LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lffi phunzilo 1
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
  • Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUMBANI MOZAMILAPO
  • CIDULE CAKE
  • FUFUZANI
  • Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
  • Zimene Mungacite Kuti Muzipindula Kwambili Poŵelenga Baibo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • N’ciyani Cingakuthandizeni Kuti Musaleke Kuphunzila Baibo?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Baibo Imatilonjeza Moyo Wacimwemwe Kutsogolo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Oyambilapo
lffi phunzilo 1
Phunzilo 1. Baibo yotsegula.

PHUNZILO 01

Kodi Baibo Ingakuthandizeni Bwanji pa Umoyo Wanu?

Yopulinta
Yopulinta
Yopulinta

Tonse timafuna kudziŵa mayankho pa mafunso okhudza moyo, mavuto, imfa, komanso za kutsogolo. Timakhalanso na nkhawa zina, monga mmene tingapezele ndalama kapena cimwemwe m’banja. Anthu ambili apeza kuti Baibo yawathandiza kupeza mayankho pa mafunso ofunika mu umoyo, komanso yawapatsa nzelu zothandiza kwambili. Ndithudi, Baibo ingathandize munthu aliyense.

1. Kodi ni mafunso ena ati amene Baibo imayankha?

Baibo imayankha mafunso ofunika kwambili aya: Kodi moyo unayamba bwanji? Nanga colinga ca moyo n’ciani? N’cifukwa ciani anthu osalakwa nawonso amavutika? Kodi munthu akamwalila amayenda kuti? Popeza tonse mtendele timaufuna, n’cifukwa ciani padziko pakucitika nkhondo zambili conco? Kodi n’ciani cidzacitike padziko lapansi kutsogolo? Baibo imatilimbikitsa kufufuza mayankho a mafunso amenewa. Ndipo pali anthu mamiliyoni amene apeza mayankho okhutilitsa kwambili.

2. Kodi Baibo ingatithandize bwanji kukondwela na umoyo wathu?

Baibo imatipatsa malangizo anzelu. Mwacitsanzo, imaphunzitsa mabanja mmene angapezele cimwemwe ceni-ceni. Imatiuzanso zocita tikakhala na nkhawa, komanso mmene tingakondwelele na nchito yathu. Mudzadziŵa zimene Baibo imaphunzitsa pa nkhani zimenezi, komanso zina zambili pamene tikambitsilana za m’buku lino. Inunso mudzavomeleza kuti “malemba onse [zonse zolembedwa m’Baibo] ndi . . . opindulitsa.”—2 Timoteyo 3:16.

Buku lino silitenga malo a Baibo. Koma lidzakulimbikitsani kuti muziiŵelenga Baibo kuti muimvetsetse. Conco, muziŵelenga malemba amene aikidwa m’maphunzilo ano, ndiponso onani mmene akugwilizanila na zimene mukuphunzila.

KUMBANI MOZAMILAPO

Ganizilani mmene Baibo yathandizila anthu, mmene mungasangalalile poiŵelenga, komanso cifukwa cake kuli kofunika kuti wina akuthandizeni kuimvetsetsa.

3. Baibo ingatitsogolele njila

Baibo ili monga toci yowala bwino. Ingatithandize kupanga zisankho zanzelu, na kudziŵilatu zimene zidzacitika kutsogolo.

Ŵelengani Salimo 119:105, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi mlembi wa salimo ili anali kuiona bwanji Baibo?

  • Nanga imwe mumaiona bwanji Baibo?

Munthu akuyenda m’njila ya miyala mbali mwa nyanja kamdima katayamba, ndipo akuunika m’njila yake na toci yowala bwino.

4. Baibo ikhoza kuyankha mafunso athu

Mzimayi wina anakamba kuti Baibo inayankha mafunso amene anam’vutitsa maganizo kwa zaka zambili. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

VIDIYO: Musataye Mtima! (1:48)

  • Mu vidiyo iyi, kodi mzimayi uja anali na mafunso otani?

  • Kodi kuphunzila Baibo kunam’thandiza bwanji?

Baibo imatilimbikitsa kufunsa mafunso. Ŵelengani Mateyu 7:7, na kukambilana funso ili:

  • Kodi muli na mafunso abwanji amene mungakonde kupeza mayankho ake m’Baibo?

5. Kuŵelenga Baibo kungakukondweletseni

Anthu ambili amakondwela kuŵelenga Baibo, ndipo kumaapindulila. Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso aya.

VIDIYO: Kuŵelenga Baibo (2:05)

  • Mu vidiyo iyi, kodi acinyamatawo nkhani ya kuŵelenga anali kuiona bwanji?

  • Nanga n’cifukwa ciani kuŵelenga Baibo lomba amakuona mosiyana?

Baibo imanena kuti ingatipatse malangizo otitonthoza, imatipatsanso ciyembezo. Ŵelengani Aroma 15:4, na kukambilana funso ili:

  • Pamene Baibo imalonjeza za citonthozo na kupeleka ciyembekezo, kodi zimakukopani mtima?

6. Ena angatithandize kuimvetsetsa Baibo

Kuwonjezela pa kuŵelenga Baibo paokha, ambili apeza kuti nizothandizanso kuikambilana na munthu wina. Ŵelengani Machitidwe 8:26-31, na kukambilana funso ili:

  • Kodi n’ciani cingatithandize kuimvetsetsa Baibo?​—Onani mavesi 30 na 31.

Zithunzi: 1. Mlaliki Filipo akufotokoza malemba kwa mwamuna wa ku Itiyopiya. 2. Mboni ya Yehova ikambilana Baibo na mayi pamodzi na ana ake aŵili.

Mwamuna wa ku Itiyopiya anafunikila thandizo kuti amvetsetse malemba. Anthu ambili masiku ano apeza kuti n’zothandiza kukambitsilana Baibo na munthu wina

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Kuphunzila Baibo n’kutaya nthawi cabe.”

  • Nanga imwe mukuti bwanji? Cifukwa ciani?

CIDULE CAKE

Baibo imatipatsa malangizo othandiza pa umoyo, imayankha mafunso ofunika kwambili, ndiponso imapeleka citonthozo na ciyembekezo.

Mafunso Obweleza

  • Kodi m’Baibo tingapezemo malangizo otani othandiza?

  • Nanga ni mafunso ena ati amene Baibo imayankha?

  • N’ciani cimene mungakonde kuphunzila m’Baibo?

Zocita

FUFUZANI

Ganizilani mmene malangizo a m’Baibo alili othandiza masiku ano.

“Ziphunzitso za m’Baibo N’zothandiza Nthawi Zonse” (Nsanja ya Mlonda Na. 1 2018)

Onani mmene Baibo inathandizila munthu amene anali na mtima wapacala kuyambila ali wamng’ono.

Mmene N’nayambila Moyo Wanga Watsopano (2:53)

Onani malangizo othandiza pa umoyo wa banja.

“Zinsinsi 12 za Mabanja Acimwemwe” (Galamuka! Na. 2 2018)

Onani mmene Baibo imaunikila bwino za amene akulamulila dziko lapansi, zimene anthu ambili sadziŵa.

N’cifukwa Ciani Muyenela Kuphunzila Baibulo? —Vidiyo Yonse (3:14)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani