LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr21 September
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2021
  • Tumitu
  • SEPTEMBER 6-12
  • SEPTEMBER 13-19
  • SEPTEMBER 20-26
  • SEPTEMBER 27–OCTOBER 3
  • OCTOBER 4-10
  • OCTOBER 11-17
  • OCTOBER 18-24
  • OCTOBER 25-31
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2021
mwbr21 September

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

SEPTEMBER 6-12

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | DEUTERONOMO 33-34

“Funani Citetezo m’Manja a Yehova ‘Amene Adzakhalapo Mpaka Kale-kale’”

it-2 51

Yesuruni

Dzina laulemu la Isiraeli. M’Baibo ya Cigiriki ya Septuagint, liwu lakuti “Yesuruni” linagwilitsidwa nchito monga dzina loonetsa cikondi. Linamasulidwa kuti “wokondedwa.” Dzina lakuti “Yesuruni” linayenela kukumbutsa Aisiraeli kuti anacita pangano na Yehova, ndipo anali na udindo wokhalabe okhulupilika kwa iye. (Deut. 33:5, 26; Yes. 44:2) Pa Deuteronomo 32:15, dzina lakuti Yesuruni linagwilitsidwa nchito poonetsa kuti mtundu wa Aisiraeli sunacite zinthu mogwilizana na dzinali. Mtunduwo unakhala wosalamulilika, unaiŵala Mulungu amene anaupanga, ndipo unanyoza Mpulumutsi wawo.

rr 120, bokosi

Amatithandiza Kuimililanso

Kumbukilani kuti zaka mahandiledi ambili isanafike nthawi ya Ezekieli, mneneli Mose anakamba kuti Yehova ali na mphamvu, komanso kuti amalakalaka kuseŵenzetsa mphamvu zakezo pothandiza anthu ake. Mose analemba kuti: “Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo, ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27) Conco tingakhale otsimikiza kuti ngati tithaŵila kwa Yehova pa nthawi ya mavuto, iye adzatiika m’manja ake acikondi, adzatinyamula mwacikondi, ndipo adzatithandiza kuimililanso.—Ezek. 37:10.

w11 9/15 19 ¶16

Tiyeni Tithamange Mpikisano Mopilila

16Mofanana na Abulahamu, nayenso Mose sanaone malonjezo a Mulungu akukwanilitsidwa. Aisiraeli ali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mulungu anauza Mose kuti: “Pakuti udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa m’dziko limene ndikupeleka kwa ana a Isiraeli.” Izi zinacitika cifukwa cakuti iye na Aroni atapsetsedwa mtima ndi anthu osamvela, anacita zinthu “mosakhulupilika kwa [Mulungu] pakati pa ana a Isiraeli, kumadzi a pa Meriba.” (Deut. 32:51, 52) Kodi Mose anakwiya na zimenezi? Ayi sanakwiye. Tikutelo cifukwa anapempha Yehova kuti adalitse Aisiraeli ndipo mawu ake omaliza anali akuti: “Ndiwe wodala Isiraeli iwe! Ndani angafanane ndi iwe, anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova, cishango cako cokuthandiza, amenenso ndi lupanga lako lopambana?”—Deut. 33:29.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 439 ¶3

Mose

Mose anamwalila ali na zaka 120. Poonetsa kuti Mose anali na mphamvu zacibadwa, Baibo imati: “Diso lake silinacite mdima, ndipo anali adakali ndi mphamvu.” Iye anaikidwa m’manda na Yehova pa malo amene sadziŵika mpaka pano. (Deut. 34:5-7) Mulungu ayenela kuti anacita izi pofuna kuteteza Aisiraeli kuti asagwele mumsampha wolambila mafano mwa kupanga manda a Mose kukhala malo olambilila. N’zoonekelatu kuti Mdyelekezi anali kufuna kuseŵenzetsa mtembo wa Mose pa colinga ngati cimeneci, cifukwa Yuda, wophunzila wa Yesu Khristu, amenenso anali m’bale wake, analemba kuti: “Pamene Mikayeli mkulu wa angelo anasemphana maganizo ndi Mdyelekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose, sanayese n’komwe kumuweluza ndi mawu onyoza. M’malomwake, anati: ‘Yehova akudzudzule.’” (Yuda 9) Aisiraeli asanaloŵe m’dziko la Kanani motsogoleledwa na Yoswa, analila Mose kwa masiku 30.—Deut. 34:8.

SEPTEMBER 13-19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 1-2

“Mmene Mungakhalile na Moyo Wopambana”

w13 1/15 8 ¶7

Ukhale Wolimba Mtima Cifukwa Yehova Ali Nawe

7Kuti tikhale olimba mtima n’kumacita zofuna za Mulungu, tiyenela kuphunzila ndiponso kutsatila Mawu ake. Izi n’zimene Yoswa anauzidwa kucita ataloŵa m’malo mwa Mose. Anauzidwa kuti: “Iwe khala wolimba mtima kwambili ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Uonetsetse kuti ukutsatila malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakulamula. . . . Buku la malamulo ili lisacoke pakamwa pako, uziliwelenga ndi kusinkhasinkha usana ndi usiku, kuti uonetsetse kuti ukutsatila zonse zolembedwamo. Pakuti ukatelo, udzakhala ndi moyo wopambana, ndipo udzacita zinthu mwanzelu.” (Yos. 1:7, 8) Yoswa anatsatila malangizo amenewa ndipo anakhala na “moyo wopambana.” Nafenso tikatelo, tidzakhala olimba mtima ndipo zinthu zidzatiyendela bwino potumikila Mulungu.

w13 1/15 11 ¶20

Ukhale Wolimba Mtima Cifukwa Yehova Ali Nawe

20Kupitiliza kucita zimene Mulungu akufuna pokumana na mavuto m’dziko loipali si kopepuka. Komabe, sitili tokha cifukwa Mulungu ali nafe. Nayenso Mwana wake, amene ni Mutu wa mpingo, ali nafe. Palinso Mboni za Yehova zinzathu padziko lonse lapansi zoposa 7,000,000. Pamodzi na anzathu amenewa, tiyeni tipitilize kukhala na cikhulupililo ndiponso kulengeza uthenga wabwino. Tizikumbukilanso lemba la caka ca 2013 lakuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. . . . Yehova Mulungu wako ali nawe.”—Yos. 1:9.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w04 12/1 9 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa

2:4, 5—N’cifukwa ciani Rahabi akusoceletsa anthu a mfumu amene akusakasaka azondi aja? Rahabi akuika moyo wake paciswe poteteza azondiwo cifukwa cakuti iye wayamba kukhulupilila Yehova. Motelo palibe cifukwa coti Rahabi aululile kumene kuli azondiwo kwa anthu ofuna kupha anthu a Mulunguwa. (Mateyu 7:6; 21:23-27; Yohane 7:3-10) Ndipotu Rahabi ‘anayesedwa wolungama cifukwa ca nchito’ zake, kuphatikizapo nchito yosoceletsa nthumwi za mfumuzi.—Yakobo 2:24-26.

SEPTEMBER 20-26

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 3-5

“Yehova Amatidalitsa Ngati Ticita Zinthu Zoonetsa Cikhulupililo”

it-2 105

Yorodano

Nthawi zambili, cigawo ca mtsinje wa Yorodano cimene cili kuphompho kwa Nyanja ya Galileya, cimakhala cozama mita imodzi mpaka mamita atatu pa avaleji. Ndipo m’mimba mwake, cigawo ca mtsinje cimeneci cimakwana mamita pafupifupi 27 mpaka 30. Koma m’nyengo yokolola, mtsinje wa Yorodano umasefukila, ndipo umakula na kuzama kuposa pamenepa. (Yos. 3:15) Pa nthawi ngati imeneyo, zikanakhala zangozi kuti mtundu wa Aisiraeli wokhala na amuna, akazi, ndi ana uwoloke mtsinje wa Yorodano, maka-maka kuwolokela pafupi na Yeriko. Pa malo amenewo, madzi amathamanga kwambili cakuti m’zaka zaposacedwapa onyaya ena anakokoloka na madzi. Komabe, Yehova mozizwitsa anaimitsa madzi a mu mtsinje wa Yorodano, na kupangitsa kuti Aisiraeli akwanitse kuwoloka mtsinjewo pa nthaka youma. (Yos. 3:14-17) Pambuyo pa zaka mahandiledi, cozizwitsa cofananaco cinacitikila Eliya kamodzi ali na Elisa, ndipo cinacitikilanso Elisa kamodzi ali yekha.—2 Maf. 2:7, 8, 13, 14.

w13 9/1 16 ¶17

Kondwelani Ndi Zikumbutso za Yehova

17Kodi timalimbitsa bwanji cidalilo cathu pa Yehova pamene ticita zinthu mokhulupilika? Ganizilani nkhani ya m’Malemba yonena za mmene Aisiraeli analoŵela m’Dziko Lolonjezedwa. Yehova analamula ansembe kuti anyamule likasa la cipangano na kupita ku Mtsinje wa Yorodano. Koma anthuwo atayandikila mtsinjewo, anapeza kuti ni wosefukila. Kodi Aisiraeli anacita ciani? Kodi iwo anamanga msasa m’mphepete mwa mtsinjewo na kuyembekezela kwa milungu kapena kuposelapo kuti madziwo acepe? Ayi, iwo anakhulupilila Yehova na kutsatila malangizo ake. Kodi zotsatila zake zinali zotani? Baibo imanena kuti pamene mapazi a ansembe ‘anaponda madzi a m’mphepete mwa mtsinjewo, . . . madzi otsika kucokela kumtunda anayamba kuima.’ Imanenanso kuti iwo “anangoima cilili panthaka youma pakati pa mtsinje wa Yorodano. Anaimabe conco pamene Aisiraeli onse anali kuwoloka panthaka youmayo.” (Yos. 3:12-17) Aisiraeli ayenela kuti analimbikitsidwa pamene anaona kuti madzi othamanga amenewo aima. Kunena zoona, cikhulupililo cawo pa Yehova cinalimba cifukwa cakuti anadalila malangizo ake.

w13 9/1 16 ¶18

Kondwelani Ndi Zikumbutso za Yehova

1N’zoona kuti Yehova sacitila anthu ake zinthu zozizwitsa masiku ano, koma iye amawadalitsa ngati acita zinthu mokhulupilika. Mzimu woyela wa Mulungu umawapatsa mphamvu kuti akwanitse kugwila nchito yawo yolalikila uthenga wa Ufumu padziko lonse. Ndiponso Mboni yaikulu ya Yehova, Yesu Kristu, ataukitsidwa anatsimikizila otsatila ake kuti adzawathandiza pa nchito yofunika imeneyi. Iye anati: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga . . . ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Abale na alongo amene anali na manyazi kapena mantha aona kuti mzimu woyela wa Mulungu wawathandiza kulankhula molimba mtima kwa anthu acilendo mu utumiki.—Ŵelengani Salimo 119:46; 2 Akorinto 4:7.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w04 12/1 9 ¶2

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa

5:14, 15—Kodi ndani amene ali “kazembe wa ankhondo a Yehova”? Kazembe amene akumulimbikitsa Yoswa paciyambi polanda Dziko Lolonjezedwa n’zacionekele kuti ni “Mawu,” kapena kuti Yesu Khristu asanabadwe monga munthu. (Yohane 1:1; Danieli 10:13) N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti ngakhale panopo Yesu Khristu, amene tsopano anapatsidwa ulemelelo, amakhala nawo anthu a Mulungu pankhondo yawo yauzimu.

SEPTEMBER 27–OCTOBER 3

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 6-7

“Pewani Zinthu Zopanda Pake”

w10 4/15 20 ¶5

Musamaone Zinthu Zacabe

5Patapita zaka mazana ambili, Mwisiraeli wina dzina lake Akani, ‘anaona’ zinthu zina mumzinda wa Yeriko, womwe unali utawonongedwa, ndipo anaziba. Mulungu anali atalamula kuti zinthu zonse mumzindawo ziwonongedwe kupatulapo zinthu zina zimene zinayenela kupelekedwa mosungila cuma ca Yehova. Aisiraeli anacenjezedwa kuti ‘asakhudze copelekedwaco’ kuopela kuti angakhumbile n’kutengako zinthu zina. Cifukwa ca kusamvela kwa Akani, Aisiraeli anagonjetsedwa na anthu a mumzinda wa Ai ndipo ambili anaphedwa. Akani sanaulule chimo lake mpaka pamene anaonekela poyela. Akani anati: “Pamene ndinaona” zinthuzo “ndinazikhumbila ndi kuzitenga.” Cilakolako ca maso ake cinacititsa kuti iye awonongedwe limodzi “ndi zake zonse.” (Yos. 6:18, 19; 7:1-26) Akani analakalaka zinthu zimene analetsedwa.

w97 8/15 28 ¶2

N’kuululilanji Coipa?

