LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwbr21 November
  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki
  • Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2021
  • Tumitu
  • NOVEMBER 1-7
  • NOVEMBER 8-14
  • NOVEMBER 15-21
  • NOVEMBER 22-28
  • NOVEMBER 29–DECEMBER 5
  • DECEMBER 6-12
  • DECEMBER 13-19
  • DECEMBER 20-26
  • DECEMBER 27–JANUARY 2
Malifalensi a kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu—2021
mwbr21 November

Malifalensi a Kabuku ka Umoyo na Utumiki

NOVEMBER 1-7

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 18-19

“Yehova Analigaŵa Mwanzelu Dziko la Kanani”

it-1 359 ¶1

Malile

Cioneka kuti kagaŵidwe ka malo pakati pa mafuko a Isiraeli kanadalila pa zinthu ziŵili izi: zotsatilapo za maele komanso kukula kwa fuko. Maele ayenela kuti anali kungothandiza kudziŵa cigawo ca Dziko Lolonjezedwa cimene fuko lidzalandilako coloŵa cake ca malo, kaya Kumpoto kapena Kum’mwela, Kum’maŵa kapena Kum’madzulo, kumbali kwa nyanja kapena kudela la mapili. Popeza kuti zotsatilapo za maelewo zinali kucokela kwa Yehova, zinathandiza kuti mafukowo asamacitilane nsanje kapena kulimbilana malo. (Miy. 16:33) Komanso kupitila m’maele amenewo, Mulungu anayendetsa zinthu m’njila yakuti fuko lililonse lilandile coloŵa mogwilizana na ulosi wouzilidwa wolembedwa pa Genesis 49:1-33 umene Yakobo anakamba pa nthawi ya kufa kwake.

it-1 1200 ¶1

Colowa

Malo a colowa. Yehova ndiye anapatsa ana a Isiraeli colowa ca malo, ndipo anauza Mose malile a malowo. (Num. 34:1-12; Yos. 1:4) Ana a Gadi, ana a Rubeni, na hafu ya fuko la Manase anapatsidwa na Mose colowa cawo ca malo. (Num. 32:33; Yos. 14:3) Yoswa na Eleazara ndiwo anapatsa mafuko otsalawo colowa cawo ca malo mwa kucita maele. (Yos. 14:1, 2) Mogwilizana na ulosi wa Yakobo wa pa Genesis 49:5, 7, mafuko a Simiyoni na Levi sanapatsidwe gawo lapadela la malo monga colowa cawo. A fuko la Simiyoni anapatsidwa malo (komanso mizinda ina) m’cigawo ca fuko la Yuda (Yos. 19:1-9). Ndipo a fuko la Levi anapatsidwa mizinda 48 ya m’madela osiyana-siyana a dziko la Isiraeli. Popeza Alevi anasankhidwa kuti azicita utumiki wapadela pa malo opatulika, Malemba amati Yehova ndiye anali colowa cawo. Iwo anali kulandila cakhumi monga gawo lawo kapena kuti colowa cawo cifukwa ca utumiki umene anali kucita. (Num. 18:20, 21; 35:6, 7) Mabanja anali kupatsidwa malo m’cigawo ca fuko lawo. Pamene mabanja anali kuculuka, ana n’kumatenga malo a makolo awo monga colowa, m’kupita kwa nthawi malowo anayamba kugaŵidwa n’kukhala zigawo zing’ono-zing’ono.

it-1 359 ¶2

Malile

Pambuyo pakuti maele aonetsa kumene fuko lidzalandila colowa cake ca malo, panafunika kudziŵa ukulu wa malowo potengela kukula kwa fukolo. Mulungu anati: “Mukagaŵile dzikolo kwa mabanja anu monga coloŵa canu mwa kucita maele. Banja la anthu ambili mukaliwonjezele colowa cawo, ndipo banja la anthu ocepa mukalicepetsele colowa cawo. Malo alionse amene maele akagwele banja, akapatsidwe kwa banjalo.” (Num. 33:54) Conco akacita maele, dela kumene fuko lapatsidwa malo monga coloŵa silinali kusintha, koma nthawi zina cimene cinali kusintha ni kukula kwa malowo. Ndiye cifukwa cake ataona kuti malo a fuko la Yuda akula kwambili, anawacepetsako mwa kupeleka mbali ina ya malowo ku fuko la Simiyoni.—Yos. 19:9.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 359 ¶5

Malile

Nkhani yokamba za kugaŵana dela la kum’madzulo kwa Mtsinje wa Yorodano imaonetsa kuti coyamba a fuko la Yuda (Yos. 15:1-63), la Yosefe (Efuraimu) (Yos. 16:1-10), na hafu ya fuko la Manase, amene anakhala kum’madzulo kwa Mtsinje wa Yorodano (Yos. 17:1-13) anapatsidwa malo awo, anauzidwa malile a malowo, ndipo mizinda yawo inaŵelengedwa. Cioneka kuti pambuyo pake, nchito yogaŵa malo inaima cifukwa Malemba amaonetsa kuti Aisiraeli anacoka ku Giligala n’kukakhala ku Silo. (Yos. 14:6; 18:1) Baibo siifotokoza kutalika kwa nthawi imene inapitapo. Koma patapita nthawi, Yoswa anadzudzula mafuko otsalawo a Isiraeli cifukwa cozengeleza kukakhala m’madela otsala a dzikolo. (Yos. 18:2, 3) Pali zifukwa zosiyana-siyana zimene anthu amakamba kuti zinacititsa mafuko 7 otsalawo kuzengeleza kucita zimenezo. Ena amakamba kuti anazengeleza kulanda malo otsalawo cifukwa cakuti anatenga zofunkha zambili kwa Akanani amene anawagonjetsa, komanso anali kuona kuti panalibe Akanani amene anali kupeleka ciopsezo kwa iwo panthawiyo. N’kuthekanso kuti anazengeleza cifukwa coopa tumagulu twina twa adani ovuta. (Yos. 13:1-7) Komanso n’kutheka kuti cigawo cimeneci ca Dziko Lolonjezedwa sanali kucidziŵa bwino kwenikweni poyelekezela na madela amene anali atagaŵilidwa kale.

NOVEMBER 8-14

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 20-22

“Zimene Tingaphunzile pa Kusamvana Kumene Kunacitika”

w06 4/15 5 ¶3

Cinsinsi Colankhulana Bwino na Mwamuna Kapena Mkazi Wanu

Ngati tilankhulana momasuka tingapewe kusamvetsetsana na kuganizilana molakwa. Kale mu Isiraeli, mafuko a Rubeni, Gadi, na hafu ya fuko la Manase amene anali kukhala kum’maŵa kwa mtsinje wa Yorodano anamanga ‘guwa lalikulu zedi,’ pafupi na mtsinje wa Yorodano. Mafuko enawo sanamvetsetse cimene anzawo anamangila guwa la nsembelo. Poganiza kuti abale awo tsidya lina la Yorodano apanduka, mafuko amene anali kukhala kumadzulo kwa mtsinjewo anakonza zoti akamenye nawo nkhondo anthu amene anali kuwaganizila kuti agalukilawo. Koma asananyamuke kupita kunkhondo kuja, anatuma nthumwi kuti zikalankhule na mafuko a kum’maŵa aja. Imeneyi inali nzelu yaikulu. Anapeza kuti guwa la nsembe lija silinali lopselezela nsembe zosaloledwa na Mulungu ayi. Koma kuti mafuko a kum’maŵa amenewo anali kuopa kuti patsogolo, mafuko enawo angadzanene kuti “Inu mulibe gawo mwa Yehova.” Guwa la nsembelo linali kudzakhala umboni woti iwonso anali kulambila Yehova. (Yoswa 22:10-29) Ndipo iwo anacha guwa la nsembelo kuti Mboni, mwina cifukwa linali umboni woti kwa iwo, Yehova ndiye anali Mulungu woona.—Yoswa 22:34.

w08 11/15 18 ¶5

“Titsatile Zinthu Zodzetsa Mtendele”

N’kutheka kuti iwo anaona kuti panali umboni wokwanila woti anzawowo akucita zolakwa. Motelo anakonza zoti akawagonjetse mowadzidzimutsa kuti adaniwo asakakule mphamvu n’kuwaphela asilikali ambili. Koma mafuko a kumadzulo kwa Yorodano sanacite zinthu mopupuluma, m’malomwake anatumiza nthumwi kuti zikakambilane kaye nkhaniyi na abale awowo. Iwo anafunsa kuti: “‘N’cifukwa ciani mwacita zosakhulupilika kulakwila Mulungu wa Isiraeli? N’cifukwa ciani lelo mwatembenuka n’kusiya kutsatila Yehova?” Koma mafuko amene anamanga guwalo sanali kuligwilitsa nchito pa kulambila mafano. Koma kodi iwo anayankha bwanji poimbidwa mlandu umenewu, womwe sunali woona n’komwe? Kodi anapsa mtima n’kuwakalipila kwambili anzawowo kapena kodi anakana kulankhula nawo? Ayi, sanatelo. M’malomwake mafukowo anayankha modekha, n’kufotokoza bwino-bwino kuti anacita zimenezo na colinga cotumikila Yehova. Mayankhidwe awowo anathandiza kuti asakhumudwitse Yehova komanso kuti pasafe munthu. Cifukwa cokambilana mitima ili m’malo, nkhaniyo anaithetsa mwamtendele.—Yos. 22:13-34.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 402 ¶3

Kanani

Akanani ambili sanawonongedwe pamene dziko lawo linagonjetsedwa ndipo sanafune kugonjela Aisiraeli. Ngakhale zinali conco, tingakambebe kuti “Yehova anapatsa Aisiraeli dziko lonse limene analumbila kuti adzapatsa makolo awo.” Anawapatsa “mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulila,” komanso kuti “palibe lonjezo ngakhale limodzi limene silinakwanilitsidwe pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli; onse anakwanilitsidwa.” (Yos. 21:43-45) Adani onse a Isiraeli anali na mantha, ndipo sakanathanso kulimbana nawo. Mulungu anali atakambilatu kuti adzathamangitsa Akananiwo “pang’onopang’ono” kuti dzikolo lingakhale bwinja mwamsanga na kuti zilombo zakuchile zingaculuke. (Eks. 23:29, 30; Deut. 7:22) Akanani anali na zida zapamwamba zomenyela nkhondo, monga magaleta ankhondo okhala na zitsulo zazitali zakuthwa za m’mawilo. Ngakhale n’conco, kulephela kwa Aisiraeli kulanda madela ena sikunali cifukwa cakuti Yehova analephela kukwanilitsa lonjezo lake. (Yos. 17: 16-18; Ower. 4:13) M’malomwake, Baibo imaonetsa kuti nthawi zocepa zimene Aisiraeli anagonjetsedwa cinali cifukwa ca kusamvela kwawo.—Num. 14:44, 45; Yos. 7:1-12.

NOVEMBER 15-21

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YOSWA 23-24

“Malangizo Othela a Yoswa kwa Aisiraeli”

it-1 75

Mgwilizano

Zinthu zinali zosiyana kwambili pamene mtundu wa Isiraeli unaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa la Kanani. Mulungu, amene ni Wolamulila Wamkulu Koposa anapatsa Aisiraeli dziko la Kanani kuti likhale lawo, pokwanilitsa lonjezo lake kwa makolo awo. Conco iwo sanali kulowa m’dzikolo monga alendo, ndipo Yehova anawaletsa kupanga mgwilizano na mitundu yacikunja ya m’dzikolo. (Eks. 23:31-33; 34:11-16) Aisiraeli anayenela kumvela cabe malamulo a Mulungu na zigamulo zake, osati malamulo a mitundu imeneyo, imene inali pafupi kuthamangitsidwa. (Lev. 18:3, 4; 20:22-24) Anacenjezedwa mwamphamvu kuti sanayenele kucita mgwilizano wa cikwati na anthu a mitundu imeneyo. Kucita zimenezo kukanapangitsa kuti apange ubale na akazi acikunjawo komanso acibululu awo. Kukanapangitsanso kuti ayambe kucita nawo miyambo na zinthu zina za cipembedzo conama. Zotulukapo zake, Aisiraeli akanapandukila Yehova, ndipo uwu ukanakhala msampha kwa iwo.—Deut. 7:2-4; Eks. 34:16; Yos. 23:12, 13.

w07 11/1 26 ¶19-20

Mawu a Yehova Amakwanilitsidwa Nthawi Zonse

19Apatu, malinga na zimene taona, tinganene kuti: “Pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwanilitsidwe. Onse akwanilitsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwanilitsidwe.” (Yoswa 23:14) Yehova amapulumutsa, kuteteza ndiponso kusamalila atumiki ake. Kodi mungathe kunena lonjezo lina lililonse limene iye sanakwanilitse pa nthawi yake? Simungathe kutelo. Conco, ni bwino kukhulupilila Mawu a Mulungu omwe ni odalilika.

20Nanga bwanji za m’tsogolo? Yehova watilonjeza kuti ambilife tidzakhala m’dziko lapansi, litakonzedwa bwino kukhala paradaiso wokongola. Anthu ocepa cabe akuyembekezela kukalamulila limodzi na Khristu kumwamba. Kaya tikuyembekezela kudzakhala padziko lapansi, kaya kupita kumwamba, tili na zifukwa zomveka zokhalila okhulupilika ngati Yoswa. Nthawi ina, zonse zimene tikuyembekezela zidzakwanilitsidwa. Ndiyeno tikadzakumbukila zonse zimene Yehova anatilonjeza, nafenso tidzatha kunena kuti: “Onse akwanilitsidwa.”

Kufufuza Cuma Cauzimu

w04 12/1 11 ¶10

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yoswa

24:2—Kodi Tera, yemwe anali atate wake wa Abulahamu anali kulambila mafano? Poyamba, Tera sanali kulambila Yehova Mulungu. N’kutheka kuti anali kulambila Sin, yemwe anali mulungu wochuka wamwezi ku Uri. Malinga na zimene Ayuda amakhulupilila, n’kuthekanso kuti Tera anali munthu wopanga mafano. Koma Abulahamu atacoka ku Uri pomvela lamulo la Mulungu, Tera anapita naye limodzi ku Harana.—Genesis 11:31.

NOVEMBER 22-28

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 1-3

“Nkhani Yocititsa Cidwi Yoonetsa Kulimba Mtima”

w04 3/15 31 ¶3

Ehudi Anathyola Goli la Wopondeleza

Zomwe Ehudi anakonza kuti acite zinayenda bwino, osati cifukwa ca kucenjela kwake kapena cifukwa cakuti adani awo anali olephela penapake. Kukwanilitsidwa kwa colinga ca Mulungu sikudalila zocita za anthu. Cinthu cacikulu cimene cinacititsa kuti zinthu zimuyendele bwino Ehudi n’cakuti, Mulungu anali kum’thandiza pamene iye anali kucita zinthu mogwilizana na colinga ca Mulungu copulumutsa anthu Ake cimene sicikanalepheletsedwa. Mulungu anautsa Ehudi, ndipo “Yehova akawapatsa oweluza [anthu ake], Yehova anali kukhaladi ndi aliyense wa oweluzawo.”—Oweruza 2:18; 3:15.

w04 3/15 30 ¶1-3

Ehudi Anathyola Goli la Wopondeleza

Cinthu coyamba cimene Ehudi anacita cinali “kudzipangila lupanga,” limene linali lakuthwa konse-konse ndiponso lalifupi bwino moti akanatha kulibisa m’zovala zake. N’kutheka kuti anali kuyembekezela kukasecedwa. Kaŵili-kaŵili malupanga anali kuwamangilila mbali ya kumanzele, komwe anthu ogwilitsa nchito dzanja lamanja sanali kuvutika kulisolola. Popeza kuti Ehudi anali wamanzele, iye anabisa cida cakeci “pansi pa zovala zake pa nchafu ya kulamanja,” komwe zinali zokayikitsa kuti alonda a mfumu angaseceko. Motelo, iye anapita ‘kukapeleka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Moabu’ popanda vuto lililonse.—Oweruza 3:16, 17.

Sitikuuzidwa tsatane-tsatane wa zimene zinacitika koyambilila m’nyumba ya Egiloni. Baibo imangonena kuti: “Ehudi atapeleka msonkhowo, anauza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita.” (Oweruza 3:18) Ehudi anapeleka msonkho, na kupelekeza anthu onyamula msonkhowo kucoka panyumba ya Egiloni mpaka pamalo oti sangacitidwe coopsa, ndipo iye anabwelela atawauza anthuwo kuti azipita. N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Mwina anawatenga n’colinga coti azimuteteza, kapena mwamwambo cabe, kapenanso monga anthu ongonyamula msonkho basi. Ndipo mwina Ehudi anali kufuna kuti anthuwo ayambe acoka kaye n’colinga cakuti iye akamacita zimene anali atakonza, iwo asavulazidwe. Kaya maganizo a Ehudi anali otani pamenepa, koma iye anabwelela yekha molimba mtima kunyumba ya Egiloni.

“Atafika pamiyala yogoba imene inali ku Giligala, [Ehudi] anabwelela kwa mfumu na kuiuza kuti: “Pepanitu mfumu, ndili ndi uthenga wacinsinsi woti ndikuuzeni.’” Malemba safotokoza kuti zinatheka bwanji kuti amulolenso kukaonana na Egiloni. N’kutheka kuti alonda sanam’kayikile. Mwina alondawo anali kuganiza kuti Mwisiraeli mmodzi sangacite coopsa ciliconse kwa mbuye wawo. N’kuthekanso kuti kubwelanso yekha kwa Ehudi kunawapatsa maganizo oti akuwapita pansi anthu a m’dziko lake. Mulimonsemo, Ehudi anafuna kuti alankhulane pa aŵili na mfumu, ndipo anamulola.—Oweruza 3:19.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 1/15 24 ¶7

Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza

2:10-12. Tiyenela kukhala na cizoloŵezi cophunzila Baibo nthawi zonse kuti ‘tisaiŵale zocita za Yehova.’ (Salimo 103:2) Makolo ayenela kukhomeleza coonadi ca Mawu a Mulungu m’mitima ya ana awo.—Deuteronomo 6:6-9.

NOVEMBER 29–DECEMBER 5

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 4-5

“Yehova Anaseŵenzetsa Akazi Aŵili Populumutsa Anthu Ake”

w15 9/1 12-13

“Ine Ndinauka Monga Mayi mu Isiraeli”

Ku Isiraeli, anthu akamva dzina lakuti Sisera anali kucita mantha kwambili. Cipembedzo na cikhalidwe ca Akanani cinali cankhanza, anali kupeleka ana nsembe ndipo anali kucita ciwelewele pakacisi. Nanga zinthu zinali bwanji pamene Sisera na asilikali ake anali kulamulila dziko? Nyimbo ya Debora imafotokoza kuti kuyenda m’njila kunali kovuta ndipo panalibe aliyense amene anali kukhala m’midzi. (Oweruza 5:6, 7) Anthu anali kubisala m’nkhalango na m’mapili. Iwo sanali kulima ndipo anacita mantha kukhala m’midzi yopanda citetezo ndiponso sanali kuyenda pamsewu kuopa kuti ana awo angatengedwe ndipo akazi awo angagwililidwe.

w15 9/1 13 ¶1

“Ine Ndinauka Monga Mayi mu Isiraeli”

Anapitiliza kukhala mwamantha kwa zaka 20 kufikila pamene Yehova anaona kuti anthu ake ouma khosi anali kufuna kusintha. Nyimbo youzilidwa ya Debora na Baraki imati: “Kufikila pamene ine Debora ndinauka, kufikila pamene ine ndinauka monga mayi mu Isiraeli.” Sitikudziŵa ngati Debora mkazi wa Lapidoti anali na ana, koma cimene tikudziŵa n’cakuti mawu amenewa ni ophiphilitsa. Yehova anapatsa udindo Debora woteteza mtunduwo monga mmene mayi amatetezela mwana wake. Yehova anacititsa Debora kulimbikitsa na kutsogolela Woweluza Baraki, munthu wa cikhulupililo, kukamenyana na Sisera.—Oweruza 4:3, 6, 7; 5:7.

w15 9/1 15 ¶1

“Ine Ndinauka Monga Mayi mu Isiraeli”

Coyamba, Yaeli anafunika kuganiza cocita mwamsanga. Iye anapatsa Sisera malo kuti apumule. Sisera analamula mkaziyo kuti kukabwela munthu aliyense womufunafuna, asamuulule. Yaeli anam’funditsa bulangete ndipo atam’pempha madzi akumwa, anam’patsa mkaka. Atamwa mkakawo, Sisera anagona tulo tofa nato. Zitatelo, Yaeli anatenga cikhomo na nsando zimene akazi okhala m’mahema anali kudziŵa kuziseŵenzetsa mwaluso. Pokhala wakupha woikidwa na Yehova, Yaeli anayenda mwakacetecete kufika pamene panali mutu wa Sisera. Iye akanacedwa pang’ono kapena kukayikila zinthu zikanaipilatu. Kodi anakumbukila mmene munthu ameneyu anavutitsila anthu a Mulungu kwa zaka zambili? Kapena kodi anaganizila za mwayi umene anali nawo wokhala kumbali ya Yehova? Baibo siikamba ciliconse. Koma cimene tikudziŵa n’cakuti Yaeli anacitapo kanthu mwamsanga, ndipo Sisera anaphedwa.—Oweruza 4:18-21; 5:24-27.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 1/15 25 ¶5

Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza

5:20—Kodi nyenyezi zinamenya nkhondo motani kucokela kumwamba pothandiza Baraki? Baibo siinena ngati zimenezi zikutanthauza thandizo la angelo, kugwa kwa miyala yocokela kumwamba imene anzelu a Sisera anati inali kulosela tsoka, kapena ngati zikutanthauza ulosi wabodza umene okhulupilila nyenyezi anauza Sisera. Koma n’zosakayikitsa kuti Mulungu anacitapo kanthu.

DECEMBER 6-12

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 6-7

“Pita ndi Mphamvu Zimene Ndakupatsazi”

w02 2/15 6-7

Mfundo za Cikhalidwe za Mulungu Zingakupindulitseni

Munthu wina yemwe anali kudziona moyenela ndiponso yemwe anali kudzipatsa ulemu woyenelela anali Gidiyoni, woweluza wa Aheberi akale. Iye sanacite kufuna kuti akhale mtsogoleli wa Isiraeli. Komabe, atasankhidwa kuti akhale paudindowu, Gidiyoni anadziona wopeleŵela. Iye anati: “Banja lathu ndilo laling’ono zedi m’fuko lonse la Manase, ndipo m’nyumba ya bambo anga, wamng’ono kwambili ndine.”—Oweruza 6:12-16.

w05 7/15 16 ¶3

“Lupanga la Yehova ndi la Gidiyoni”

Mwadzidzidzi, Amidiyani anagwidwa na mantha kwambili na zimene zinacitika. Bata lawo linasokonezeka na ciphokoso ca kuphwanyidwa kwa mbiya 300, kulila kwa malipenga 300, na kufuula kwa anthu 300. Podabwa, makamaka na mfuu yakuti “Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!,” Amidiyani anawonjezela phokosolo pamene nawonso anayamba kufuula. M’cipwilikitico, sakanatha kusiyanitsa mnzawo na mdani. Asilikali 300 aja anangoimabe m’malo awo pamene Mulungu anacititsa adaniwo kusolola malupanga awo na kuyamba kuphana okha-okha. Msasawo unagonjetsedwa, panalibe zopulumuka, omwe anali kuthaŵa anawapitikitsa mpaka kutali kwambili n’kuwamalizilatu onse. Ulamulilo wautali na wankhanza wa Amidiyani uja unathela pamenepa.—Oweruza 7:19-25; 8:10-12, 28.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 1/15 26 ¶6

Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza

6:25-27. Gidiyoni anali wosamala kuti asakwiyitse cisawawa anthu amene anali kutsutsana nawo. Polalikila uthenga wabwino, tiyenela kusamala kuti tisakhumudwitse ena mosayenelela cifukwa ca mmene tikulankhulila.

DECEMBER 13-19

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 8-9

“Kudzicepetsa N’kwabwino Kuposa Kunyada”

w00 8/15 25 ¶3

Kodi Mumatani Pakakhala Kusamvana?

Ali mkati mwa nkhondo yolimbana na Amidiyani, Gidiyoni anaitana fuko la Efuraimu kuti lithandize. Komabe, nkhondoyo itatha, Efuraimu anatembenukila Gidiyoni n’kumudandaulila mwaukali kuti sanawaitane paciyambi pa nkhondoyo. Nkhaniyo imati “iwo anayesetsa mwamphamvu kuti acite naye mkangano.” Poyankha, Gidiyoni anati: “Kodi ine ndacita ciani poyelekeza ndi inu? Kodi zokunkha za Efuraimu si zabwino kwambili kuposa mphesa zimene Abi-ezeri wakolola? Kodi Mulungu sanapeleke Orebi ndi Zeebi, akalonga a Midiyani m’manja mwanu? Ndipo ine ndacita ciani poyelekeza ndi inu?” (Oweruza 8:1-3) Na mawu ake osankhidwa bwino komanso odekha, Gidiyoni anapewa nkhondo yaciweniweni imene ikanakhala yowononga kwambili. Mwina vuto la fuko la Efuraimu lingakhale lakuti anali kudziona kukhala ofunika kwambili komanso kunyada. Komabe, zimenezo sizinam’letse Gidiyoni kuyesetsa kuti abwezeletse mtendele. Kodi tingacite cimodzimodzi?

w17.01 20 ¶15

N’cifukwa Ciani Kudzicepetsa N’kofunikabe?

15Gidiyoni anali citsanzo cabwino ngako ca kudzicepetsa. Pamene mngelo wa Yehova anaonekela kwa Gidiyoni, iye modzicepetsa anati sanali woyenelela udindowo pokhalanso wocokela ku banja lotsika. (Ower. 6:15) Koma pamene analandila udindowo kwa Yehova, Gidiyoni anayesetsa kuumvetsa udindo wake na kuusamalila bwino lomwe. Anadalilanso Yehova kuti amutsogolele. (Ower. 6:36-40) Ngakhale kuti Gidiyoni anali munthu wolimba mtima, anacitabe zinthu mosamala ndi mwanzelu. (Ower. 6:11, 27) Iye sanaumilile nga-nga-nga paudindo pofuna kuchuka ayi. Atangotsiliza nchito imene anapatsidwa, anali wokondwa kubwelela pamalo ake akale.—Ower. 8:22, 23, 29.

w08 2/15 9 ¶9

Yendani M’njila za Yehova

9Kuti tikhale mabwenzi a Mulungu, tiyenela kukhala na “maganizo odzicepetsa.” (1 Pet. 3:8; Sal. 138:6) Lemba la Oweruza caputala 9 limasonyeza kufunika kwa kudzicepetsa. Yotamu mwana wa Gidiyoni anati: “Kalekale mitengo inafuna kudzoza mfumu yawo.” Anachula mtengo wa maolivi, wa mkuyu ndi wa mpesa. Mitengo imeneyi inaimila anthu oyenelela amene sanafune kulamulila Aisiraeli anzawo. Koma mtengo wa minga, umene unali kugwila nchito monga nkhuni basi, unaimila ufumu wa Abimeleki wodzikuza amene anali munthu wambanda na wokonda kupondeleza ena. Ngakhale kuti iye “anakhala ngati mfumu ya Isiraeli zaka zitatu,” anafa imfa yosayembekezeleka. (Ower. 9:8-15, 22, 50-54) Conco ni bwino kukhala na “maganizo odzicepetsa.”

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-1 753 ¶1

Efodi, I

Gidiyoni anali na zolinga zabwino popanga covala ca Efodi. Anafuna kulemekeza Yehova komanso kukumbukila mmene iye anawathandizila kupambana nkhondo. Ngakhale zinali conco, Efodiyo ‘anakhala msampha kwa Gidiyoni ndi nyumba yake’, cifukwa Aisiraeli anacita cigololo cauzimu mwa kuyamba kulambila covalaco. (Ower. 8:27) Koma Baibo siikambako kuti Gidiyoni nayenso anali kucilambila covalaco. M’malomwake, Gidiyoni anachulidwa mwacindunji na mtumwi Paulo monga mmodzi wa anthu amene apanga ‘mtambo waukulu’ wa mboni zokhulupilika za Yehova zimene zinakhalapo Cikhristu cisanayambe.—Aheb. 11:32; 12:1.

DECEMBER 20-26

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 10-12

“Yefita Anali Munthu Wauzimu”

w16.04 5 ¶9

Mulungu Amakonda Anthu Okhulupilika

9Citsanzo ca Yosefe ciyenela kuti cinam’thandiza kwambili Yefita. Zioneka kuti iye anali kudziŵa mmene Yosefe anasonyezela cifundo kwa abale ake ngakhale kuti anali kumuzonda. (Gen. 37:4; 45:4, 5) Kuganizila citsanzo cimeneci kuyenela kuti kunamuthandiza kucita zinthu zokondweletsa Yehova. Zimene abale ake anam’citila zinamuŵaŵa kwambili. Koma kuteteza dzina la Yehova na anthu ake ndiye cinali cinthu cofunika kwambili kuposa mavuto amene anali kukumana nawo. (Ower. 11:9) Iye anayesetsa kukhala wokhulupilika kwa Yehova. Yehova anadalitsa Yefita na Aisiraeli cifukwa ca mmene Yefita anacitila zinthu.—Aheb. 11:32, 33.

it-2 27 ¶2

Yefita

Yefita anali munthu wosazengeleza pocita zinthu. Atangoikidwa kukhala mtsogoleli, nthawi yomweyo anayamba kuonetsa mphamvu zake monga mtsogoleli. Anatumiza uthenga kwa mfumu ya Aamoni, woiuza kuti inalakwa kuukila dziko la Isiraeli. Koma poyankha mfumuyo inakamba kuti Aisiraeli analanda dzikolo m’manja mwa Aamoni. (Ower. 11:12, 13) Zimene Yefita anayankha zinaonetsa kuti sanali msilikali wankhanza wosadziŵa zinthu. Koma kuti anali munthu wodziŵa bwino mbili yakale, maka-maka yokhudza mmene Mulungu anali kucitila zinthu na anthu ake. Iye anatsutsa zimene mfumu ya Aamoni inakamba, ndipo anaonetsa kuti (1) Aisiraeli sanavutitsa Aamoni, Amowabu, kapena Aedomu (Ower. 11:14-18; Deut. 2:9, 19, 37; 2 Mbiri 20:10, 11); (2) Aamoni sanali kukhala m’dzikolo pamene Aisiraeli analigonjetsa, cifukwa linali m’manja mwa mtundu wacikanani wa Aamori. Ndipo Mulungu anapeleka Sihoni mfumu ya Aamori, na dziko lake m’manja mwa Aisiraeli; (3) kwa zaka 300 Aamoni sanalimbane na Aisiraeli cifukwa cokhala m’dela limenelo. Conco panalibe cifukwa cakuti panthawiyi ayambe kulimbana nawo.—Ower. 11:19-27.

it-2 27 ¶3

Yefita

Tsopano Yefita anafotokoza pamene panagona nkhani. Anaonetsa kuti kwenikweni nkhaniyo inali yokhudza kulambila. Yefita anakamba kuti Yehova Mulungu ndiye anapatsa Aisiraeli dzikolo, komanso kuti pa cifukwa cimeneco sakanapeleka ngakhale gawo locepetsetsa la dzikolo kwa anthu olambila mulungu wonama. Iye anakamba kuti mulungu wa Aamoni anali Kemosi. Ena amaganiza kuti pamenepa panalakwika cifukwa Aamoni anali kulambila mulungu wochedwa Milikomu, ndipo Kemosi anali mulungu wa Amowabu. Komabe, mitundu imeneyi inali yogwilizana, ndipo inali kulambila milungu yambili. Solomo anafika ngakhale popangitsa Aisiraeli kuyamba kulambila mulungu wonama ameneyo Kemosi cifukwa ca akazi ake acikunja. (Ower. 11:24; 1 Maf. 11:1, 7, 8, 33; 2 Maf. 23:13) Kuwonjezela apo, akatswili ena amakamba kuti dzina lakuti “Kemosi” lingatanthauze “Wogonjetsa”. (Onani buku lakuti Gesenius’s Hebrew and Chaldee Lexicon, lomasulidwa na S. Tregelles, 1901, peji 401.) Conco n’kutheka kuti Yefita anachula mulungu ameneyu poonetsa kuti Aamoni anali kum’tamanda kuti ndiye anali kuwathandiza ‘kugonjetsa’ mitundu ina na kuwapatsa malo.

Kufufuza Cuma Cauzimu

it-2 26

Yefita

Yefita Sanali Mwana Wam’cigololo. Amayi ake a Yefita anali “hule”. Koma izi sizitanthauza kuti Yefita anali wobadwila m’cigololo. Amayi ake anali hule asanakwatiwe na Giliyadi monga mkazi wake waciŵili. Anali ngati Rahabi, amene poyamba anali hule, koma pambuyo pake anakwatiwa na Salimoni. (Ower. 11:1; Yos. 2:1; Mat. 1:5) Cimene citsimikizila kuti Yefita sanali wobadwila m’cigololo n’cakuti abale ake, obadwa kwa mkazi wamkulu wa Giliyadi, anamuthamangitsa panyumba kuti asalandileko colowa atate ake. (Ower. 11:2) Komanso pambuyo pake, Yefita anavomelezedwa kukhala mtsogoleli wa amuna a Giliyadi. (Pa amuna amenewo cioneka kuti abale ake a Yefita a mimba ina ndiwo anali akulu). (Ower. 11:11) Kuwonjezela apo, iye anapeleka nsembe kwa Mulungu pa cihema. (Ower. 11:30, 31) Zonsezi sizikanatheka akanakhala kuti Yefita anali mwana wam’cigololo, cifukwa Cilamulo cinakamba mosapita m’mbali kuti: “Mwana wapathengo asalowe mumpingo wa Yehova. Ana ake asalowe mumpingo wa Yehova kufikila m’badwo wa 10.”—Deut. 23:2.

DECEMBER 27–JANUARY 2

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OWERUZA 13-14

“Zimene Makolo Angaphunzile kwa Manowa na Mkazi Wake”

w13 8/15 16 ¶1

Makolo—Phunzitsani Ana Anu Kuyambila Ali Akhanda

Taganizilani za munthu wina wa fuko la Dani, dzina lake Manowa, amene anali kukhala m’tauni ya Zoari ku Isiraeli. Mngelo wa Yehova anauza mkazi wa Manowa, yemwe anali wosabeleka, kuti adzabeleka mwana wamwamuna. (Ower. 13:2, 3) Manowa na mkazi wake ayenela kuti anasangalala kwambili atamva zimenezi koma panali zina zimene zinali kuwadetsa nkhawa. Manowa anapemphela kuti: “Yehova, lolani kuti munthu wa Mulungu woona amene munam’tuma, abwelenso kuti adzatilangize zoyenela kucita ndi mwana amene adzabadweyo.” (Ower. 13:8) Manowa na mkazi wake anali kufunitsitsa kulela bwino mwanayo. Iwo ayenela kuti anaphunzitsa mwana wawo, dzina lake Samisoni, cilamulo ca Mulungu ndipo zotsatila zake zinali zabwino. Baibo imanena kuti: “Kenako mzimu wa Yehova unayamba kugwila nchito pa [Samisoni].” Izi zinacititsa kuti Samisoni acite zinthu zambili zodabwitsa pa nthawi imene anali woweluza wa Aisiraeli.—Ower. 13:25; 14:5, 6; 15:14, 15.

w05 3/15 25-26

Samisoni Anapambana Cifukwa ca Mphamvu za Yehova

Pamene Samisoni anali kukula, ‘Yehova anapitiliza kumudalitsa.’ (Oweruza 13:24) Tsiku lina Samisoni anapita kwa bambo na mayi ake na kuwauza kuti: “Ine ndaona mkazi ku Timuna mwa ana aakazi a Afilisiti, conco mukam’tenge kuti akhale mkazi wanga.” (Oweruza 14:2) Tangoganizani mmene iwo anadabwila. M’malo mopulumutsa Isiraeli m’manja mwa adani opondelezawo, mwana wawo akufuna kukwatila mkazi wamtundu umenewo. Kukwatila mkazi wolambila milungu yacikunja kunali kotsutsana na Cilamulo ca Mulungu. (Ekisodo 34:11-16) Pa cifukwa cimeneci, makolo akewo anatsutsa nati: “Kodi wasowa mkazi pakati pa ana aakazi a abale ako ndi anthu onse a mtundu wathu, kuti upite kukatenga mkazi kwa Afilisiti osadulidwa?” Koma Samisoni anaumililabe nati: “Ingonditengelani mkazi ameneyu, cifukwa ndi amene ali woyenela kwa ine.”—Oweruza 14:3.

Kufufuza Cuma Cauzimu

w05 3/15 26 ¶1

Samisoni Anapambana Cifukwa ca Mphamvu za Yehova

Kodi mkazi wacifilisiti ameneyu anali “woyenela” motani kwa Samisoni? Buku lochedwa Cyclopedia lolembedwa na McClintock na Strong limati, sikuti anali woyenela m’lingalilo lakuti anali “wokongola, wosangalatsa, kapena wokopa ayi, koma anali woyenela mogwilizana na kukwanilitsa colinga cake.” Kukwanilitsa colinga cotani? Lemba la Oweruza 14:4 limafotokoza kuti Samisoni “anali kufunafuna mpata woti amenyane ndi Afilisiti.” Samisoni anali kufuna mkaziyo kuti apezelepo mpata wolimbana na Afilisitiwo. Samisoni atakula, “mzimu wa Yehova unayamba kugwila nchito pa iye,” kapena kuti kumulimbikitsa kucitapo kanthu. (Oweruza 13:25) Cotelo mzimu woyela ni umene unalimbikitsa Samisoni kupeleka pempho lake lodabwitsali lokhudza mkazi ameneyu, komanso ni umene unali kum’tsogolela pa nchito yake yonse monga woweruza wa Isiraeli. Kodi mpata umene Samisoni anali kuufuna unapezeka? Coyamba tiyeni tione mmene Yehova anam’tsimikizila kuti adzam’thandiza.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani