PHUNZILO 12
Kodi Mungamuyandikile Bwanji Mulungu?
1. Kodi Mulungu amamva mapemphelo onse?
Mulungu amafuna kuti anthu a mitundu yonse ayandikile kwa iye mwa kumapemphela. (Salimo 65:2) Komabe, iye samamva kapena kuti kulandila mapemphelo onse. Mwacitsanzo, Mulungu angatsekeleze mapemphelo a mwamuna amene amacitila nkhanza mkazi wake. (1 Petulo 3:7) Ndiponso, pamene Aisiraeli anapitiliza kucita zoipa, Mulungu sanamvele mapemphelo ao. N’zoonekelatu kuti, pemphelo ndi mwai wapadela kwambili. Komabe, Mulungu amalandila mapemphelo ngakhale a anthu ocimwa ngati io alapadi.—Ŵelengani Yesaya 1:15; 55:7.
Tambani vidiyo Kodi Mulungu Amamvela Mapemphelo Onse?
2. Kodi tiyenela kupemphela bwanji?
Pemphelo ni mbali ya kulambila kwathu. Conco, tiyenela kupemphela cabe kwa Mlengi wathu, Yehova. (Mateyu 4:10; 6:9) Popeza ndife opanda ungwilo, tiyenelanso kupemphela m’dzina la Yesu cifukwa anafela macimo athu. (Yohane 14:6) Yehova samafuna kuti tizipeleka mapemphelo oloŵeza pamtima kapena olemba m’buku. Amafuna kuti tizipemphela kucokela pansi pa mtima.—Ŵelengani Mateyu 6:7; Afilipi 4:6, 7.
Mlengi wathu amamva ngakhale mapemphelo a mumtima. (1 Samueli 1:12, 13) Iye amatiuza kuti tizipemphela nthawi iliyonse, monga kum’maŵa tikauka, popita kukagona, panthawi ya cakudya, ndi pamene takumana ndi mavuto.—Ŵelengani Salimo 55:22; Mateyu 15:36.
3. N’cifukwa ciani Akristu amasonkhana pamodzi?
Kuyandikila kwa Mulungu si cinthu copepuka cifukwa tikhala pakati pa anthu amene samakhulupilila Mulungu, ndipo amasuliza lonjezo lake lakuti adzabweletsa mtendele pa dziko lapansi. (2 Timoteyo 3:1, 4; 2 Petulo 3:3, 13) Mwa ici, timafunikila cilimbikitso ca olambila anzathu, ndipo naonso amafuna kuti tiziwalimbikitsa.—Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.
Kugwilizana ndi anthu amene amakonda Mulungu kumatithandiza kuti timuyandikile. Misonkhanoya Mboni za Yehova imapeleka mipata yabwino yakuti tilimbikitsidwe ndi cikhulupililo ca ena.—Ŵelengani Aroma 1:11, 12.
4. Kodi mungamuyandikile bwanji Mulungu?
Mungamuyandikile Yehova mwa kusinkha-sinkha zimene mwaphunzila m’Mau ake. Ganizilani zimene mwaphunzila pa zocita zake, malangizo ake, ndi malonjezo ake. Pemphelo ndi kusinkha-sinkha kumatithandiza kuyamikila cikondi ca Mulungu ndi nzelu zake.—Ŵelengani Yoswa 1:8; Salimo 1:1-3.
Mungayandikile Mulungu ngati mumam’dalila ndi kum’khulupilila. Koma cikhulupililo cili monga cinthu camoyo cimene cimafunika zakudya. Muyenela nthawi zonse kudyetsa cikhulupililo canu mwa kusinkha-sinkha zifukwa zimene zimakucititsani kukhala ndi cikhulupililo cimeneco.—Ŵelengani Mateyu 4:4; Aheberi 11:1, 6.
5. Kodi kuyandikila Mulungu kungakuthandizeni bwanji?
Yehova amasamala anthu amene amam’konda. Angawachinjilize ku zilizonse zimene zingaononge cikhulupililo ndi ciyembekezo cao ca moyo wosatha. (Salimo 91:1, 2, 7-10) Iye amaticenjeza za njila zoipa zimene zingaononge thanzi lathu ndi kutilanda cimwemwe. Yehova amatiphunzitsa njila yabwino yotsatila pa umoyo wathu.—Ŵelengani Salimo 73:27, 28; Yakobo 4:4, 8.