Cifukwa cimodzi coululila chimo n’cakuti kumathandiza kusunga ciyelo ca mpingo. Yehova ni Mulungu woyela, wopatulika. Amafuna onse omulambila akhale oyela mwauzimu na mwamakhalidwe. Mawu ake ouzilidwa amati: “Monga ana omvela, lekani kukhala motsatila zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziwa. Koma khalani motsanzila Woyela amene anakuitanani. Inunso khalani oyela m’makhalidwe anu onse, cifukwa Malemba amati: ‘Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.’” (1 Petulo 1:14-16) Awo amene amacita zinthu zonyansa kapena zolakwa angabweletse cidetso na kutayitsa ciyanjo ca Yehova pampingo wonse mpaka atawongoleledwa kapena kucotsedwa.—Yelekezelani na Yoswa, caputala 7.

w10 4/15 21 ¶8

Musamaone Zinthu Zacabe

8khristu oona nawonso amakhala na cilakolako ca maso na ca thupi. N’cifukwa cake Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala odziletsa pa nkhani ya zinthu zimene timaona na zimene timakhumbila. (1 Akor. 9:25, 27; ŵelengani 1 Yohane 2:15-17.) Munthu wolungama Yobu anazindikila kuti pali kugwilizana pakati pa kuona na kukhumbila. Iye anati: “Ndacita pangano ndi maso anga. Conco ndingayang’anitsitse bwanji namwali?” (Yobu 31:1) Yobu anakana kukhudza mkazi m’njila yaciwelewele komanso sanalole kumaganiza zinthu zotelozo m’pang’ono pomwe. Yesu anatsindika mfundo yakuti sitiyenela kuganizila zaciwelewele. Iye anati: “Aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kumulakalaka, wacita naye kale cigololo mumtima mwake.”—Mat. 5:28.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w15 11/15 15 ¶2-3

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

M’nthawi zakale, asilikali anali kuzungulila mpanda wa mzinda kuti aulande. Ngati asilikali azungulila mzindawo kwa nthawi yaitali, anthu mumzindawo anali kukakamizika kudya zakudya zimene anasunga. Ndiyeno asilikali akalanda mzinda, anali kutenga ciliconse cimene afuna, kuphatikizapo cakudya ciliconse cimene catsala. Ndiye cifukwa cake akatswili ofufuza zinthu zakale anapeza cakudya cocepa m’mabwinja a mizinda ya ku Palesitina imene inagongetsedwa mwa njila imeneyi, ndipo m’mizinda ina sanapezemo cakudya ciliconse. Koma zimene anapeza m’mabwinja a Yeriko n’zosiyana na zimenezi. Buku lina lofotokoza zinthu zakale limati: “M’mabwinja a Yeriko anapezamo zinthu zambili zoumba. Koma kuwonjezela pamenepo, anapezamonso zakudya zambili.” Bukuli limanenanso kuti: “N’zodabwitsa kuti m’mabwinja a Yeriko anapezamo zakudya zambili.”—Biblical Archaeology Review.

Baibo imakamba kuti Aisiraeli sanatenge cakudya ciliconse mumzinda wa Yeriko cifukwa Yehova anawalamula kuti sayenela kutelo. (Yoswa 6:17, 18) Imakambanso kuti Aisiraeli anawononga mzinda wa Yeriko m’nyengo yokolola, nthawi imene mumzindawo munali zakudya zambili. (Yoswa 3:15-17; 5:10) Monga mmene tanenela, mumzinda wa Yeriko munapezeka zakudya zambili. Izi zionetsa kuti mzindawo unawonongedwadi m’kanthawi kocepa monga mmene Baibo imanenela.

OCTOBER 4-10

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 8-9

“Zimene Tingaphunzile pa Nkhani ya Agibeoni”

it-1 930-931

Agibeoni

Mmene Anacitila Zinthu na Yoswa. M’nthawi ya Yoswa, ku Gibeoni kunali kukhala Ahivi, umodzi mwa mitundu 7 ya Akanani imene inali kufunika kuwonongedwa. (Deut. 7:1, 2; Yos. 9:3-7) Agibeoni anali kuchedwanso Aamori cifukwa zioneka kuti nthawi zina dzinali anali kuliseŵenzetsa pokamba za Akanani onse. (2 Sam. 21:2; yelekezelani na Gen. 10:15-18; 15:16.) Mosiyana na Akanani ena, Agibeoni anazindikila kuti ngakhale kuti anali na gulu lankhondo lamphamvu komanso kuti anali na mzinda waukulu, sakanakwanitsa kulimbana na Aisiraeli cifukwa Yehova anali kuwamenyela nkhondo. Conco, pambuyo pa kuwonongedwa kwa mzinda wa Yeriko na Ai, amuna a ku Gibeoni amenenso aoneka kuti anaimila mizinda ina itatu ya Ahivi, yomwe inali Kefira, Beeroti, na Kiriati-yearimu (Yos. 9:17), anatumiza nthumwi kwa Yoswa ali ku Giligala kuti akagwilizane naye za mtendele. Agibeoni amene anatumizidwawo anavala zovala zansanza na nsapato zakutha. Ananyamula vinyo m’matumba acikopa akutha na cakudya m’matumba akutha, ndipo mkate wawo unali wouma na wofumbutuka. Iwo anafika kwa Yoswa monga anthu ocokela ku dziko lakutali, limene Aisiraeli sanafunike kuliwononga. Agibeoni anavomeleza kuti Yehova ndiye anagonjetsa Aiguputo na mafumu aŵili a Aamori, Sihoni na Ogi. Koma iwo mwanzelu sanafotokoze za kugonjetsedwa kwa mizinda ya Yeriko na Ai, cifukwa mbili ya kuwonongedwa kwa mizinda imeneyi ikanakhala kuti inali isanawafike pamene anali kunyamuka ku dziko lawo limene anati ni “lakutali kwambili.” Conco, atsogoleli a Isiraeli anapenda umboniwo na kukhutila nawo, ndipo anacita nawo pangano kuti asawaphe.—Yos. 9:3-15.

w11 11/15 8 ¶14

“Usadalile Luso Lako Lomvetsa Zinthu”

14Cifukwa cakuti tonse ndife anthu opanda ungwilo, aliyense kuphatikizapo akulu, ayenela kusamala kuti asasiye kuyendela malangizo a Yehova posankha zocita. Taganizilani zimene Yoswa yemwe analoŵa m’malo mwa Mose limodzi na amuna aakulu a Isiraeli anacita pa nthawi imene anthu a ku Gibeoni ananamizila kuti akucokela kutali kwambili. Iwo asanafunsile kwa Yehova, anagwilizana nawo za mtendele ndipo anacita nawo pangano kuti asawaphe. Ngakhale kuti Yehova anadzagwilizana na zimene anacita, iye anaonetsetsa kuti colakwa cawo cimeneci cilembedwe m’Malemba kuti tiphunzilepo kanthu.—Yos. 9:3-6, 14, 15.

w04 10/15 18 ¶14

‘Yenda-yenda M’dzikoli’

14Nthumwizo zinati: “Akapolo anufe tacokela kudziko lakutali kwambili. Tabwela cifukwa tamva za dzina la Mulungu wanu, Yehova.” (Yoswa 9:3-9) Malinga na mmene zovala ndiponso zakudya zawo zinalili, anali kuonekadi ngati acokela kutali kwambili, koma mudzi wa Gibeoni unali pamtunda wa makilomita pafupifupi 30 okha kucokela ku Giligala. Atakhulupilila zimenezi, Yoswa na akalonga ake anapanga pangano la mtendele na Gibeoni ndiponso midzi yawo imene inali kufupi na mudzi wa Gibeoni. Kodi cinyengo ca Agibeonici cinali congofuna kupewa kuwonongedwa? Ayi. Cinaonetsa mtima womwe anali nawo wofuna kuyanjidwa na Mulungu wa Isiraeli. Yehova anavomeleza kuti Agibeoni akhale “otola nkhuni ndi otungila madzi Aisiraeli, ndiponso kuti azitola nkhuni ndi kutunga madzi a paguwa lansembe la Yehova” komanso kuti azibweletsa nkhuni zogwilitsa nchito zofunika popeleka nsembe paguwa. (Yoswa 9:11-27) Agibeoni anapitiliza kukhala odzipeleka kutumikila Yehova pogwila nchito zonyozeka. Mwacionekele, ena mwa iwo anali pagulu la Anetini amene anabwelela kucokela ku Babulo na kukatumikila pa kacisi amene anamangidwanso. (Ezara 2:1, 2, 43-54; 8:20) Tingatengele mtima wawo mwa kuyesetsa kupitiliza kukhala pamtendele na Mulungu na kukhala ofunitsitsa kum’tumikila ngakhale panchito zonyozeka.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 1030

Kupacika Pamtengo

M’cilamulo cimene Yehova anapatsa Aisiraeli, anthu ena ophwanya malamulo akaphedwa anali kupacikidwa pamtengo kuti cikhale monga cizindikilo cakuti ni “otembeleledwa ndi Mulungu,” ndipo anali kuikidwa pa malo oonekela kuti akhale monga citsanzo cocenjeza kwa anthu ena. Koma mtembo wa opacikidwayo unayenela kutsitsidwa kusanade na kuuika m’manda. Kusiya mtembowo pamtengo usiku wonse kukanaipitsa nthaka imene Mulungu anapatsa Aisiraeli. (Deut. 21:22, 23) Aisiraeli anali kutsatilabe lamulo limeneli ngakhale kuti amene waphedwa sanali Mwisiraeli.—Yos. 8:29; 10:26, 27.

OCTOBER 11-17

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 10-11

“Yehova Anawamenyela Nkhondo Aisiraeli”

it-1 50

Adoni-zedeki

Mfumu ya Yerusalemu pa nthawi imene Aisiraeli analanda Dziko Lolonjezedwa. Adoni-zedeki anagwilizana na mafumu ena ang’ono-ang’ono a kum’madzulo kwa Yorodano kuti alimbane na gulu la nkhondo la Yoswa. (Yos. 9:1-3) Komabe, Ahivi a ku Gibeoni anacita pangano lamtendele na Yoswa. Cifukwa cokhumudwa na zimenezi komanso pofuna kuti mafumu enanso asagwilizane na adani awo, Adoni-zedeki anagwilizanitsa gulu lake lankhondo na magulu ankhondo a mafumu ena anayi a Aamori, ndipo anakamanga msasa pafupi na mzinda wa Gibeoni na kuuthila nkhondo. Koma Yoswa anapulumutsa Agibeoni na kugonjetsa kothelatu magulu a asilikali a mafumu amene anagwilizanawo. Ataona zimenezo, mafumu asanuwo anathaŵila ku Makeda, kumene anakabisala kuphanga. Koma asilikali a Yoswa anawatsekela kuphangalo na miyala ikulu-ikulu. Yoswa iyemwini ndiye anapha Adoni-zedeki na mafumu enawo anayi pamaso pa asilikali ake. Kenako anawapacika pa mitengo. Pamapeto pake, mitembo ya mafumuwo anaiponyanso m’phanga limene anabisalamo, ndipo phangalo ndilo linakhala manda awo.—Yos. 10:1-27.

it-1 1020

Matalala

Amene Yehova Anagwilitsila Nchito. Nthawi zina Yehova anali kuseŵenzetsa matalala pofuna kukwanilitsa mawu ake ndiponso pofuna kuonetsa mphamvu zake zazikulu. (Sal. 148:1, 8; Yes. 30:30) Nthawi yoyamba pamene Baibo imakamba kuti Mulungu anaseŵenzetsa matalala ni pa mlili wa namba 7 umene unagwela Iguputo wakale. Pa mliliwo, matalala oopsa anawononga zomela, anagwetsa mitengo, ndipo anapha anthu na nyama zimene zinali panja. Koma sanafike ku dela la Goseni kumene kunali Aisiraeli. (Eks. 9:18-26; Sal. 78:47, 48; 105:32, 33) Patapita zaka, Aisiraeli ali m’Dziko Lolonjezedwa, motsogoleledwa na Yoswa anathandiza Agibeoni amene anaukilidwa na mafumu asanu a Aamori amene anagwilizana. Pa nthawiyo, Yehova anaseŵenzetsa matalala akulu-akulu pogonjetsa Aamoriwo. Amene anafa pa nthawiyo na matalala anali ambili kuposa amene anaphedwa na ana a Isiraeli.—Yos. 10:3-7, 11.

w04 12/1 11 ¶1

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa

10:13—Kodi zodabwitsa zotelezi zinatheka motani? “Kodi pali cosatheka ndi Yehova,” yemwe ali Mlengi wa kumwamba na dziko lapansi? (Genesis 18:14) Atafuna, Yehova angathe kusintha kayendedwe ka dzikoli moti munthu amene ali padziko pano angaone ngati kuti dzuŵa na mwezi sizikuyenda. Kapenanso angathe kucititsa kuti dziko na mwezi zisasunthe kenako n’kucititsa kuti kuwala kwa dzuŵa ndiponso mwezi kusasiye kuoneka padziko pano. Zilibe kanthu kuti anacita bwanji zimenezi koma mfundo ni yakuti, sipanakhaleko “tsiku lina lofanana ndi limenelo” m’mbili yonse ya anthu.—Yoswa 10:14.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w09 3/15 32 ¶5

Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga

N’zoona kuti mabuku ena anachulidwa m’Baibo komanso kuti mfundo zake zina anazigwilitsa nchito, koma zimenezi zisatipangitse kuganiza kuti mabuku onsewo anali ouzilidwa. Komabe, Yehova Mulungu wasunga zolemba zonse zomwe zili na “mawu a Mulungu wathu,” ndipo zolemba zimenezi ‘zidzakhala mpaka kalekale.’ (Yes. 40:8) Zoonadi, zimene Yehova anasankha kuti zikhale m’mabuku 66 a m’Baibo imene tili nayo, ni zokhazo zimene timafunikila kuti tikhale “okonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.”—2 Tim. 3:16, 17.

OCTOBER 18-24

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 12-14

“Tsatilani Yehova na Mtima Wonse”

w04 12/1 12 ¶2

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa

14:10-13. Ngakhale kuti ali na zaka 85, Kalebe akupempha kuti apatsidwe nchito yovuta yothamangitsa anthu m’cigawo ca Heburoni. M’delali mukukhala Aanaki, amene ni anthu a matupi aakulu kwambili. Mothandizidwa na Yehova, munthu wodziŵa nkhondoyu akugonjetsa adaniwa, ndipo mzinda wa Heburoni ukusanduka mudzi wopulumukilako. (Yoswa 15:13-19; 21:11-13) Citsanzo ca Kalebe cimatilimbikitsa kuti tisamazembe nchito zovuta zokhudza kutumikila Mulungu.

w06 10/1 18 ¶11

Kulimba Mtima Cifukwa ca Cikhulupililo na Kuopa Mulungu

11Cikhulupililo cotelo sicimangokhala malo amodzi. Cimakula tikamagwilitsa nchito coonadi m’moyo wathu, ‘tikamalawa’ ubwino wake, ‘tikamaona’ mapemphelo athu akuyankhidwa ndiponso tikamazindikila m’njila zina kuti Yehova ni amene akutitsogolela. (Salmo 34:8; 1 Yohane 5:14, 15) Sitingakayikile kuti cikhulupililo ca Yoswa na Kalebe cinakula atalaŵa ubwino wa Mulungu. (Yoswa 23:14) Taganizilani mfundo izi: Iwo anapulumuka ulendo wa zaka 40 m’cipululu, monga momwe Mulungu ananenela kuti adzatelo. (Numeri 14:27-30; 32:11, 12) Iwo anacita nchito yaikulu pa zaka zisanu na cimodzi zogonjetsa Kanani. Pomaliza, anakhala moyo wathanzi ndiponso wautali, ndipo aliyense analandila ngakhale colowa cake. Yehova amapelekadi mphoto kwa anthu amene amam’tumikila mokhulupilika na molimba mtima.—Yoswa 14:6, 9-14; 19:49, 50; 24:29.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 902-903

Gebala

Yehova anaphatikizapo “dziko la Agebala” pa maiko amene Aisiraeli anayenela kulanda m’masiku a Yoswa. (Yos. 13:1-5) Anthu ena otsutsa amakamba kuti zimenezi si zoona cifukwa mzinda wa Gebala unali kutali, kumpoto kwa Isiraeli (makilomita pafupifupi 100 kumpoto kwa fuko la Dani), ndipo n’zoonekelatu kuti Aisiraeli sanaulande mzinda umenewo. Akatswili ena amakamba kuti mbali ya mpukutu imene panali mawu a Ciheberi a pa vesiyi inawonongeka. Ndipo amakhulupilila kuti kalelo pa vesiyi panali mawu akuti “dela la kufupi na dziko la Lebanoni,” kapena kuti ‘mpaka kumalile kwa dziko la Agebala.’ Komabe, tiyenelanso kukumbukila kuti malonjezo a Yehova a pa Yoswa 13:2-7 anadalila pa zocita za Aisiraeli. Conco n’kutheka kuti Aisiraeli sanalande dziko la Agebala cifukwa ca kusamvela kwawo.—Yelekezelani na Yos. 23:12, 13.

OCTOBER 25-31

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 15-17

“Tetezani Colowa Canu Camtengo Wapatali”

it-1 1083 ¶3

Heburoni

Aisiraeli popitiliza kulanda madela a kum’mwela kwa Kanani, anapha anthu okhala ku Heburoni, kuphatikizapo mfumu yawo (mwacidziŵikile mfumu imene inaloŵa m’malo Hohamu). (Yos. 10:36, 37) Ngakhale kuti motsogoleledwa na Yoswa, Aisiraeli anagonjetsa Akanani, cioneka kuti iwo sanali kuika mwamsanga asilikali olondela madela amene anagonjetsawo. Conco n’zoonekelatu kuti pamene Aisiraeli anali kumenya nkhondo ku dela lina, Aanaki anakhazikikanso ku Heburoni. Ndiye cifukwa cake patapita nthawi, Kalebe (kapena amuna a fuko la Yuda motsogoleledwa na Kalebe) anakauthilanso nkhondo mzindawo kuti aulande m’manja mwa Aanaki. (Yos. 11:21-23; 14:12-15; 15:13, 14; Ower. 1:10) Poyamba, mzinda wa Heburoni unapelekedwa kwa Kalebe wa fuko la Yuda. Koma pambuyo pake unakhala mzinda wopatulika wothaŵilako. Unalinso mzinda wa ansembe. Komabe, “malo ozungulila mzindawo [Heburoni]” na midzi yake anawapeleka kwa Kalebe kuti akhale colowa cake.—Yos. 14:13, 14; 20:7; 21:9-13

it-1 848

Nchito ya Ukapolo

N’zoonekelatu kuti m’nthawi yakale kugwilitsa anthu “nchito ya ukapolo” (m’Ciheberi, mas) kunali kofala. Nthawi zambili anthu amene agonjetsedwa pankhondo anali kuwapanga kukhala akapolo. (Deut. 20:11; Yos. 16:10; 17:13; Esitere 10:1; Yes. 31:8; Maliro 1:1) Pamene Aisiraeli anali akapolo ku Iguputo, moyang’anilidwa na akulu a Iguputo amene anali kuwagwilitsa nchito mwankhanza, anamanga mizinda yosungilamo zinthu ya Pitomu na Ramese. (Eks. 1:11-14) Kenako Aisiraeli ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, sanatsatile lamulo la Yehova lakuti athamangitse anthu onse okhala m’dziko la Kanani na kuwawononga kothelatu. M’malomwake, anayamba kuwagwilitsa nchito ya ukapolo. Izi zinagwetsela Aisiraeli mumsampha wa kulambila mafano. (Yos. 16:10; Ower. 1:28; 2:3, 11, 12) Mfumu Solomo inapitiliza kugwilitsa nchito ya ukapolo mbadwa za Akanani, kutanthauza Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi, na Ayebusi.—1 Maf. 9:20, 21..

it-1 402 ¶3

Kanani

Akanani ambili sanawonongedwa pamene dziko lawo linagonjetsedwa ndipo sanafune kugonjela Aisiraeli. Ngakhale zinali conco, tingakambebe kuti “Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbila kuti adzapatsa makolo awo.” Anawapatsa “mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulila,” komanso kuti “palibe lonjezo ngakhale limodzi limene silinakwanilitsidwe pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli; onse anakwanilitsidwa.” (Yos. 21:43-45) Adani onse a Isiraeli anali na mantha, ndipo sakanathanso kulimbana nawo. Mulungu anali atakambilatu kuti adzathamangitsa Akananiwo “pang’ono-pang’ono” kuti dzikolo lingakhale bwinja mwamsanga na kuti zilombo zakuchile zingaculuke. (Eks. 23:29, 30; Deut. 7:22) Akanani anali na zida zapamwamba zomenyela zankhondo, monga magaleta ankhondo okhala na zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo. Ngakhale n’conco, kulephela kwa Aisiraeli kulanda madela ena sikunali cifukwa cakuti Yehova analephela kukwanilitsa lonjezo lake. (Yos. 17:16-18; Ower. 4:13) M’malomwake, Baibo imaonetsa kuti nthawi zocepa zimene Aisiraeli anagonjetsedwa cinali cifukwa ca kusamvela kwawo.—Num. 14:44, 45; Yos. 7:1-12.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w15 7/15 32

Kodi Mudziŵa?

Kodi ku Isiraeli wakale kunali nkhalango monga mmene Baibo imanenela?

BAIBO imafotokoza kuti madela ena a Dziko Lolonjezedwa anali na nkhalango zoŵilila. (1 Maf. 10:27; Yos. 17:15, 18) Anthu ena akamaona malo aakulu amene alibe mitengo masiku ano, amakayikila ngati kunalidi nkhalango.

Buku lina limati: “Kale ku Isiraeli kunali nkhalango zikulu-zikulu kusiyana ndi masiku ano.” (Life in Biblical Israel) Nkhalango zimenezi zinali na mitengo ikulu-ikulu ya paini, oki na telebeti. Mitengo ya mkuyu inali kupezekanso m’cigawo ca Sefela, malo amene anali pakati pa mapili na nyanja ya Mediterranean.

Buku linanso limakamba kuti madela ena ku Isiraeli kulibiletu mitengo masiku ano. N’cifukwa ciani? Bukuli limafotokoza kuti zimenezi zakhala zikucitika mwapang’ono-pang’ono. Limati: “Anthu akhala akudula mitengo maka-maka kuti alambule malo olimapo na odyetsela ziŵeto, komanso kuti apezeko zomangila na nkhuni.”—Plants of the Bible.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani