mmene Natani anacitila. Muuzeni kuti akapemphe thandizo kwa akulu mwamsanga. Ngati sanacite zimenezo, inuyo mukauze akulu za colakwaco. Mukacita zimenezo, mudzaonetsa kuti ndinu wokhulupilika kwa Yehova. Komanso, ndiye kuti mwamucitila zinthu mokoma mtima cifukwa akulu adzamuthandiza kukhalanso paubwenzi wabwino na Yehova. Iwo adzamuwongolela mwacikondi ndi mokoma mtima.​—Ŵelengani Levitiko 5:1; Agalatiya 6:⁠1.

it-1 1130 ¶2

Ciyelo

Nyama na Mbewu. Ana amphongo oyamba kubadwa a ng’ombe, nkhosa, na mbuzi anali opatulidwa kwa Yehova ndipo sanali kufunika kuwomboledwa. Nyama zimenezi zinali kufunika kupelekedwa nsembe, ndipo gawo lina la nyamayo linali kupelekedwa kwa ansembe opatulika. (Num. 18:​17-​19) Zipatso zoyambilila komanso cakhumi zinali zopatulika, cimodzi-modzinso nsembe zonse na mphatso zonse zopatulika zimene zinapeledwa kuti zigwilitsidwe nchito pa malo opatulika. (Eks. 28:38) Zinthu zonse zopatulika kwa Yehova sizinali kuonedwa mopepuka kapena kugwilitsidwa nchito monga zinthu wamba, kapenanso kudetsedwa mwanjila iliyonse. Mwacitsanzo, ganizilani lamulo la cakhumi. Ngati tate wapatulako gawo lina la zinthu zake, mwacitsanzo tiligu, kuti akapeleke kwa Mulungu monga cakhumi, ndiyeno iye olo wina wa m’banja lake mosadziŵa watengako tiliguyo kuti aseŵenzetse panyumba, monga kuphikila, tateyo anali kukhala na mlandu wophwanya lamulo la Mulungu lokhudza kulemekeza zinthu zopatulika. Malinga na Cilamulo, munthuyo anali kufunika kupeleka ku malo opatulika malipilo ofanana na zimene analonjezazo komanso 20 pesenti yowonjezela. Anafunikanso kupeleka mbuzi yaimuna yopanda cilema monga nsembe yopalamula. Conco, zinthu zopatulika za Yehova zinali kulemekezedwa kwambili.​—Lev. 5:​14-​16.

NOVEMBER 23-​29

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 6-7

“Njila Yoonetsela Kuyamikila”

w19.11 23 ¶9

Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la Levitiko

9Mfundo yaciŵili: Timatumikila Yehova cifukwa comuyamikila. Kuti timvetsetse mfundoyi, tiyeni tikambilane za nsembe zaciyanjano. Kupeleka nsembe zimenezi, inali mbali inanso yofunika kwambili pa kulambila koona mu Isiraeli wakale. Buku la Levitiko limakamba kuti Aisiraeli anali kupeleka nsembe zaciyanjano “posonyeza kuyamikila.” (Lev. 7:​11-​13, 16-​18) Aisiraeli anali kupeleka nsembe zimenezi, osati mocita kulamulidwa, koma mwa kufuna kwawo. Anali kucita izi cifukwa cokonda Mulungu wawo Yehova. Munthu wopeleka nsembeyo, banja lake, na wansembe, anali kudya nyama ya nsembeyo. Koma ziwalo zina za nyamayo zinali kupelekedwa kokha kwa Yehova. Kodi ziwalo zimenezo ni ziti?

w00 8/15 15 ¶15

Nsembe Zimene Zinakondweletsa Mulungu

15Copeleka cina caufulu cinali nsembe yaciyanjano, imene yafotokozedwa mu Levitiko caputa 3. Dzinali lingamasulidwenso kuti “nsembe ya zopeleka za mtendele.” M’Ciheberi, mawu akuti “mtendele” amatanthauza zoposa kungokhala kopanda nkhondo kapena zosokoneza zina. “M’Baibo, amatanthauza zimenezi, ndiponso mkhalidwe kapena unansi wa mtendele na Mulungu, kupeza bwino, cimwemwe, na cisangalalo,” limatelo buku lochedwa Studies in the Mosaic Institutions. Motelo, nsembe zaciyanjano zinali kupelekedwa, osati pofuna-funa mtendele na Mulungu, monga ngati kumutonthoza mtima, koma posonyeza kuyamikila kapena kukondwelela dalitso lokhala pamtendele na Mulungu umene awo amene iye anawavomeleza anali kusangalala nawo. Ansembe ndiponso wopeleka nsembeyo anali kudya nyama ya nsembeyo pambuyo popeleka magazi ndi mafuta kwa Yehova. (Levitiko 3:​17; 7:​16-​21; 19:​5-8) Mwa njila yokondweletsa ndi yophiphilitsa, wopeleka nsembeyo, ansembe ndiponso Yehova Mulungu anali kudyela pamodzi, kuonetsa unansi wamtendele umene unali pakati pawo.

w00 8/15 19 ¶8

Nsembe Zotamanda Zimene Zimakondweletsa Yehova

8Nanga bwanji za munthu amene akupeleka nsembeyo? Cilamulo cinali kunena kuti aliyense wobwela pamaso pa Yehova anayenela kukhala waudongo ndi wosadetsedwa. Munthu amene pacifukwa cina anali wodetsedwa, coyamba anafunika kupeleka nsembe yaucimo kapena yopalamula kuti abwezeletse mbili yake yabwino pamaso pa Yehova kotelo kuti nsembe yake yopseleza kapena yaciyanjano ikhale yololeka kwa Iye. (Levitiko 5:​1-6, 15, 17) Motelo, kodi ife timazindikila kufunika kwa kukhala ndi mbili yabwino nthaŵi zonse pamaso pa Yehova? Ngati tikufuna kuti kulambila kwathu kukhale kololeka kwa Mulungu, tiyenela kukonza mofulumila zolakwa zilizonse pa malamulo a Mulungu. Tiyenela kugwilitsa nchito mofulumila njila zimene Mulungu watipatsa zotithandizila, zimene ni “akulu a Mpingo” ndiponso “nsembe yophimba macimo athu,” Yesu Khristu.​—Yakobo 5:​14; 1 Yohane 2:​1, 2.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

it-1 833 ¶1

Moto

Wa pacihema komanso pakacisi. Moto woseŵenzetsa pa kulambila unapitilizabe kuyaka pa cihema komanso pambuyo pake, pa kacisi. Tsiku lililonse m’maŵa na madzulo kuli kacisisila, mkulu wa ansembe anali kufukiza zofukiza pa guwa la zofukiza. (Eks. 30:​7, 8) M’cilamulo, Mulungu analamula kuti moto wa paguwa lansembe zopseleza uziyaka nthawi zonse. (Lev. 6:​12, 13) Ayuda amakhulupilila kuti moto wa pa guwawo unayatsidwa na Mulungu mozizwitsa. Olo kuti maganizo amenewa ni ofala, sagwilizana na zimene Malemba amakamba. Malinga na malangizo amene Yehova anapatsa Mose poyamba, ana a Aroni anauzidwa kuti “aziika moto paguwa lansembelo ndi kuyalapo nkhuni” asanaike nsembe paguwapo. (Lev. 1:​7, 8) Pambuyo pakuti Mose walonga unsembe Aroni na ŵana ŵake, komanso wapeleka nsembe zolongela ansembe, m’pamene moto wocokela kwa Yehova unatsika na kunyeketsa nsembe zimene zinali paguwa lansembe. Mwina motowo unatsika kucokela mumtambo umene unaima pamwamba pa cihema. Conco, moto wozizwitsa umene unaonekela, sunatsike kukayatsa nkhuni zimene zinali paguwa lansembe ayi, koma “kukanyeketsa nsembe yopseleza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe.” Pambuyo pake, moto unapitiliza kuyaka paguwapo. Izi ziyenela kuti zinacitika cifukwa ca zonse ziŵili, moto wocokela kwa Mulungu komanso moto umene unalipo kale pa guwapo. (Lev. 8:⁠14–​9:​24) Zofanana na zimenezi zinacitikanso pa nthawi yopatulila kacisi wa Solomo. Panthawiyo, Solomo atangotsiliza kupemphela, moto wocokela kwa Yehova unatsika na kunyeketsa nsembe.​—2 Mbiri 7:1; onaninso Ower. 6:​21; 1 Maf. 18:​21-​39; 1 Mbiri 21:26 kuti mumvele zocitika zina pamene Yehova anaseŵenzetsa moto poonetsa kuti walandila nsembe za atumiki ake.

si 27 ¶15

Buku Namba 3 la m’Baibo​—Levitiko

15(3) Nsembe yamachimo inali kupelekedwa ngati munthu wacita macimo mosadziŵa, kapena mwangozi. Mtundu wa nyama yopelekedwa nsembe, unali kudalila pa munthu amene wacita chimo, kaya ni wansembe, mtundu wonse wa Isiraeli, mtsogoleli kapena munthu wamba. Mosiyana na nsembe zaufulu zopseleza ndi nsembe zaciyanjano zimene anthu anali kupeleka, munthu anali kupeleka nsembe yamacimo mwalamulo.​—4:​1-​35; 6:​24-​30.

NOVEMBER 30–DECEMBER 6

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LEVITIKO 8-9

“Umboni wa Dalitso la Yehova”

it-1 1207

Kulonga ansembe

Mose anasambika Aroni na ŵana ŵake Nadabu, Abihu, Eleazara, na Itamara (kapena anangowalamula kuti asambe) m’beseni lamkuwa la m’bwalo lacihema. Kenako anaveka Aroni zovala zaulemelelo za mkulu wa ansembe. (Num. 3:​2, 3) Apa Aroni anavala zovala zokongola, zogwilizana na udindo komanso utumiki wake. Pambuyo pake, Mose anadzoza cihema, zipangizo na ziwiya zake zonse, guwa la nsembe zopseleza na beseni komanso ziwiya zake. Mwakutelo, iye anayeletsa zinthu zimenezi, kuzipatula kuti ziyambe kugwilitsidwa nchito kokha potumikila Mulungu. Pamapeto pake, Mose anadzoza Aroni mwa kuthila mafuta pamutu pake.​—Lev. 8:​6-​12; Eks. 30:​22-​33; Sal. 133:⁠2.

it-1 1208 ¶8

Kulonga ansembe

Pa tsiku la 8, ansembe ataikidwa pa udindo wawo na kukonzekeletsedwa bwino, anagwila nchito okha kwa nthawi yoyamba (popanda thandizo la Mose). Iwo anapelekela mtundu wa Aisiraeli nsembe yophimba macimo. Aisiraeli anali kufunikila kwambili kuyeletsedwa cifukwa ca ucimo wawo wobadwa nawo, komanso cifukwa ca kusamvela kwawo mwa kupanga fano la mwana wang’ombe, zimene zinakhumudwitsa Yehova. (Lev. 9:​1-7; Eks. 32:​1-​10) Ansembe atsopanowo atangotsiliza kupeleka nsembe kwa nthawi yoyamba imeneyi, Yehova anaonetsa kuti wavomeleza kuikidwa kwawo monga ansembe mwa kutumiza moto, mwacionekela kucokela mumtambo umene unali pamwamba pa cihema. Motowo unanyeketsa nsembe zimene zinatsala paguwa lansembe.​—Lev. 9:​23, 24.

w19.11 23 ¶13

Mfundo Zimene Tingaphunzile mu Buku la

Levitiko

13Mfundo yacinayi: Yehova akudalitsa gawo la pa dziko lapansi la gulu lake. Ganizilani zimene zinacitika mu 1512 B.C.E. pamene Aisiraeli anamanga cihema m’mbali mwa Phili la Sinai. (Eks. 40:17) Mose anatsogolela pa mwambo woika Aroni ndi ana ake kukhala ansembe. Mtundu wa Isiraeli unasonkhana kuti uonelele pamene ansembewo anali kupeleka nsembe zoyamba za nyama. (Lev. 9:​1-5) Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anavomeleza Aroni ndi ana ake amene anali atangoikidwa kumene kukhala ansembe? Pamene Mose na Aroni anali kudalitsa Aisiraeli, Yehova anagwetsa moto umene unanyeketsa nsembe yotsala imene inali pa guwa la nsembe.​—Ŵelengani Levitiko 9:​23, 24.

Kufufuza Cuma ca Kuuzimu

w14 11/15 9 ¶6

Cifukwa Cake Tifunika Kukhala Oyela

6Lamulo lakuti akulu ansembe aciisiraeli azikhala oyela mwakuthupi, lili ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu a Yehova masiku ano. Anthu amene timaphunzila nawo Baibo amaona kuti malo athu olambilila ndi aukhondo, ndipo timavala bwino. Conco, ciyelo ca akulu ansembe cimatithandiza kudziŵa kuti, aliyense amene akufuna kulambila Yehova ayenela kukhala “woyela mumtima mwake.” (Ŵelengani Salimo 24:​3, 4; Yes. 2:​2, 3.) Pocita utumiki wopatulika kwa Mulungu, tiyenela kukhala oyela m’maganizo, m’mitima, ndi matupi athu. Kucita zimenezi kumafuna kudzipenda nthawi zonse. Ena angafunike kupanga masinthidwe aakulu paumoyo wawo kuti akhale oyela. (2 Akor. 13:⁠5) Mwacitsanzo, wofalitsa wobatizika amene mwadala wakhala akupenyelela zamalisece ayenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikuyesetsa kukhala woyela?’ Iye ayenela kuyesetsa kupeza thandizo kuti aleke cizoloŵezi coipa cimeneci.​—Yak. 5:​14.

it-2 437 ¶3

Mose

Mulungu anaika Mose kukhala mkhalapakati wa pangano lake la Cilamulo na Aisiraeli. Umenewu unali udindo wapadela kwambili umene munthu aliyense sanapatsidweko kupatulapo Yesu Khristu yekha, amene ni Mkhalapakati wa pangano latsopano. Mose anatenga magazi a nsembe zanyama na kuwaza buku la cipangano, cimene cinali pakati pa Yehova na Aisiraeli (mosakayikila moimilidwa na akulu a mtunduwo). Iye anaŵelengela anthuwo buku la panganolo, ndipo anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tidzacita zomwezo ndipo tidzamumvela.” (Eks. 24:​3-8; Aheb. 9:​19) Pa nchito yake monga mkhalapakati, Mose anali na mwayi woyang’anila nchito yomanga cihema na kupanga ziwiya zake, ndipo iye ndiye anapatsidwa mapulani a kapangidwe ka zinthu zimenezo. Analinso na mwayi wolonga ansembe, kudzoza cihema, komanso Aroni mkulu wa ansembe na mafuta opangidwa mwapadela. Pambuyo pake, anayang’anila ansembe olongedwa kumenewo pamene anali kucita utumiki wawo kwa nthawi yoyamba.​—Eks. macapu. 25-​29; Lev. macapu. 8, 9.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani